Vuto

Midzi ya mbiri iri m’malo moti chitukuko sichingathe kufika ndi pang’ono pomwe. Anthu awa amangokhala ndicholinga chokuti apulumuke basi, mwina chifukwa chokuti amalandira chakudya chaulere ndipo samachokako ai. Iwo amakhala moyo wokumva bwino kuti amene amawapatsa chakudya adzawapatsanso pamene adzachifuna kawiri. Ngati tilimbikitsa kudalira pa munthu, ndiye kuti tikuwalimbikitsa osauka kuyang’ana malo ochokera zinthu olakwika, kwa munthu osati kwa Mulungu ai. 

• 2 Atesalonika 3:10 “ngati munthu sagwira ntchito, asadye.” 

Ntchito sitemberero ai koma ndi m’dalitso. Anthu ambiri mwa osauka amenewa ali ndi minda imene ikungokhala kumidzi kwawo. 

Dziko la Afrika ndilotchuka kwambiri ndi nkhani yakupemphapempha pa dziko lapansi, koma Mulungu angathe kutembenuza zimenezi, kusintha dziko lopemphapempha kukhala la mwana alirenji. 

Njira ya Mulungu ndiyokuti anthu akuyenera kutukuka molingana ndi malamulo ake, pamene Iye amapereka mphotho molingana ndi lamulo lakufesa ndi kukolola, komanso lamulo loyang’anira ndikukhala okhulupirika ndi zimene unakhulupiridwa nazo. 

Yankho: Tikuyenera kupereka ndicholinga chokuti tithe kulandira 

Pamene tidzamvetsa kuti Mulungu ndiye chiyambi cha china chiri chonse chathu komanso kuti kukwanira kwake mu zonse kumakhala ndi ife nthawi zonse, tingayambe kukhala anthu osadalira anthu ena koma pamalonjezo ake basi. 

• Machitidwe 20:35 “Kupereka kumadalitsa koposa kulandira” 

Kusintha maganizo kuchokera pakulandira ndikubwera pakupereka kuli ndi zinthu zabwino zambiri, apa mungathe kufikira mafuko ndi uthenga wabwino wa Ambuye Yesu Khristu. 

• Luka 6:38 

• Miyambo 28:19

Mu ulimi palibe chitsanzo chachikulu choposera pamenepa chimene timayenera kumapereka ndi kumafesa mowirikiza kuti tikathe kukolola. Tikuyenera kufesa mbeu zathu, fetereza ndi zothira m’mapando zina, anthu ogwira ntchito, nthawi, kuyang’anira komanso ndalama zoyambira. 

Sitingangokhala tikutenga koma osabwezera kena kake pambuyo ai. Baibulo limanena kuti tidzakolola zimene tafesa. 0 kuchulukitsa ndi 0 yankho lake ndi 0, 0 kuchulukitsa ndi 100 yankho lake ndi 0, pamapando 22,222 popanda kuthirapo kena kalikonse yankho lake lidzakhala 0. ngati simupereka china chiri chonse ngakhale ku dothi labwino simungathe kupeza kena kalikonse. 

Njira zimene tingafesere: 

Fesani moolowa manja 

2 Akorinto 9:6 “ ichi ndiyankhula kuti, iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta koma iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.” 

Fesani ndi chidziwitso 

M’maiko ambiri a mu Afrika, chimene chikubweretsa umphawi sikuti ndikusagwira ntchito kwa anthu ai koma kupanga zinthu mopanda chidziwitso. 

• Hoseya 4:6 “anthu anga akuonongeka chifukwa chakusadziwa” 

Fesani mokhulupirika 

Chinsinsi cha Kulima mu Njira ya Mulungu ndikuyamba mochepa ndikukhala okhulupirika pazazing’ono. 

• Luka 16:10 “Iye amene amakhala okhulupirika pazazing’ono amakhalanso okhulupirika pazazikulu;” 

Fesani ndi chimwemwe 

Cholinga chimene timaperekera ndi chinthu chofunika kwambiri. 

• 2 Akorinto 9:7 

• Nehemiya 8:10b 

Chimwemwe chathu chimapezeka mwa Ambuye poyambirira, koma chimwemwe chomwechi chikuyenera kudutsa mbali zonse za moyo wathu komanso ku ntchito za manja athu.