Chiyambi 

• Kompositi ndi zinthu zimene zavunda komanso kophwanyidwa ndi tizilombo timene timagwira ntchito munthaka mwachitsanzo mabakiteriya ndi mafangasi. 

• Mungathe kugwiritsa ntchito m’malo mwa fetereza. Pamene mukuika kompositi yabwino munthaka, alimi angathe kupeza phindu lofanana mwinanso loposera pofanizira ndi pamene akanagwiritsa ntchito fetereza. 

• Kompositi imathandiza kumanga zakudya za mbeu munthaka komanso imathandiza kuika zinthu zimene zinaonongeka mu dothi makamaka za chirengedwe. 

• Mulingo wabwino wa kompositi ndi umene ukuyambira pa mamita awiri mulitali, mamita awiri mulifupi komanso mamita awiri kukwera m’mwamba. 

• Pamene yakwanira, mulingo umenewu mungathe kuthira munda okwanira ekara imodzi imene iri theka la hekitala ya munda wa chimanga. 

• Sizovomerezeka kuti muchepetse mulingo wa kompositi yanu kuchepera pa mita imodzi ndi theka mbali zonse zitatu. 

• Yambani kutolera zipangizo za kompositi pamene mbeu yanu yangopanga kumene m’thunzi m’munda chifukwa nthawi iyi pamakhala zinthu zobiriwira zochuluka. 

Zidangodango 

Kompositi imapangidwa ndi zidangodango zazikulu za mitundu itatu; nayitulojeni, zobiriwira, komanso zatinkhuni / zouma. 

1) Naitulojeni 

• Akuyenera kukhala maperesenti 10 pa mulu wanu amene ali matumba 15 a manyowa. 

• Ngati palibe manyowa gwiritsani ntchito masamba ndi makoko a mbeu za mtundu wa nyemba zochuluka. 

• Chidangodango ichi ndiye mafuta pa kompositi yathu ndipo chimapangitsa kuti mabakiteriya ayambe kugwira ntchito yawo. 

• Zikhale maperesenti 45 pa mulu wanu. 

• Chiri chonse chimene chinadulidwa chiri chobiriwira ngakhale chitauma. 

3) Zatinkhuni zouma 

• Zikhale maperesenti 45 pa mulu wanu. 

• Tizinthu tankhuni timapangitsa kuti mafangasi ayambe kukula, izo ndi monga zikonyo zachimanga, mapesi, nthambi za mitengo, zikatoni, ndi zipalopalo za matabwa. 

• Zouma zimaonjezera kuchuluka, izo ndi monga, udzu ofolerera nyumba, masamba ndi udzu. 

Zidangodango zikuyenera kuikidwa pamalo osiyanasiyana kufikira zonse zitakwanira molingana ndi miyezo yake. 

Kumanga mulu wanu wa Kompositi 

• Kuonetsetsa kuti mulingo wina uliwonse ulipo okwanira ndizofunika kwambiri. 

• Mangani mulu wanu pogwiritsa ntchito mitundu itatu ya zidangodango. 

• Onetsetsani kuti mwaviika m’madzi zidangodango zobiriwira komanso zouma ndi zatinkhuni musanaziike pa mulu wanu. 

• Yambani ndi masentimita 20 a zouma zatinkhuni, kenako masentimita 20 a zobiriwira, kenako matumba awiri a manyowa onyowetsedwa bwino. 

• Pitilizani kuchita zimenezi kufikira mutamanga mpaka pa mulingo wa mamita awiri kupita m’mwamba.

Kutentha 

• Kutentha kwabwino kukuyenera kukhala pa mulingo wa madigili seleshiyasi 55 ndi 68. 

• Kutentha kumeneku kukuyenera kukhala chonchi kwa masiku atatu, izi zimathandidza kuti mbeu za udzu komanso matenda onse aferetu. 

• Gwiritsani ntchito choyezera kutentha kuti mudziwe kutentha kwenikweni. 

• Njira yina yosadula ndikugwiritsa ntchito chitsulo kapena waya. Mukachilowetsa pa mulu wanu kwa mphindi zingapo, tulutsani ndikuona ngati mungakwanitse kuchigwira kwa masekanzi asanu. Ngati mungakwanitse kutero ndiye kuti kutentha sikunafike madigili 70. Koma ngati simungakwanitse kuchigwira ndiye kuti mukuyenera kutembenuza kompositi yanu.

• Kutentha kukapitirira madigili 70, ndiye kuti mumapha tizilombo tofunika komanso mumatentha kaboni ndikumutaya. 

• Kompositi ikuyenera kukhwima komanso kuzizira pakapita masabata asanu ndi limodzi kapena asanu ndi atatu. 

Kutembenuza kompositi yanu 

• Poyamba tembenuzani pakatha masiku atatu (kutentha kusanafike pa madigili 70). 

• Sakanizani mulu wanu wa kompositi potenga zinthu za mkati kudzibweretsa kunja ndipo zimene zinali kunja kudzipititsa mkati. 

• Kutembenuza kumeneku kumapangitsa kuti kutentha kudzikhala pa mulingo woyenera, komanso zidangodango zimasakanikirana, kumapangitsa kuti zinthu za mkati zibwere kunja ndikuti nazo zakunja zitenthedwe, komanso mumapangitsa kuti mpweya uzitha kulowa komanso kuti muone chinyezi chanu ngati kuli kofunika kutero. 

• Ngati simutembenuza mulu wanu, ndiye kuti padzayamba kutuluka mpweya woipa komanso idzidzanunkha ndipo zotsatira zake kompositi yanu idzakhala yosachita bwino. 

• Anthu osauka akuyenera kungouzidwa kuti azitembenuza kompositi yawo pakapita masiku atatu mukutembenuza koyambirira ndipo akuyenera kuchita izi katatu ndipo kenako akuyenera kutembenuza pakapita masiku khumi ndipo akuyenera kutembenuza kanayi kapena kasanu. 

• Pakadutsa miyezi iwiri, kutembenuza kumakhala kutatha. 

• Mukamaliza kutembenuza, mukuyenera kuisiya kompositi yanu kuti ikhale kwa miyezi inayi kuti ichite bwino. 

Madzi mu kompositi yanu 

• Madzi amauluka ngati mpweya choncho akuyenera kubwezeretsedwamo. 

• Onetsetsani kuti mu kompositi yanu madzi ali pamulingo wa maperesenti 50. 

• Mungathe kuona izi pofinya m’manja mwanu. 

• Ngati madzi azidontha ndiye kuti ndiyonyowa kwambiri. 

• Ngati madzi sakudontha, ndipo pamene mukutsegula manja anu, zinyalala sizikuima monga munazifinyira ndiye kuti kompositi yanu ndiyouma kwambiri ndipo mukuyenera kuonjezera madzi. 

• Ngati mufinya ndipo pamene mutsegula dzanja lanu ndikuona kuti zinyalala ziri monga munafinyira ndiye kuti madzi anu ayandikira pa maperesenti 50.

• Pamwamba pa kompositi yanu mukuyenera kupangapo mwasulupu ndipo ikani udzu oforerera kapena matumba a mulandedza kuti madzi a mvula asamalowe onse ai, amenenso angathe kuziziritsa mulu wanu. 

Zoonetsa kuti kompositi iri bwino 

• Imaoneka mtundu wakuda wa bulawoni 

• Imanunkhira bwino 

• Imakhala ngati dothi la mibulu mibulu 

• Mukuyenera kumatha kuona mafangasi 

Mungathe kusunga kompositi yanu kwa zaka zingapo musanaigwiritse ntchito ndipo palibe china chiri chonse chingachokemo komanso ndiyosadula chifukwa mtengo wake ndi mphamvu zanuzo basi. 

Kompositi ikuyenera kumaoneka pa munda wa munthu aliyense ngati chizindikiro chakukhulupirika ndi zimene Mulungu anatipatsa popyolera mu kukwanira kwake mu zonse.