Tikuyenera kumutenga Mulungu mu madera onse a moyo wathu, kuphatikizirapo minda yathu. Tikuyenera kutenganso nthaka yathu ndipo izi zimatheka pamene ife tazindikira mafano amene timapembedza, ufiti, kukhetsa mwazi osalakwa, ndi njira zina zoipa zimene zimatipangitsa ife kuyenda m’matemberero. 

• Yakobo 5:14 “pemphero la munthu olungama likhoza kuchita kwakukulu.” 

• Miyambo 15:29 “Yehova amakhala kutali ndi ochimwa, koma amamva pemphero la olungama” 

• 2 Mbiri 7:14 “Ngati anthu anga amene amatchulidwa ndi dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zawo zoipa, pamenepo ndizamvera m’Mwamba ndi kukhululukira zochimwa zao ndi kuchiritsa dziko lao.” 

Ngati amene tasandulika olungama a Mulungu kupyolera mwa khristu Yesu, tikuyenera kumapemphera, kukhulupirira Mulungu chifukwa cha Mau ake ndi malonjezano ake kuti minda yathu ndi midzi yathu ikathe kutukuka. 

Timaima pa Mau a Mulungu ngati ana a Mulungu pakutenga Yesu ndikumuika m’madera onse a moyo wathu. Yesu anatiphunzitsa m’mene tingapempherere “lolani ufumu wanu udze pansi pano monga kumwamba.” 

Mungaime bwanji pa Mau a Mulungu 

• Kudzichepetsa ndiye malo oyambira (Yakobo 4:10) 

• Funafunani nkhope yake osati manja ake ai (Deuteronomo 4:29) 

• Vomerezani ndi kulapa zochimwa zanu 

• Pemphani ndipo kudzapatsidwa kwa inu(Mateyu 7:7, Yakobo 4:2) 

• Pempherani 

• Imani nji (Aefeso 6:10, Aroma 8:37) 

Mulungu ali mbali yathu, ndipo samasutsana nafe ai ndipo ndichokhumba chake kuti minda yathu idalitsike. Tengani ndi kubwezera m’chimake dziko limene liri m’manja mwa m’daniyo.