6.3.5 Mbatata ya Kachewere – Njira ya Kompositi/Manyowa 

Mbatata ya kachewere ndi mbeu yaikulu yachinayi pa dziko lonse kuyambira ku chimanga, tirigu ndi mpunga. Mbatata iri ndi ufa wochuluka kufikira pa muyeso wa 17% kupangitsa kuti ikhale chakudya chofunikira kwa anthu ambiri. Ngakhale irinso ndi vitamini B6 komanso C, kumbali yopatsa thanzi siingapose masamba ena. 

Mbatata ya kachewere imabzalidwa kozizira kuchokera 7℃ mpaka 30℃ koma ndi kaziziridwe kabwino ka pakati pa 15℃ mpaka 25℃. Kum`mwera kwa Afirika Madera ogwa mvula nthawi ya chilimwe, ndikoyenera kubzala mu August mpaka January. Imaikidwa mu gulu la mbeu za nyengo yozizira chifukwa pamene kwatentha kupitilira 27℃ imasiya kukula mitsitsi yake mbatata simafufuma. 

Kabzalidwe 

Mbatata imabzalidwa motalikirana 30cm pakati pa zomera ndi motalikirana 75cm pakati pa mizere pa malo opanda mabedi kapena pamabedi okhazikika okwera. 

Kuyala Zingwe za tingalande 

Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo choyang’anizana nacho cha mbali yina. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangete la Mulungu 

Sunthani bulangete la Mulungu pa muyeso wa 30cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira, kuti nthaka ikhale poyera. 

Kumasula Nthaka 

Ngati nthaka yanu ndi yogogomezeka, mbatata yanu ipatseni mpata ochita bwino pomasula nthaka pa mnzere wa 75cm ulionse ndi 30cm kuya koma pokhala kuti tibzala pa 15cm kuya izi sizingakhale zofunika. 

Tingalande 

Konzani ngalande yokuya 15cm kupita pansi, pa mzere uli onse wa 75cm, samalani posataya dothi kutali kwambiri ku mbali ya kumunsi ya dothi lounjikidwa. 

Kukonza Nthaka ya Mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kuti ikhale ya chonde chofikirika thirani supuni imodzi ya phulusa, ufa wa mafupa kapena supuni imodzi ya laimu, pa muyeso wa 60cm iri yonse pa mizere yobzalira. 

Manyowa/Kompositi Wochepa 

Wazani kompositi kapena manyowa wokwanira muyeso wa 500ml pa mita iri yonse kenako kwirirani ndi 3cm ya dothi kuti mukhale ndi muyezo wobzalira wa 10cm. 

Kubzala Mbeu ya Mbatata 

Mbatata amabzalidwa kuchokera ku mbatata yaing’onoing’ono yake yosagwidwa ndi matenda kapena kuchokera ku mbatata yaikulu yoduladula yokhala ndi malo ophukira atatu kapena awiri pa chidutswa chiri chonse. Bzalani mbeu ya mbatata motalikirana ndi 30cm mu ngalande ndipo kwirirani ngalande yonse. 

Bulangete la Mulungu 

Kukwezera sikofunika kuti mbatata afufume koma bulangete labwino ndilo lofunika. Siyani mpata wa 5cm pamwamba pa dzenje la phando kuti ithe kumera. Ikamera ikani bulangete lokhuthala pakati pa 5cm mpaka 10cm, kuti tipewe mitsitsi ya mbatata yanthu kubiriwira komanso kuti isazike pansi kwambiri. 

Kukolora 

Bulangete likakhala lokhuthala bwino, ndi kosavuta kuti mukolore mbatata ndipo kusokoneza nthaka kumakhala kochepa. Gwiritsani ntchito foloko kutukula mwamba mbatata pang`onopang`ono yomwe ingapezeke pafupi kwambiri ndi pansi pa nthaka chifukwa cha chinyontho chochokera ku Bulangete la Mulungu.