A) Bitiruti – Njira ya Kompositi oika Pamwamba 

Bitiruti amatengedwa kukhala gwero la zakudya zopatsa thanzi ndi anthu odziwa za madyedwe, wokhala ndi kuchuluka kwa muyeso wochotsa zosafunika mthupi. Masamba angathenso kudyedwa monga sipinachi, kubweretsa kagwiritsidwe ntchito ka njira zosiyanasiyana ku mbeu zomwe ndi zosiyaniranatu ndi nthawi zimene masamba ena a gulu la masamba obiriwira amakhala kuti sakupezeka kwa ka nthawi kochepa m’munda. 

Bitiruti ali ndi nyengo yofanana ya kalimidwe ndi kaloti, makamaka pakati pa mulingo wa katenthedwe ka 15-24 oC, koma angathenso kukhala nyengo yotentha kufikira muyeso wa mpaka 35 oC. Bzalani bitiruti kuchokera nyengo ya kasupe kupyolera mu nyengo ya dzinja. 

Kabzalidwe 

Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani mizere yokhala iwiri pa mpata wotalikana wa 20cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo. M’munda waung’ono, kulitsani bande wanu kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mugwiritse tchito bwino malo anu ochepa. 

Kuyala zingwe kuti tibzale 

Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zokhalitsa ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande la manyowa oika pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamula ndi kuziponya pansi. 

Kusunta Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu pokakhira m’munsi pa mpata wa 25cm wa bande lobzalira, kuti muonetsetse kuti palibe bulangeti lomwe laola. Likhoza kupangitsa nthaka kukhala wopanda naitulojeni kupangitsa kukolola zochepa. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kukonza Nthaka ya Mnchere 

Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse. 

Kompositi oika Pamwamba 

Bitiruti amadya mochepa choncho thirani muyeso wa 2cm wa kompositi oika pamwamba, pamwamba pa bande wa muyeso wa 25cm kupita m’mbali. Sizoyenerera kukwilira kompositi mu nthaka. Dongosolo limeneri la kompositi oika pamwamba ndiye kutsatira chimodzimodzi zimene Yehova wa chilengedwe chonse wationetsa ife kuyambira pachiyambi cha nthawi zonse, pamene adapanga zomera kudya kuchokera m’mwamba. 

Kupanga Ngalande ndi Kubzala Mbeu 

Dindani kangalande ka muyeso wa 2cm kuzika pansi pa bande wokonzedwa wa muyeso wa 25cm m’mbali ndipo bwerezani pa mzere wa 20cm uliwonse cha kumunsi kwa malo otsetsereka. Bzalani mbeu ya bitiruti kupita pansi pa muyeso wa 2cm ndiponso 5cm kutalikana. Ndizofunikira kupeza mbeu yabwino ya bitiruti kulumikizana ndi kompositi, choncho kwirirani mbeu powaza ngalande ndi kutsendera nthaka pang’ono. Zikamela, patulirani Bitiruti mpaka pa muyeso wotalikana wa 10cm pakati pa zomera. 

Musaike bulangeti pamwamba pa bande kufikira zitamera, pamenepo ndi pamene bulangeti libweretsedwe pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm kuti ilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Mbande 

Bitiruti angathe kubzalidwanso kuchokera ku mbande, kupereka changu komanso kuphweka kwa kakulidwe kofanana. Mu njira imeneyi ikani kompositi ndipo gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi chizindikiro cha kazikidwe ka pansi, izikeni kupyola bulangeti ndi kuizika mu bande wa kompositi pa muyeso wa kupita pansi woyenera. Kakhirani maenje amenewa mkati pa muyeso wa 10cm pakati pa zomera ndi 20cm pakati pa mizere. 

Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. 

Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. 

B) Bitiruti – Njira ya Manyowa 

Bitiruti amatengedwa kukhala gwero lochokera zakudya zopatsa thanzi ndi anthu odziwa za madyedwe, wokhala ndi muyeso wochuluka wochotsa zosafunikira mthupi. Masamba angathenso kudyedwa monga sipinachi, kubweretsa kagwiritsidwe ntchito ka njira zosiyanasiyana ku mbeu zomwe ndi zosiyaniranatu ndi nthawi zimene masamba ena a gulu la masamba obiriwira amakhala kuti sakupezeka kwa ka nthawi kochepa m’munda. 

Bitiruti ali ndi nyengo yofanana ya kalimidwe ndi kaloti, makamaka pakati pa mulingo wa katenthedwe ka 15-24 oC, koma angathenso kukhala nyengo yotentha kufikira muyeso wa mpaka 35 oC. Bzalani bitiruti kuchokera nyengo ya kasupe kupyolera mu nyengo ya dzinja. 

Kabzalidwe 

Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani mizere yokhala iwiri pa mpata wotalikirana wa 20cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo. M’munda waung’ono, kulitsani beseni kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mugwiritse bwino malo anu ochepa. 

Kuyala zingwe kuti mubzale mmabeseni osaya 

Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zokhalitsa ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange beseni losaya kuzika pansi. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu pa muyeso wa 10cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira, kuti nthaka ikhale poyera. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere. 

Kukonza Mabeseni Osaya 

Chifukwa chakufupikana kwa kutalikana kwa muyeso mzere wa 20cm, ndikovuta kukumba ngalande ya mbeu za mizere yaing’ono ya mbeu zimenezi. M’malo mwake konzani beseni losaya kupita pansi pokumba nthaka pa muyeso wa 5cm pakati pa zingwe ndi mbali ya kumunsi kwa malo otsetsereka. 

Kukonza Nthaka ya Mnchere 

Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse. 

Manyowa 

Wazani mulingo wa 1cm wa manyowa pansi pa beseni losaya ndipo salazani bwino lomwe ndi leki. 

Kuzika kwa mbeu ndi dothi lolekanitsira 

Kwirirani manyowa ndi nthaka kuti ikhalenso yofanana. Izi zipangitsa kusiyana bwino kwa mpata pakati pa manyowa ndi mbeu zomwe ndi zoyenera kupewa kupsa kwa mbeu. 

Kupanga Tingalande ndi kubzala Mbeu 

Dindani kangalande ka muyeso wa 2cm kuzika pansi pa beseni wokonzedwa ndipo bwerezani pa mzere wa 20cm uliwonse cha kumunsi kwa malo otsetsereka. Bzalani mbeu ya bitiruti kupita pansi pa muyeso wa 2cm ndiponso 5cm kutalikana. Ndizofunikira kuti mbeu yabwino ya bitiruti ilumikizane ndi kompositi, choncho kwirirani mbeu powaza ngalande ndi kutsendera nthaka pang’ono. Zikamela, patulirani Bitiruti munsi mpaka pa muyeso wotalikana wa 10cm pakati pa zomera. 

Musaike bulangeti pamwamba pa bande kufikira zitamera, pamenepo ndi pamene bulangeti libweretsedwe pa matsinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Mbande 

Ngati mukubzala mbande za Bitiruti, kwirirani mbande ndi nthaka yochokera kumunsi kwa mulu wanu kusalaza beseni ndi kubwezeretsa bulangeti lokhuthala la muyeso wa 2.5cm. gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe ka pansi, izikeni ndodoyi kupyola bulangeti ndi kuizika pa beseni lokonzedwa, pa mulingo woyenera wokhala ndi muyeso wa 10cm kutalikana kwa zomera ndi 20cm kutalikana kwa mizere. 

Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi.