Mu Baibulo, chitsanzo chabwino chokuti Yesu samataya kanthu chikuoneka pamene Iye anadyetsa amuna zikwi zisanu
(Mateyu 14:14)
Zitsanzo za Mulungu zosataya kanthu:
• Mzungulire wa madzi
• Mzungulire wa Kaboni
Kutaya kwa munthu:
• Kugwetsa nkhalango mwachisawawa
• Ulimi wochetcha ndi kuotcha
• Kukokololoka kwa dothi
• Kuthamanga kwa madzi
• Kulima minda yaikulu popanda phindu ndi kutaya
Kulima mu Njira ya Mulungu kumaonetsetsa kuti pasakhale kutaya kanthu pa madera awa:
• Kusafuna kupeza malo ena olima chifukwa zokolola zimachuluka pa malo omwewo muli nawo.
• Mumateteza nthaka
• Mvula imalowa pansi
• Kuthamanga kwa madzi kumachepetsedwa
• Mumateteza chinyezi
• Chonde chimachuluka munthaka kupyolera mkuzungulira kwa zakudya za mbeu muchirengedwe
• Mbeu zimapanga m’thunzi mwachangu
• Zothira m’mapando zimagwira ntchito moyenera
• Nthawi komanso ndalama zimasungidwa