Ndi zinthu zodabwitsa kwambiri, chifukwa pamene tigwiritsa ntchito mfungulo zitatu zimenezi tidzapeza kuti tidzakhala ndi chimwemwe chochuluka chifukwa cha ntchito ya manja athu. Kumbukiraninso kuti mukafesa ndi chimwemwe, mudzatutanso ndi chimwemwe koma mukafesa ndi nkhope yokwiya, yong’ung’udza ndi kudandaula, mudzakololanso ndikung’ung’udza.
• 2 Akorinto 9:7 “Munthu wina aliyense achite monga waganizira mumtima mwake: osati mokakamiza ndi mwakusafuna: pakuti Mulungu amakonda opereka mwachimwemwe.”
Kukhumba kwathu kuti tikayang’anire bwino, komanso kuti tikapeze phindu lopitirira, ndi chinthu chachiwiri mumayendedwe oyenera kutchedwa ana ake. Tikuyenera kuchita china chiri chonse chimene timapanga ngati tikupangira Yehova, ndi zipatso zonse za Mzimu Woyera zikuoneka monga umboni wa ntchito imene Mulungu wachita m’moyo wathu.