Poganizira za chikhalidwe cha Mulungu, mphamvu komanso chuma chake, zingakhale bwanji zotheka kumubera Iye? Molingana ndi malemba pa Malaki 3, ndizotheka kumulanda Mulungu kudzera muchakhumi ndi zopereka zathu. Lemba iri linaperekedwa kwa anthu amene anali alimi komanso mitima ya anthu pamene akupereka kwa Mulungu, pamakhala zinthu zotsatirapo makamaka pa nkhani ya za ulimi.
• Malaki 3:7-12
Chakhumi, ngakhale chimakwaniritsidwa popereka ku mpingo kapenanso kwina kuli konse kumene munthu akumva kuti akapereke, kumakhala kupereka kwa Mulungu. Mulungu sikuti amafuna chuma chathu komanso zochuluka zathu ai, koma zimamuonetsera Iye kumene kuli mitima yathu pamene timuzindikira Iye poyambirira mu kupereka kwathu.
• Mateyu 6:21
Kaya tipereka ndalama zochuluka kwambiri kapena zochepa monga za mkazi wamasiye, izi sizimamukhuza Mulungu ai. Iye amadziwa zimene tiri nazo komanso kuti zatengera chiyani kuti ife timupatse Iye. Chopereka chonga cha mkazi wamasiye chimakhala cha mtengo wapamwamba kwambiri kuposera ndalama zankhaninkhani zimene mungapereke ku mpingo. Mulungu amadziwa cholinga cha mitima yathu tisanapereke ndipo pamene akupereka madalitso, Iye adzayang’ana cholinga cha mtima wathu osati kuchuluka kwa chopereka chathu ai.
Chinthu chodabwitsa kwambiri chokhuzana ndi kupereka kwa Mulungu ndichokuti, izi zimapangira ubwino ife tomwe. Izi sizinayambitsidwe ndi Mulungu ndi cholinga chokuti munyumba yosungiramo mudzikhala katundu ai koma kuti woperekayo akathe kudalitsidwa. Madalitso amabwera kwa woperekayo katatu konse:
1) Mulungu analonjeza kuti adzatsegula zipata zakumwamba ndikutsanula m’dalitso osowa pokhala. Miyambo 3:9
2) Mulungu mwini wake adzadzudzula zolusa kuti zisakaononge zipatso za m’minda yathu…
3) Mulungu adzapangitsa maiko onse kukutcha iwe odala chifukwa udzakhala chimwemwe.
Kupereka kwa Yehova kumamupatsa ulemu komanso timamuzindikira mu njira imene ife sitingathe kumvetsetsa. Kupereka kwa Mulungu kumatikakamiza ife ndikukhala anthu osadziganizira tokha ndi osadzikonda ndipo timaika ufumu wake patsogolo pathu.