Mu Kulima mu Njira ya Mulungu timawalimbikitsa alimi kuti adzibyala mbeu zosiyanasiyana, komanso kubyala mbeu za kapitiriza ndi mbeu zina zimene zimabweretsa manyowa munthaka.
Kasinthasintha wa mbeu
• Kasinthasintha wa mbeu akuyenera kuchitika chaka chachitatu chiri chonse.
• Gawani munda wanu m’magawo atatu ofanana ndipo magawo awiri oyambirira mukuyenera kulimapo mbeu ya chakudya yaikulu mwachitsanzo chimanga, ndipo gawo lachitatu likhale losinthira mbeu mwachitsanzo nyemba.
•Onetsetsani kuti mbali imodzi ya mbali zitatu mukuchita kasinthasintha wa mbeu.
• Kasinthasintha wa mbeu amathandiza kuthetsa matenda komanso tizilombo toononga mbeu. Amathandiza kuti dothi lichite bwino komanso kuchulukitsa chonde, mbeu izi zimapereka zakudya zomanga thupi ndi zotiteteza ku matenda mu zakudya zathu komanso zimathandidza kuti pasakhale kutaya ndalama mu nthawi ya ngozi.
Zinthu zina zokutsogolerani:
• Sinthani mbeu yosagawanikana diso ndikubyala mbeu zogawikana maso.
• Komanso ndikwabwino kubyala mbeu za mitundu ya nyemba monga nyemba zimene, soya, nandolo, nsawawa, mtedza komanso mungathe kubyala mbeu monga mpendadzuwa, mbatata, ndi mbeu zamasamba.
• Ndime yachitatu mungathenso kuigawa kangapo ndikubyala mbeu zingapo monga zamasamba ndicholinga chokuti mudzigwiritsa ntchito pakhomo.
Mbeu za kapitiliza ndi mbeu zimene zimabyalidwa pamene mbeu zina zakhwima ndipo izi zimalimbikitsidwa m’madera m’mene nyengo yawo imawalola kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito chinyenzi chotsalira. Mbeu za kapitiliza zimasiyana ndi mbeu zachiwiri zimene mumabyala mukakolola mbeu yoyambirira. Khalani osamala posafulumira kubyala mbeu yanu ya kapitiliza chifukwa izi zidzapangitsa kuti mbeu yanu yoyambirira ivutike mwachitsanzo nandolo akuyenera kubyalidwa pamene chimanga chikufa masamba
Dziwani izi: mbeu za kapitiliza ndizosiyana ndikuphatikiza mbeu zingapo m’munda umodzi ( mwachitsanzo kubyala nyemba pakati pa mizera ya chimanga). Ife sitimalimbikitsa m’chitidwe osakaniza mbeu.
39
Mbeu zobiriwira zobweretsa manyowa
Mbeu zobweretsa manyowa zakhala zikugwiritsidwa ntchito kwa zaka zingapo pothandiza kuchulukitsa bulangeti la Mulungu komanso kuika nayitulojeni munthaka, kuonjezera chonde munthaka, kulimbana ndi udzu, kuteteza kukokololoka kwa nthaka, kupereka zakudya zanyama, kubweretsa ndalama zoonjezera komanso zakudya kwa anthu. Izi zimakhala ngati kulima kompositi m’munda mwanu komanso ubwino wake kupambana kompositi ndiwokuti izi sizimafuna kuthiriridwa komanso ntchito yake imakhala yochepa.
Izo zimachita bwino ku nyengo yapakati komanso kumadzulo kwa Afrika komanso m’madera m’mene amalandira mvula yotalikirapo. Ganizo lathu ndilokuti mbeu zimenezi zizilimidwa mu nthawi ya mvula yochepa ndi cholinga chokuti dothi lidzikonzeka musanabyale mbeu yeniyeni.
Chitsanzo:
• Mbeu za mtundu wa nyemba: nkhunguzu, kalingonda, nseula, alifafa, nsawawa ndi zina.
• Zosagawikana diso: tirigu, reyi ndi oti.
Nsawawa, nandolo ndi tirigu zingathenso kubyalidwa ngati kapitiliza.