Palibe upangiri ndi ukadaulo wina uliwonse umene ungaphwanye temberero la umphwawi m’dziko la Afrika. 

Pakuyenera kuti mau ndi ntchito zonse zichitike 

Mfungulo za m’Baibulo 

Mau a Mulungu ndi mphamvu yokhayo pa choona chimene timakhalira komanso kutembenukira ku Mau ake kumabweretsa mavumbulutso ndi chizindikiritso kuti goli limeneri ndi la uzimu. Ngati tidzachita mfungulo za upangiri ndi kuyang’anira kokha basi ndiye kuti sitidzatha kuwaombola osauka 

• Hoseya 4:1-3 

• Masalmo 107:33,34 

• Yeremiya 23:10b 

Mu phunziro iri, mfungulo zisanu ndi imodzi ya mu Baibulo zidzavumbulutsa zinsinsi zimene dziko la Afrika lamangidwira ndi goli la umphawi komanso kupereka mayankho a umulungu a m’mene tingaphwanyire goli limeneri. 

Mfungulo 1: Kuzindikira Mulungu ndipo Mulungu yekha basi  

Vuto

Anthu a ku Afrika ali ndi zikhulupiriro zambiri za ufiti komanso kupembedza mizimu ya makolo awo. Amaula ndi asing’anga amapezeka m’midzi ya mbiri ndipo anthu amapita kukaombedza pa china chiri chonse makamaka pamene mwana akubadwa, pa matenda, pamene ana afika pa msinkhu wa chisodzera, pamdulidwe, pamaukwati ndi pamaliro. Asing’anga amatengedwanso ndikukapempherera nthaka kuti ibereke zochuluka. Apa amapereka nsembe monga za nkhuku, kuwaza mwazi wa nyama, kumwaza mafupa, kuika zinthumwa komanso zigaza za nyama m’makona.

Kupembedza mizimu ya makolo ndi pamene munthu amalemekeza makolo ake amene anamwalira kalekale pothira nsembe, kupanga miyambo ina ndi malumbiro. Kulambira uku sikuti kumachitika chifukwa cha chikondi ai koma chifukwa cha mantha ndi kuopa. 

• Yesaya 8:19-22 

• Levitiko 19:31 

• Deuteronomo 18:10 

• Deuteronomo 5:7,8 

• Mateyu 6:24 

• Masalmo 24:3 

Yankho

Pali Mulungu oona m’modzi yekha basi ndipo timabwera kwa Iye kupyolera mwa mwana wake Yesu Khristu, amene anafera pamtanda kuti ife tikhale ndi mphatso yaulere ya moyo wosatha. Choncho tsopano sitili a dziko lapansi ai koma tinatengedwa mu banja lake ndipo tiri ndi mwai omudziwa Mulungu ngati Atate wathu. 

Tikuyenera kubwerera ndikulambira Mulungu ndipo Mulungu yekha basi m’madera onse a moyo wathu, osati kumpingo kwathu lamulungu lokha basi ai. Mulungu samanyozedwa.. 

Miyambo 3:5,6 “Khulupirira Yehova ndi mtima wako onse ndipo usachirikizike pa luntha lako. Mlemekeze Iye mu njira zako zonse, ndipo adzaongola mayendedwe ako.” 

Lemba iri limatipatsa chitsogozo cha m’mene tingabooledzere. 

Khulupirira Yehova ndi mtima wako onse: 

Wina aliyense amene timamukhulupirira tidzapita ndikukafunsira kumeneko. 

Usachirikizike pa luntha lako

Yesu anakwaniritsa zonse zimene anayenera kuchita, osati kupyolera pakuzidalira yekha koma pakudalira Atate wake. Atate wake anamuonetsa Iye zimene anayenera kuchita ndipo anachita ndikupambana. 

• Yohane 8:28 

• Yohane 8:38 

• Yohane 5:19

Tangoganizani, ndi moyo wanji waulemerero umene ife tingakhale titati takwaniritsa kuchita chokhumba chake china chiri chonse cha pa moyo wathu. 

Mlemekeze Iye mu njira zako zonse

Mu njira zathu zonse akutanthauza choncho basi – dera lina lirironse, ku ntchito, mau, muzochita zathu ndi maganizo athu. Izi zikutanthauzanso kuti timuzindikire Iye pa kubadwa, pamene tikukula, pamaukwati, pamaliro, pamachiritso, tisanabyale, poyembekeza mvula, pokolola komanso pochita zina ziri zonse. 

Ndipo adzaongola njira zanu: 

Mu dziko lathu la Afrika tikusowekera kuti Ambuye aongole njira zathu zokhota komanso zopanda chiyembekezo zimene zakhala zikuwatengera anthu paulendo umene sukupita kwina kulikonse kwa nthawi yaitali. Kuongola kwa Mulungu kudzatitengera ife kuchidzalo cha malonjezano ake a moyo osatha. 

• Deuteronomo 8:18 

• Deuteronomo 7:13-15 

Ngati tikukhulupirira kuti ino ndi nthawi ya Afrika, tikuyenera kuphwanya ndi kuononga malo amene anthu amapereka nsembe ku mizimu ya makolo ao ndikutaya miyambo ya ufiti imene yakhala ikutimanga kwa nthawi yaitali. 

Apo tingathe kubwera ndi kukwera ku mapiri a Yehova ndi manja angwiro ndi mitima yoyera ndikumulambira Iye yekha muzimu ndi muchoonadi.