Phata lenireni la upangiri wa Kulima mu Njira ya Mulungu ndi … 

Musaotche kapena kusakaniza bulangeti la Mulungu; 

Osatembenuza nthaka, chitani kasinthasintha wa mbeu 

Osaotcha….. 

Bulangeti la Mulungu liri ndi kuthekera kovumbulutsa malonjezano ochuluka a Mulungu m’munda wathu. Bulangeti limapangitsa kuti machiritso abwere ku nthaka yathu. 

Osatembenuza nthaka….. 

Mu nthawi za Baibulo, kulima kumachitika ndi chinthu chokuthwa monga nthungo, chimene sichimatembenuza nthaka, koma amangomasula nthaka kuti pakhale malo obyalapo. 

Kuchita kasinthasintha wa mbeu….. 

Kasinthasintha wa mbeu waonetsa kuti ndiwabwino pochiritsa nthaka yathu komanso ku thanzi la mbeu. 

Ubwino wa Kulima mu Njira ya Mulungu waombedwa mkota m’munsimu: 

Ubwino mu zonse 

1) Madzi amathamanga mochepa Kulima kotembenuza nthaka: maperesenti 90 a mvula amapita ku mtsinje. Kulima mu Njira ya Mulungu: maperesenti 6 okha a mvula amapita ku mtsinje. 

2) Kukokololoka kwa dothi kumachepa Kulima kotembenuza nthaka: matani 55 mpaka 250 a dothi amakokololoka pa hekitala pa chaka mu Afrika. Kulima mu Njira ya Mulungu: dothi lochepa kwambiri limene limachoka pa hekitala pa chaka.

3) Madzi amalowa munthaka mosavuta Kulima kotembenuza nthaka: Mphamvu ya madontho a mvula imene imabwera monga nyundo pa dothi imagogomeza dothi ndikupanga chikhakha chimene chimapangitsa kuti maperesenti 10 okha a mvula alowe pansi. Kulima mu Njira ya Mulungu: bulangeti la Mulungu limateteza madontho a mvula amene amabwera ngati nyundo ndipo limamwa madzi ochuluka, izi zimapangitsa kuti maperesenti 94 a mvula alowe mu nthaka. 

4) Kuuluka kwa madzi munthaka kumachepa Kulima kotembenuza nthaka: Ka 10 peresenti ka mvula kamene kamalowa munthaka kamapezeka kuti kakumana ndi kutentha kwambiri kumene kumapangitsa kuti madzi auluke munthaka. Kulima mu Njira ya Mulungu: bulangeti la Mulungu limapangitsa m’thunzi pamwamba pa dothi, zimene zimapangitsa kuti pakhale chinyezi komanso pakhale pozizira, izi zimachepetsa kuuluka kwa madzi munthaka. 

5) Dothi lozizila zimapangitsa mbeu kukula bwino Mbeu zimene zabyalidwa pa munda wa Kulima mu Njira ya Mulungu zimatenga nthawi yaitali zisanamere, koma pakangotha masabata atatu zikamera, mbeu izi zimathamanga ndikupitirira izo zimene zabyalidwa m’munda wotembenuza nthaka. Pamene nthaka yanu iri yozizira, zimathandiza kuti mizu yanu ikhazikike, apa mbeu yanu imakhala ya mphamvu komanso yathanzi. 

6) Simutaya mvula yoyambirira Kulima kotembenuza nthaka: Amadikira mvula yoyamba kenako azikalima ndi mathalakitala. Kenako amadikira mvula yabwino yachiwiri kuti abyale. Kulima mu Njira ya Mulungu: Minda imakhala yakonzedwa mvula yoyamba isanagwe. Angathe kubyala pamene mvula yoyamba yagwa pakuti madzi ochuluka samauluka ndikupita kumwamba. 

7) Kapalepale amakhala osavuta Kulima kotembenuza nthaka: Pamene mwatembenuza dothi zimalimbikitsa kuti udzu umere kwambiri. Kulima mu Njira ya Mulungu: Chifukwa dothi silitembenuzidwa komanso chifukwa cha bulangeti, zimathandiza kuti udzu usamere ochuluka. Kuika bulangeti pamwamba kwapezeka kuti ndi njira yabwino yogonjetsera udzu okwawa. 

Kupindula ku mbali yoti dothi limachita bwino 

8) Dothi limasunga madzi ochuluka Dothi limene silimatembenuzidwa limakhala ngati siponji ndipo izi zimathandiza kuti lizitha kusunga chinyezi. Izi zimapangitsanso kuti lithe kupirira mu nthawi ya ng’amba komanso zokolola zichuluke. 

9) Chonde chimakwera munthaka Pakapita zaka bulangeti la Mulungu limavunda kupyolera mutizilombo timene timagwira nchito yake mu nthaka. Izi zimapangitsa kuti zakudya za mbeu zibwerere mu nthaka zimene zimapangitsa kuti chonde chidzikwera. 

10) Kuika naitulojeni munthaka Chonde cha munthaka chimaonjezereka pamene muchita kasinthasintha wa mbeu makamaka pogwiritsa ntchito mbeu monga nyemba, soya, mtedza, ndi mbeu zina zimene zimaika nayitulojeni munthaka. Nayitulojeni uyu amadzagwiritsidwa ntchito ndi mbeu imene idzabyalidwe chaka chotsatira. 

11) Zimachepetsa kugogomezeka kwa nthaka Kulima kotembenuza nthaka: Dothi limene latembenuzidwa limakhala ndi mavuto pakapita kanthawi monga kugwa kwa zinthu zimene zimapangitsa kuti dothi likhale pamodzi. Mauna ndi ziboowo zopezeka mudothi zimatsekeka ndipo izi zimapangitsa kuti dothi ligogomezeke kwambiri, komanso pamene mukulima dothi lanu ndi mathalakitala mumapangitsa kuti dothi lizigwirana pansi chifukwa limagogomezeka kwambiri. Kulima mu Njira ya Mulungu: Chaka ndi chaka dothi limakhala likuchuluka, ndi mizu ya mbeu komanso mauna amene tizilombo tamunthaka timapanga. Izi zimapangitsa kuti mbeu imene ibyalidwe chaka chotsatiracho idzathe kulowetsa mizu yake mosavuta popanda chotchinga china chiri chonse.

12) Mpweya umayenda bwino munthaka Pamene dothi lanu liri ngati siponji chifukwa chosalima motembenuza, limathandiza kuti mpweya uzitha kulowa ndi kumayenda mu nthaka yanu popanda chovuta. Izi zimachitika chifukwa cha mauna komanso ziboowo zimene tizilombo touluka komanso tokhala munthaka timapanga. Izinso zimathandiza kuti mizu izipuma ngakhale pa malo okuti dothi ndilodzala ndi madzi kwambiri. 

13) Nyongolosi za mudothi zimasangalala Pali magulu awiri a zilombo zokhala munthaka, zimene maina ao ali awa, zopuma mpweya wabwino komanso zopuma mpweya woipa. Kulima kotembenuza nthaka: Pamene tikutembenuza nthaka, timatenga tizilombo topuma mpweya wabwino ndikuziika pa malo pokuti palibe mpweya wabwino komanso timatenga zapansi zimene zimapuma mpweya woipa ndikuziika pamwamba pamene pali mpweya wabwino ndipo izi zimapangitsa kuti zonse zife. Kulima mu Njira ya Mulungu: Pakusaotcha bulangeti komanso kusatembenuza dothi, timapanga malo oyenera, ozizira komanso a chinyezi ndipo izi zimapangitsa kuti moyo ochuluka wa munthaka udzikula. Dothi la thanzi ndi dothi limene liri ndi moyo ndi tizilombo. 

Kupindula pa chuma 

14) Kuteteza matenda ndi tizilombo toononga mbeu Mbeu zimene zikuvutikira chinyenzi komanso zakudya munthaka zimatulutsa kuwala kwa dzuwa kwambiri ndipo izi zimapangitsa kuti zikhale zokopera zilombo. Izi zimapangitsanso kuti matenda abwere. 

Kulima mu Njira ya Mulungu kumapangitsa kuti mbeu zikhale zathanzi. Komanso kumapangitsa kuti dothi lizitha kugwira ntchito yake bwino mu chirengedwe zimene zimapangitsa kuti tizilombo tina tizitha kudya zilombo zoononga mbeu. 

Kasinthasintha wa mbeu nayenso amathandiza kuononga namzungulire wa matenda ndi tizilombo toononga mbeu ndipo izi zimachepetsa mbeu zoonongeka.

15) Nthawi yokonza m'munda imachepa komanso ndalama zimachepa Kafukufuku wapeza kuti alimi akuluakulu amene amagwiritsa ntchito mathalakitala polima amaononga ndalama zochuluka katatu kuposera mlimi amene satembenuza dothi. Ndalamazi zimagwira ntchito pogula mafuta, oyilo, komanso kukonzera makina akaonongeka. 

Alimi ang’ono ang’ono amatenga masabata osachepera khumi kuti alime mizera ndikukumba mapando ao. Izi zikusiyana ndi alimi amene amalima mu Njira ya Mulungu chifukwa amatenga masabata asanu ndi limodzi kuti amalize mapando ao ndikumadikirira mvula. 

16) Kutaika kwa fetereza kumakhala kochepa Chaka ndi chaka fetereza ochuluka amathawira ku malo otsetsereka chifukwa chakukokololoka kwa dothi ndi kuthamanga kwa madzi komanso wina amalowa pansi. 

Kulima mu Njira ya Mulungu kumachepetsa kutaika kumeneku komanso kuonetsetsa kuti fetereza amene wathiridwa waikidwa pa malo oyenera amene mizu ingathe kugwiritsa ntchito mosavuta. 

17) Pamakhala kupilira ku ng'amba komanso kupewa ngozi zina Pali zinthu zitatu zimene zimathandiza kuti dothi lithe kuima mu nthawi ya ng’amba: 

• M’mene mwavindikirira munda wanu ndi bulangeti la Mulungu 

• Ngati dothi lanu liri labwino kwambiri mwachitsanzo lamibulu mibulu 

• Komanso kuchuluka kwa zinthu zamoyo zimene ziri munthaka yanu 

Kasinthasintha wa mbeu chaka chachitatu china chiri chonse amathandiza kuti pamene mbeu ina yalephereka chifukwa cha ng’amba muthe kukolola ina komanso pakakhala kuti kwagwa zilombo zoononga mbeu ku dera lanu. 

18) Ndalama zothiririra zimachepa Mungathe kuchepetsa nthawi imene mumagwira ntchito yothirira chifukwa chakusatembenuza dothi komanso chifukwa cha bulangeti lochuluka limene mumavindikira pa munda wanu.

19) Mbeu ndi zokolola zimachita bwino Kulima mu Njira ya Mulungu kumapangitsa malo oyenera kuti mbeu yanu idzitha kukula bwino popanda vuto lirironse, izinso zimathandiza kuti mukolole zochuluka. Mizu imangokula bwino pansi pa bulangeti komanso imagwiritsa ntchito chonde cha bulangeti lovunda komanso ndi kumasangalala ndi chinyenzi chimene chimapezeka m’mwambamwamba mwa munda wanu. 

20) Zokolola zimachuluka Abambo ake a Dickson amakolola matumba atatu pachaka. Dickson anatenga mundawu ndikuyamba kuulima ndipo anasintha malimidwe ake ndikuyamba Kulima mu Njira ya Mulungu. 

Dickson: Chaka choyamba anapeza matumba 5 

Chaka chachiwiri anapeza matumba 45 

Chaka chachitatu anapeza matumba 54 

Chaka chachinayi anapeza matumba 69 

Yosefe: Anakolola matumba 70 mu chaka choyamba kuchoka pa matumba 7 

Joji : Zokolola zake zinachulukitsidwa kasanu ndi kanayi.