Vuto

Kachisi wa m’moyo wathu ali pabwinja chifukwa chokuti takhala tikutumikira maganizo athu odzikonda eni komanso njira zathu zoipa ndipo sitinayende mu njira za Mulungu. 

Ngati ife, ana a Mulungu tiri kachisi wa Mulungu monga Mulungu wanenera, apa tikuyenera kuonanso m’mene kachisi wathu aliri. 

Tikuyenera kusamala njira zathu!

Hagai 1:2-11 samalani njira zanu-kachisi wanga ali pa malo a bwinja 

Zitsanzo zingapo zochepa za matemberero amene timayendamo ngati njira zathu sizikugwirizana ndi njira za Mulungu: 

a) Temberero kupyolera kukhetsa kwa mwazi ndi ziwawa 

• Nkhani ya Kaini ndi Abele 

• Zitsanzo zambiri mu Afrika 

• Yesaya 59:3 

b) Temberero la moyo waufupi 

Nthawi imene anthu amakhala ndi moyo ku Zambia, Zimbabwe, Malawi ndi ku Mozambique ndi zaka zosapitilira 37. 

• Masalmo 34:12 

• 1 Atesalonika 4:3 

• Aroma 6:23 

c) Temberero pa zimene nthaka imabereka (zokolola zochepa) 

Mu buku la Hagai, muli nkhani yochititsa chidwi kuwerenga kuti ndi Mulungu amene amagwira mvula komanso kupangitsa kuti nthaka isabereke zochuluka. 

Yankho: Kubwezera kachisi 

Poyesayesa kuti tipeze mayankho a uMulungu ku mafunso ovuta monga umphawi wadzaoneni umene watizungulirawu, timayamba posamala njira zathu pakuti ife ndife kachisi wa Mulungu wa moyo. 

Mwina sitingathe kusintha dziko lathu, koma wina aliyense wa ife angathe kusamala njira zake, kusintha miyoyo yathu ndikukhudza miyoyo ya mabanja athu ndi anthu amene timakhala nawo, zimene pamodzi zingathe kubweretsa kusintha kwakukulu. 

• 1 Petro 2:5 

• Hagai 2:18-19 

• 1 Atesalonika 2:12 

• 2 Akorinto 6:16 

Tiyeni ife ngati ana ake amuna ndi akazi tikhale odzipereka kumanganso kachisi wa Mulungu m’miyoyo yathu, pakusamalitsa njira zathu ndikuzifanizira ku njira za Mulungu, osati mu uzimu okha ai, koma m’malingaliro ndi kuthupi komwe.