Kulima Mu Njira Ya Mulung
Kuwapatsa zida anthu osauka kuti akhale ndi moyo wochuluka mwa Khristu Yesu
Dziko la Afrika liri ndi chuma chobisika chochuluka kuposa maiko onse a dziko lapansi. Liri ndi miyala ya mtengo wapatali yochuluka, zitsulo zodula komanso zitsime zamafuta, liri ndikuthekera kwakukulu pa nkhani ya zamalimidwe, anthu odabwitsa, madzi ochuluka komanso mitsinje yambiri ndi nyama zakuthengo zambiri zimene zingalipangitse dzikoli kukhala malo okuti alendo a maiko ena akanatha kumabwera ndikudzaona zinthu zimenezi.
Koma mosutsana ndi kuthekera kumeneku, Afrika ndi dziko la umphwawi kwambiri, komanso anthu amakhala movutika kwambiri, kuli njala, kusowa zakudya kochuluka m’matupi a anthu, imfa za ana zambiri, matenda, nkhondo, kudalira anthu ena, maphunziro achabechabe, kutha kwa nkhalango, katangale ndi ziphuphu komanso kusayenda bwino kwa chuma ndi kugwa kwa ndalama ngati zizindikiro zimene dzikoli likudziwika nazo.
Alimi ang’ono ang’ono alipo okwanira maperesenti 85 mwa anthu onse a ku Afrika, amene akukhala mumoyo osowa zakudya komanso opanda chiyembekezo. Zokolola za alimi amenewa palipano ndizochepa kwambiri kotero kuti sizikutha kukwanira mabanja ao zimene zapangitsa kuti chakudya chankhaninkhani chiziitanitsidwa kuchokera maiko a kunja chaka ndi chaka.
Kulima mu Njira ya Mulungu ndi yankho lodabwitsa la Mulungu ku mavuto akusowa zakudya komanso umphawi umene wagwira anthu osauka a kumudzi. Kulima mu Njira ya Mulungu siupangiri okha ai koma muli zinthu zabwino za mu Baibulo zokhuzana ndi kuyang’anira komanso ukaswiri pa nkhani za malimidwe, kuwapatsa zida osauka kuti akathe kutuluka mu umphwawi ndi zimene Mulungu waika m’manja mwawo komanso kuvumbulutsa chidzalo cha malonjezo ake a moyo wochuluka.
Pamene munthu wasinthika mtima ndi mphamvu ya Yesu, kenako pamakhala kukonzanso kwa malingaliro poyang’anira bwino ndipo pamapeto pake pamakhala ntchito yeniyeni imene imabweretsa chiombolo pa munda.
Kulima mu Njira ya Mulungu kwakhala kukuchita bwino kuyambira mu chaka cha 1984, pamene a Brian Oldreive kwa nthawi yoyamba anagwiritsa ntchito njira imeneyi pa munda waukulu otchedwa Hintoni ku Zimbabwe, ndipo pamapeto pake anapezeka akulima munda waukulu mahekitala 3,500.
Kuyambira masiku oyambirira amenewo, Kulima mu Njira ya Mulungu kwafalikira m’maiko ambiri, ndipo kukugwiritsidwa ntchito ndi mipingo, atumiki a Chikhristu ndi mabungwe amene siali a boma mu dziko lonse la Afrika. Palipano mu chaka cha 2009 Kulima mu Njira ya Mulungu kwafikira maiko monga Angola, Benin, DRC, Ethiopia, Kenya, Lesotho, Madagascar, Malawi, Mozambique, Namibia, Nigeria, Rwanda, Sierra Leone, South Africa, Swaziland, Tanzania, Uganda, Zambia, Zimbabwe ndi maiko ena osiyanasiyana mu Afrika, komanso tafika ku Mexico. Nepal, British Gayana, Amereka, Kumangalande ndi ena ambiri.
Kulima mu Njira ya Mulungu ndi mphatso yaulere ku thupi la Khristu ndipo sikwampingo ulionse ai, si kwa bungwe lina lirironse, koma ndi kwa anthu ogwira ntchito pamodzi amene anamva mumtima mwawo kuti athandize anthu osauka. Ungwiro, mayendetsedwe ndi ndondomeko za Kulima mu Njira ya Mulungu kumapangidwa ndi gulu la akuluakulu ogwira ntchito modzipereka amenenso ali akaswiri pophunzitsa.
Mfundo ya kuyang’anira osati ya umwini yakhala ikugwiritsidwa ntchito ndicholinga chokuti pakhale kufalikira kopanda malire kwa chida chimenechi chimene chingathe kusintha miyoyo ya osauka.
Mau a Mulungu amati ‘anthu anga akuonongeka chifukwa chakusadziwa.’ Tikuyenera kuzindikira kufunika kowaphunzitsa anthu osauka kukhala okhulupirika pa ulimi pamene kuthekera kwina kumene kuli m’dziko la Afrika kusanavumbulutsidwe.
ALL COURSES | MOJA APP | BUSINESS | AGRI