Cholinga cha kuyang’anira mu Kulima mu Njira ya Mulungu ndikufuna kukhazikitsa phindu lopitirira. Pali madera ambiri pamene pamakhala kusunga komanso kuteteza chuma monga dothi, chinyenzi, zakudya za mbeu, nthawi yokonza munda wanu ndi ndalama zimene mumagwiritsa ntchito ngati mukulima mu Njira ya Mulungu. Komabe kuti Kulima mu Njira ya Mulungu kuchitike bwino, mfungulo zakuyang’anira zikuyenera kukhazikitsidwa ndikukonzedwanso bwino.
Mfungulo zitatu za Kulima mu Njira ya Mulungu ndi kuchita Zinthu
Mu nthawi yake, mwapamwamba kwambiri ndi mosataya kanthu
Mfungulo 1: Mu nthawi yake
• Genesis 1:14-19 Chirengedwe cha Mulungu kuchokera pa chiyambi chimatipatsa ife maziko amene timaonerapo nthawi.
• Mulungu analenga masiku, miyezi, zaka komanso nyengo
• Mlaliki 3:11 “analenga china chiri chonse m’malo mwake mu nthawi yake.”
• Kukonzanso minda yathu munyengo yoti tamaliza kukolola
• Kutolera manyowa, bulangeti la Mulungu ndi mbeu. Kupanga kompositi nthawi yobyala isanafike.
• Kubyala munthawi yake – mu chigawo cha kum’mwera kwa Afrika kumene kumagwa mvula nthawi yotentha mumataya makilogalamu 120 a chimanga tsiku ndi tsiku ngati mwabyala patadutsa pa 25 Novembala (Ngati mvula itagwa)
• Kupalira mu nthawi yake.