Vuto:
Mzimu wodalira anthu ena wakhala ulipo kwa zaka zambiri makamaka popatsidwa zinthu komanso kukhala ndi chiyembekezo koma zinthu izi zikuoneka kuti zikuchulukirabe chaka ndi chaka. Palibe njira ina iriyonse imene dziko la Afrika lingathe kufikira kuthekera kumene liri nako ngati anthu eni ake sangathe kutero.
Yesaya 58 akutikumbutsa ife kuti tikuyenera kumakwaniritsa kusala koyenera, kumasula, kuchotsa ndi kuphwanya goli. Chinthu chimodzi cha goli la umphawi ndi chimzimu chodalira anthu ena.
Chiyambireni chirengedwe cha munthu, wakhala akuyesetsa kuti akhale okwaniritsa zonse pa yekha, kuchita zinthu mu njira ya iye mwini, kudalira nzeru za yekha mwini m’malo modalira nzeru za Mulungu. Izi zapangitsa kuti munthu akhale olephera mu njira zambiri.
Yankho: Kudziwa Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu
Mu Kulima mu Njira ya Mulungu sitimalimbikitsa kuti anthu akhale odzidalira okha ai, koma kuti azindikire kukwanira kwa Mulungu mu zonse kumene kumatipangitsa ife kuti tipeze phindu.
Iye ndiye chiyambi chathu cha china chiri chonse komanso mwa Iye timapeza kuchulukitsa. Kukwanira kwa Mulungu mu zonse ndi kwamuyaya, ndipo palibe malire mu nkhokwe zake
• 2 Akorinto 9:8
kubooleza kumabwera pamene tilapa chifukwa chodalira munthu, kuphatikizirapo ife eni, tikuyenera tisiye pambali kudzikuza kwathu, ndikudzichepetsa tokha komanso kuzindikira kuti Iye ndiye kumene timapeza zosowa zathu zonse.
Tikuyenera kutsegula maso athu ndikuona zimene ziri zopezeka kwa ife
Kudziwa Kukwanira kwa Mulungu mu zonse kumathetsa chimzimu chodalira ena.
• 2 Mbiri 14:11
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu mwa Inu
• Deuteronomo 8:18
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi ulimi
• Genesis 2:15
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi nthaka
Nthaka inapatsidwa kwa ife ndi Mulungu kuti tiziiyang’anira, kuilima komanso kuisamalira. Sikuti ndi yathu ai koma ndi Yake.
• 1 Akorinto 10:26
• Levitiko 25:23
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi mbeu
Pamene Mulungu analenga zomera, anazilenga ndi kuthekera kokuti zidzitha kupanga mbeu pazokha ndi kuchulukana.
Mbeu zahaiburidi kufanizira ndi mbeu zimene zimatha kubwerezedwa, zamasika (OPV)
• Genesis 1:11-13
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi Bulangeti la Mulungu
Bulangeti la Mulungu ndi chinthu chodabwitsa chimene chinaperekedwa pa zifukwa zopindulitsa zambiri – muone mwatsatanetsatane pa zifukwa 20 zimene timachitira m’mene timachitira.
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi zothira m’mapando:
(Manyowa, dothi la pachulu, kompositi)
Kuti mukolole zochuluka, pakuyenera kukhala kudzipereka kokuti mufese zinthu zimene muli nazo m’mapando anu.
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi zida zogwirira ntchito
Pa Eksodo 4:2 Mulungu anamufunsa Mose kuti “chimene chiri m’manja mwakocho ndi chiyani?” Mose anayankha “ndodo.” Kodi ife tiri ndi chiyani m’manja mwathu, ngati zida zothetsera umphawi komanso kusowa kwa zakudya mu dziko lathu?
Yankho ndiyokuti “Khasu.”
Kukwanira mu Zonse kwa Mulungu ndi mvula ndi kuchulukitsa
Pakupereka kwake kwa mvula, Mulungu amadalitsa ana ake ndipo mvula imapangitsa kuti mbeu ikhale ndi moyo ndikuchulukitsa zokolola.