Mu buku la genesis mutu 1, timawerenga kuti Mulungu wathu, Mlengi ndi Wodabwitsa adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zokhala m`menemo ndipo adawona kuti zidali zabwino. Adalenga dzuwa limene zamoyo zonse zimadalira mphamvu yake. Adalenga mpweya, madzi ndi zonse zofunika m`menemo ku zolengedwa zonse. Adalenga nthaka ndi zamoyo zonse zokhala m`menemo zowoneka ndi zosawoneka. Adalenganso zomera zobala zipatso monga mwa mtundu wake ndipo analenganso nyama zosiyanasiyana ndipo pomaliza adalenga munthu. Zonse zomwe adazilenga zinali zabwino ndi zopindulitsa. Palibe chimene Mulungu adachilenga chimene chinali chopanda pake pakuti zamoyo zonse modalirana pamodzi ndi zimene zimapeleka tanthauzo ku moyo wa munthu mpaka lero.
Nkhani yina yopatsa chidwi ikupezeka mu buku la Genesis mutu 2, pamene Mulungu adawapangira Adamu ndi Hava munda wa zakudya ku m`mawa kwa Edene.
Mulungu adalenga munda woyamba namuika Adamu m`mundamo kuti aulime ndi kuuyang`anira, Mulungu mwini ngati woyamba ndi Mlimi wamkulu adaphunzitsa Adamu china chiri chonse zimene amayenera kudziwa pa zolengedwa zake komanso m`mene angalimire ndikusamalira munda wa Edene.
Gen 2:8 “Ndipo Yehova Mulungu adabzala m`munda ku Edene cha kum`mawa momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo, 9 Ndipo Yehova Mulungu adameretsa m`nthaka mitengo yonse yokoma m`manso ndi yabwino kudya, ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoyipa.
15 Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo namuika iye m`munda wa Edene kuti aulime nauyang`anire”
Kodi izi ndi zofunika bwanji ku kalimidwe ka masamba? Zonse ndi zofunika!!!
Ngati timvetsetsa kuti Mulungu pachiyambi adalenga za moyo zonse ndi zonse zothangatira moyo ndi pamene tingazindikire kuti iye ali ndi ndondomeko ya m`mene tingagwiritsire ntchito zinthu zonse zomwe adazilenga moyenerera.
Monga tikudziwa kuti munthu oyenera kuphunzitsa m`mene tingagwiritsire ntchito bwino chinthu ndiye wochipanga chinthucho. Izi ziri chimodzimodzi ndi ulimi. Tikuyenera kubwera kwa Mwini chilengedwe, ndikuyang`ana m`mene zomera anazipangira kuti zizitha kukula pamalo amene izo zinapangidwira ndipo tikuyenera kudzichepetsa ndi kuphunzira kuchokera kwa Mlimi wamkulu yemwe ndi Mulungu. Mu chilengedwe chake, chilengedwe cha Mulungu chikuonetsera zonsezi mmunda wa Mulungu cha kum`mawa kwa Edene umene satembenuza nthaka, nthawi zonse nthaka imakhala yophimbidwa ndi yokutidwa pamwamba pake ndi magawo osiyanasiyana a zinthu zomela ngati; Masamba, nthambi za mtengo, Zipatso komanso manyowa. Choyenera kuchita ndiko kutsatira m`mene Mlengi watisonyezera m`mene amachita kuyambira pachiyambi.
Molingana ndi m`mene taonera, tikuyenera kutsatira bwino zonse m`mene Mlengi wathu wationetsa kuti tikuyenera kungokhudza nthaka mochepa chabe ndikuiphimba (2.5cm) komanso kumachita kasinthasintha wa mbeu.
Nkhaniyi ndi yoposa ulimi wamakono…. Ndi cholinga cha Mulungu kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Iye ndi chilengedwe ndipo amatha kubwera kudzayenda ndi kuyankhula ndi Adam nthawi yakupendeka kwa dzuwa kwa tsiku.
Chifukwa chiyani Mlengi wa dziko ndi zinthu zonse amachita izi?
Adatero chifukwa amakonda munthu ndipo cholinga chake chidali chakuti munthuyo adzichita molingana ndi chifuniro chake, Ndipo pa zolengedwa zonse mwayiwu udagwera munthu basi.
Pamene munthu adachimwa pakudya chipatso cha mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa zomwe ndi zosemphana ndi lamulo la Mlengi wake, adaphwanya pangano la ubale wawo ndipo zotsatira zake Adamu adathamangitsidwa m`munda ndipo anakanthidwa ndi thembelero lakudya thukuta lake komanso kumera kwa tchire pa nthaka. Palibe mwa mavuto amene adalipo mu ulimi munthu asadachimwe.
Komabe, chowawa kwambiri chomwe chidachitika ndi chakuti tchimo lidalekanitsa mtundu wa anthu ndi Mlengi wawo ndipo palibenso mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Iye, chomwe chidali cholinga cha Mulungu.
Nkhani yopatsa chiyembekezo ndi yakuti Yesu adabwera kudzachotsa ndi kumphanya thembelero lirilonse kwa munthu aliyense amene akhulipilira Iye ndikumupatsa mphamvu yokhalanso mwana wa Mulungu ndi kuyanjanitsidwanso ndi Atate.
Akolose 1 “ 15Amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobwadwa woyamba wa chilengedwe chonse, 16 Pakuti mwa iye zinalengedwa zonse za mwamba ndi zapadziko, zooneka ndi zosaonekazo kapena mipando ya chifumu kapena maukulu, kapena maulamuliro; Zinthu zonse, zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye. 17 Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye, 18 Ndipo iye ali mutu wathupi Eklesiayo, ndiye chiyambi wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa kuti akhale iye mwa zonse woyambayamba. 19 Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye chidzalo chonse chikhalire; 20 Mwa Iyenso, kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake, mwa Iyetu, kapena zapadziko kapena za m’mwamba.”
Yesu amene akutchedwa Adamu wachiwiri watipangira njira yolowanso m`munda muja wa kum`mawa kwa Edene pakutichotsera chiletso ndi thembelero ndikutiyika m`chiyanjano cha moyo ndi Mlengi wathu. Izi ndi zimene zikuyenera kumachitika m`minda yanthu onse ya Kulima mu Njira ya Mulungu, tikatero tidzakhala mu mgwirizano wa tanthauzo ndi Ambuye wathu pamene adzapereke madalitso osefukira pa minda yathu.
Buku iri la Kulima za Masamba mu Njira ya Mulungu ndi chipangizo chimene chikutionetsera njiri za ulimi zomwe zaunikiridwa kuti ndi zosavuta zimene zikhoza kukwanitsidwa ndi anthu onse ngakhale osauka.
Kulima mu Njira ya Mulungu sizaluso lamakono lokha komatu dongosolo loyenera la m’baibulo, kuyang’anira kwabwino ndi upangiri omwe monga yankho mu nkhani zonse za ulimi, kukonzekeretsa osowa kuchoka mu uphawi ndi zomwe Mulungu waika m`manja mwawo zomwe zikuvumbulutsa lonjezo lake la moyo ochuluka.
Mau a Mulungu ali pa mwamba pa zonse pakubooleza m’miyoyo ya anthu ndipo ndikukulimbikitsani kukagwiritsa ntchito moyenera mifungulo isanu ndi umodzi ya Kulima mu Njira ya Mulungu yopezeka m`makanema ndi m’buku la Mphunzitsi pomwe tikuphunzitsa za kulima masamba mu Njila ya Mulungu.
“Gwirani ntchito sichifukwa cha chakudya chimene chatayika koma chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro “Yohane 6:27.
“Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza mwaine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupilira Ine sadzamva lunzu nthawi zonse.” Yohane 6:35.
Mfungulo za Kuyang’anira ndi zofunikanso kwambiri monga kuchita zinthu mu Nthawi yake, Mwapamwamba kwambiri, Osaononga ndi Zipatso za Mzimu Woyera, ndipo musazengereze zimenezi ndi zofunika.
Mfungulo za Upangiri ndi monga kusatembenuza nthaka, kumphimba nthaka yonse ndi bulangete la Mulungu, kulimbikitsa kasinthasintha wa mbeu, kudzala mbeu za kapitiriza ndi mbeu zomphimba nthaka.
Cholinga chachikulu cha Mulungu chinali choti munthu akhale pa ubale wabwino ndi Iye, ndikutsata njira zake zonse. Kudzera mu Kulima mu Njira ya Mulungu ife tikulimbikitsa anthu kuti asatsate njira koma a Atate, Mlengi ndi Mlimi wamkulu, ndipo chofunika ndi chakuti tisunge mfundo zake monga “Kuchita zomwe taona Atate wathu akupanga”.