Yambani kulota maloto a Kulima mu Njira ya Mulungu amene alikufuna kuona goli la umphawi likuchoka pakati pa anthu osauka, ndikuwapangitsa iwo kuzindikira kuthekera kumene Mulungu anawapatsa. 

Kutakasika kwa m’Baibulo 

“Koma ine ndine ndani Ambuye?” mwina mungathe kuyankhula chomwechi. Inu ndinu ana amuna ndi a akazi a Mulungu wa m’mwambamwamba. Yesu anati, “chimene ndiona Atate wanga akuchita, chimenechonso ndichita. Chimene ndimva Atate wanga akuyankhula chimenechonso ndiyankhula”. Ife tikungoyenera kutsatira zimene Yesu wationetsera kuchita. Iye anabwera kudzatumikira, kudzapangira njira osauka, odwala, osweka mitima komanso otaidwa kuti apulumutsidwe ndikukhala mu lonjezo lake la moyo wosatha. Ife tiri ndi mwai wodabwitsa kuchita izi kupyolera mu chida cha Kulima mu Njira ya Mulungu pokwaniritsa ntchito ya pa Yesaya 58 – kusala kumene Mulungu anakusankha. Pakuchita izi, ndiye kuti tidzakhala ndi mwai wotumikira Mfumu (Mateyu 25:35) ndikukhala mum’dalitso wake pamene tikuganizira osauka ndiosowa thandizo (Masalmo 14:1-3) 

uthenga wabwino wa Mau komanso ntchito ungathe kugwiritsidwa ntchito mu dziko la Afrika ndikuphwanya temberero la umphawi ndi kuchotsa goli la kuzunzidwa. Anthu a Mulungu angathe kubweretsa kukhudza potengera uthenga uwu wachiyembekezo kwa anthu opanda chiyembekezo. 

Zimayamba ndi inu 

Ngati mukufuna kukhala mphunzitsi wa Kulima mu Njira ya Mulungu mukuyenera kupanga maphunziro awa bwino bwino ndipo muonetsetse kuti mwayamba ndi zochepa kenako ndikumakula ndikukhulupirika. Pitirizani kuwerenga mabuku awa komanso pitani kumaphunziro amene amachitika pafupi pafupi. 

Ngati mukufuna kukhala mphunzitsi weni weni wa Kulima mu Njira ya Mulungu mukuyenera kudutsa mukusulidwa komanso kuvomerezedwa. 

Izi ndi monga: 

• Kukhala nawo pa maphunziro osachepera atatu, 

• Kubyala komanso kutha kuyang’anira munda wanu wa chitsanzo mu nyengo yokhazikika. 

• Kuchita nao maulendo oyendera minda. 

• Ngati m’modzi wa aphunzitsi akuluakulu a Kulima mu Njira ya Mulunga adzaona kuti mwakonzeka, apa ndiye kuti tidzakuvomerezani kukhala mphunzitsi wa Kulima mu Njira ya Mulungu. 

Kumbukirani kuti Kulima mu Njira ya Mulungu si bungwe ai, koma ndi chida chimene chinaperekedwa ku thupi la Khristu. Ife sikuti tikufuna tikumangeni inu ndi Kulima mu Njira ya Mulungu ai koma kuti tikulimbikitseni kuti mudzigwiritsa ntchito Kulima mu Njira ya Mulungu. Ife cholinga chathu ndichokuti timasule anthu zikwi zikwi amene angathe kuphunzitsa uthenga wachiyembekezowu ali pansi pa mipingo yao, mautumiki ao komanso mabungwe ao amene si a boma. 

Kukhazikitsa Munda wachitsanzo 

Minda yachitsanzo kapena kuti yothiriridwa bwino ndi chinthu chodabwitsa kwambiri makamaka pophunzitsa Kulima mu Njira ya Mulungu. Minda iyi imakhala mamita asanu ndi limodzi mulitali komanso mamita asanu ndi limodzi mulifupi ndipo imathandiza kuphunzitsa anthu m’midzi yawo yomwe. Minda iyi ndiyosadula komanso imatenga nthawi yapakati pa maola awiri kapena atatu. Ngakhale iri minda yaying’ono, iyo imakhala ndi kuthekera kophunzitsa alimi m’mene angathe kuchitira Kulima mu Njira ya Mulungu pa minda yawo. Iyo imawapangitsa ophunzira kuti athe kuona bwino bwino pamene zinthu zikubwerezedwa mokwanira komanso kuwapatsa mwai okuti athe kuchita paokha. Ichi chimakhala chitsanzo chokoma makamaka chifukwa chokuti wina aliyense amachita nao ndipo pamakhala chisangalalo. 

Tsatanetsatane wa zofunika zokhuzana ndi munda wachitsanzo zingathe kupezedwa kuchokera mumakanema a Kulima mu Njira ya Mulungu komanso mu buku la mphunzitsi.

Milozo yopambana yofuna kuona kuti mukathe kukhazikika pa mudzi 

• Kudzipereka pa maphunziro kwa zaka zisanu kapena zisanu ndi chimodzi. 

• Pezani munthu wamtendere. 

• Kupereka kwa ulere kwa onse – pasakhale kusiyanitsa. 

• Mulingo wa malo – sungani makulidwe a munda wanu wachitsanzo. 

• Ngati mumakhala pafupi ndi mudzi umene mukuphunzitsa, gawani maphunziro anu mzigawo zing’onozing’ono, ndipo atengereni alimi mu nyengo yonse ya zochitika zakumunda. 

• Muonetsese kuti mukuphunzitsa mu nthawi yoyenera pachaka. 

• Aikeni alimi m’magulu ang’ono ang’ono. 

• Musagawe zinthu zaulere pokopa alimi monga fetereza komanso mbeu. 

• Kuyendera minda ndi kukaona zochitika ndi chida champhamvu powaphunzitsa alimi. 

• Pemphero. 

Kuomba mkota 

Pamene Kulima mu Njira ya Mulungu kukufalikira m’maiko, chirimbikitso chathu kwa inu nachi – musaiwale kuti OSAUKA ndiye anthu amene tikuyenera kuwafikira. Iwo ali ndi malo a padera mumtima wa Mulungu ndipo tikuyenera kuonetsetsa kuti tikuwatumikira iwo ndi mitima yathu yonse. 

Tiyeni tiutenge uthenga umenewu motakasika ndi kumvera Mau a Mulungu, komanso mozika mizu monga ya Khristu ya chifundo komanso tiwaphunzitse anthu ndi chikondi makamaka iwo osaukitsitsa kuti akathe kumasulidwa ku goli la umphawi.