Alimi mwachidziwikire ndi komphweka kuokera mbeu m`mapando kusiyana ndi ndikufesa njere nthaka, kotero kapangidwe, kamangidwe ndi kasamalidwe ka malo ofesera mbeu kakuyenera kuchitidwa ndi alimi aluso kwambiri. Kuokera kwa mbeu kuli ndi ubwino kwambiri chifukwa choti kumayambiriro kwenikweni kwa masamba omwe amera umagwira ntchito malo ochepa okha, m`malo mwa munda onse omwe mbeu zamera kumene. Mbeu zikangofika mulingo wa 7- 10cm mwa mbeu zabwino zimenezi ziyenera kuokeredwa ndipo sipamakhala vuto yakupachiza kwa mbeu ndipo zimakula mosangalala. 

Malo ofesera mbeu angathe kukhala mabedi okwera kapena m`makontena. Kasungidwe bwino ka madzi mu nthaka ndi njira yomwenso tikuyenera kuyang`ana mosamala. Malo ofesera mbeu akuyenera kuti akhale otetezeka komanso osatalikirana ndi madzi. Pa nthunzi ndi pabwino kwambiri kumayambiliro kwenikweni pofuna kubzala mbeu za masamba. Nthunzi umenewo utha kukhala womangidwa ndi masikito, masamba amitengo, udzu ofolera, msungwi kapena timitengo. Chobweretsa nthunzi chimenechi chikuyenera kukhala chachitali bwino cholinga choti wothilira komanso kusamalira munda azichita mosavuta, ndipo chiyenera kukhala chachitali mamita awiri kuchokera pansi. Onetsetsani mmene dzuwa likuyendera ndipo konzani nthunzi kapena denga moyenerera. Ukuyenera kukhala wotalika pang`ono m`mbali kusiyana ndi manazale a mbeu, cholinga choti pakhale nthunzi wokwanira omwe ungaperekedwe kwa tsiku lonse. 

Kusakaniza dothi lofesera mbeu ndi kofunikira kwambiri ku thanzi la mbeu zathu.

Sakanizani imodzi ya magao atatu dothi, mchenga imodzi ya magawo atatu ndi komposite osefa bwino imodzi ya magawo atatu. 

Kubzala mbeu m`malo ofesera mbeu/m`mabedi 

Pangani bedi m`mbali mukhale masentimita okwana 100, kukwera mmwamba masentimita okwana 15, italike mene mukufunira malingana ndi nambala ya mbeu yomwe ikufunikira (onani chaputala 2.4). Mwazani kompositi wakale wosefa bwino pamwamba 5 cm sakanizani bwino ndi dothi, nyowetsani ndi madzi bwinobwino, salazani bwino ponse pakhale fulati. Ndi ka thabwa kosongola lembani kangalande kozika 1cm, bwerezani pa 10cm iliyonse. Ikani mbeu 5cm kapena bokosi la macheso motalikirana ndi imnzake, cholinga choti pasazakhale kukolana kwa mizu mukamazachotsa. Mukamaliza kubzala, kwilirani ndi dothi labwino koma musakwilire ndi mabuluma cholinga choti mbeu zimere mosavuta. 

Mofesera Mbeu 

Kufesera mbeu mu zida zofesera mbeu monga ma thiree ndi upangiri odalilika kwambiri kuti mbeu zomwe zamera zisavute kuchoka, komanso sitimaononga madzi ndi nthawi ya ogwira ntchito, ndipo mizu imachulukana bwino kupangitsa mbeu kukula ndi thanzi. Njira ina imene timagwiritsa ntchito ngati mofesera mbeu ndi zosungira za madzira zakale kapena mathiree opanga tokha pakhomo. Musanagwiritse ntchito zosungira madzira zakale muzitsuke bwino ndi burichi kuti matenda ndi tizilombo tina tife. Dzadzani thiree ndi kompositi wakale wosefa bwino kenako boolani pango’ono pakati ndi chala ikani mbeu imodzi ndi kukwilira pang’ono 1cm ndi dothi lofewa bwino, pamwamba pasakhale zibulumwa kapena maudzu komanso musagogomezepo kuti mbeu imere mosavuta. 

Lembani mbeu, mtundu wake komanso tsiku lomwe mwafesa pa thabwa kapena pa pepala cholinga choti mudziwe zonse za mbeu zomwe muli nazo. 

Kuthilira 

Kompositi wakale wosefa bwino amapangitsa kuti madzi ambiri asungike komanso chinyontho chisathawe ndipo nthunzi wochepa wa pamwamba umateteza mbeu kumavuto akusowa kwa madzi. Kuthilira mwapang`ono kamodzi pa tsiku ndi mpope wammanja (Wota keni) ya mabowo ang`onong`ono kuzakhala kokwanira, koma m`Madera anyengo yotentha kwambiri ndibwino kuthilira kawiri pa tsiku. 

Onetsetsani kuti musathilire mopitilira muyezo chifukwa zitha kuyanbitsa matenda onyala oyambitsidwa ndi mabakiteliya ndi kumulakwitsa mlimi n`kumathilira madzi ambiri. Onetsetsani mbeu zanu ndipo gwirani dothi lanu mmene lilili pafupipafupi cholinga choti mudziwe chinyontho mmene chilili ndi kupanga ndondomeko zoyenera kuonjezera 

Kuokera 

Pakatsala masiku khumi kuti muokere, umitsani mbeu pang’ono pozionetsera ku dzuwa ndi kuchepetsa kathiliridwe. Ndizophweka kuchita pamene tagwiritsa ntchito denga la nthunzi wa masamba amitengo, msungwi kapena udzu, mumayamba kuchotsa pang’ono pang’ono mpaka kumaliza yonse kuti dzuwa lifikire mbeu zija. 

Chepetsani kathiliridwe ka madzi ndi theka pa masiku anu othilira, ndipo muzitha kukhala mosathiliridwa kwa tsiku lonse. Komabe, pasanafike nthawi yookera onetsetsani kuti mbeu zikulandila madzi ochuluka isanafike nthawi yookera ndipo azikhala okwanira mwadongosolo kuti mbeu ikhale yolimba. 

Onetsetsani kuti pamene mukuchotsa mbeu m`mabedi muli ndi chochotsera chabwino, chokuthwa, chogwirika kuti muthe kuchotsa mizu yokwanira ndi kompositi wa mbeu zili pomwepo. Mbeu zikuyenera kukhala pa nthunzi kufikira nthawi yobzala zimene zikuyenera kuchitika mwachangu m`mabedi amasamba okonzedwa bwino.

Chipangizo chabwino chookera ndi kandodo ka dibula, chomwe chili chamtengo chozungulira chogwiritsidwa ntchito popangira mayenje ang`onoang`ono pa nthaka amene tingamaokelemo mbeu zathu. Ndodo ya dibula ikuyenera kukhala yosongoka kumapeto ndi yokulirapo kusiyana ndi mbeu yathu, koma chitha kupangidwa ndi zogwilira zosiyanasiyana monga changati thabwa, chowoneka ngati T kapena chopindika. Kwa malo akulu olima ndodo ya dibula yayitali komanso yokhala ndi choyezera ndi yabwino. Alimi aminda ya masamba yapakhomo angathe kugwiritsa ntchito ka ndodo ka dibula kosapindika ka 20 – 25cm, ka thabwa kogwilira kake kutaikidwa ka mpango kuti kasamaterere. 

Choyamba dusitsani mosamala ndodo ya dibula pa bulangete, onetsetsetsani kuti musagwetsere zinyalala pa phando. Kenako lowetsani ndodo ya dibula mu nthaka kuti mupange dzenje pa mulingo ofunika. Pamene mukuokera mbeu, samalani ndipo muonetsetse kuti palibe mipata ya mpweya yomwe yatsala pansi pa mizu ya mbeu zomwe zingathe kuyambitsa kusakula ngakhale kufa kumene. 

Ikani mbeu pa mulingo oyenera ndipo kenako lowetsani ndodo ya dibula kachikena pa kona ya 45˚, moyandikana ndi mbeu, kankhirani dothi mosamala mizu ya mbeu Izi zimathandizira kuti mbeu iyime bwino komanso zimaonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya mozungulira mizu 

Dzenje laling`ono ya ndodo ya dibula mu kompositi moyandikana ndi mbeu itha kutsekedwa ndi phazi kapena dzanja kapena kusiyapo kuti pakwilirike pokha