Kompositi ndi njira ina yolowa m`malo mwa fetereza yomwe simangobweretsa chonde mnthaka kokha komanso kuthandiza kubwezeretsa zachilengedwe za moyo zopezeka mkati mwa dothi. 

2 Akorinto 9:8 "Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsa chisomo chonse kwa inu, kuti inu pokhala nacho chikwaniro chonse m`zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire ku ntchito yonse yabwino.” 

Mau a Mulungu ndi owona, wapanga njira kwa aliyense kuti akhale ndi zothira mu nthaka monga kompositi. Pothira kompositi wabwino mu nthaka, aliminso akhoza kupeza phindu lofanana kapenanso lochuluka akalima kwa nthawi yaitali poyerekeza ndi kugwiritsa ntchito fetereza. 

Komositi ndi chiyani? 

Kompositi mwachidule ndi zoola zosiyanasiyana zomwe zanyenyedwa ndi tizilombo ting`onoting`ono makamaka bakiteriya ndi fangasi. Pofuna kuti kompositi wathu akhale wa pamwamba kwambir tikuyenera kukhazikika ku zipangizo zopangira kompositi ndikupanga mwa ‘’pamwamba kwambiri’’. Tikuyamikira kuti mulu wa kompositi ukuyenera kupangidwa pa (2m) mulitali (2m) mulifupi ndi (2m) kupita m`mwamba kuchoka pansi. Uwu ndi mulingo wochepa wokwana kwa munthu m`modzi wogwira ntchito maora ochepa, pomwe mulola nyengo yokwana bwino ya mkati mwa mulu wa kompositi wanu. Zotsatira zakachulukidwe kake kadzakhala (3.5m³) womwe ndi wokwanira pa khomo lalikulu la munda wazakudya pa chaka. 

Ngati simukufuna manyowa ochuluka, mukhoza kuchepetsa mulu wanu wopangira manyowa pa mulingo wa (1.5m) mulitali (1.5m) mulifupi ndi (1.5m) kuchokera pansi kupita m`mwamba. Pamene akulu akulu amangophatikiza milu ya kompositi ya pa mulingo wa (2m) mulifupi ndi 2m kuchokera pansi kupita mwamba, mulitali amangopitiliza mpaka pomwe akufuna. 

Nthawi yopangira Kompositi 

Yambani kusonkhanitsa zinthu zopangira manyowa mu nthawi yomwe kuli zinthu zobiliwira zambiri mozungulira mdera lanu, chigawo cha ku m`mwera kwa Afrika imakhala mu Januwale kapena mu febuluwale, cholinga choti pakhale nthawi yokwanira kuti manyowa avundilane isanafike nyengo yobzala yomwe ikubwera 

Zipangizo zopangira kompositi 

Kompositi amapangidwa ndi zinthu zinayi, naitulojeni, zobiliwira, zouma ndi zatinkhuni. Masamba amachita bwino ndi kompositi wochuluka ma bakiteria kusiyana ndi ochuluka ma fangasi omwe amafunikira ku mbeu za ku munda, chomcho tikuyenera kuchepetsa mulingo wa zatinkhuni mpaka 10% ndi kuonjezera zouma zathu mpaka 35% milingo ina yonse imakhala chimodzimodzi. Izi zimachepetsa mulingo wa kaboni ku naitulogeni ndikupangitsa manyowa athu kukhala abwino, mabakiteliiya amapezekamo ambiri mkati mwake. 

a) Naitolojeni 

Naitolojeni ndi mafuta ofunika pa mulu wa kompositi ndipo amatakasa ma bakiteliya kuti agwire ntchito yake. M`mene tingapezemo Naitolojeni ochuluka ndi mundowe ndipo zikuyenera kupanga 10% ya mulu kapena matumba 15 andowe a ma 50kg. Gwiritsani ntchito ndowe zakumene (zatsopano) zimene mungathe kupeza. Ngati mdera lanu kulibe ndowe ndiye mutha kugwiritsa ntchito 4 kubiki mita ya nyemba ndiye muchepetse zobiliwira ndi zatinkhuni/ zouma mwandondomeko yake. 

b) Zobiliwira 

Masamba obiliwira mumapezeka shuga wambiri, amene ndi ofunikira kuti kompositi akhale wapamwamba. Zobiriwira zikuyenera kupanga 45% yamulu ndipo zikuyenera kugwiritsidwa ntchito mumasiku atatu ndi anayi kupanda apo shuga azitha kupita ku sitachi. Tengani zinthu zobiriwira mosapitilira 8 kubiki mita zopangidwa ndi masamba, kapinga, tchile, masamba okhalitsa kapena nthambi za mitengo ing`onoing`ono. 

c) Zatinkhuni 

Zinthu zouma kuchulukana kwa fangai m`manyowa chifukwa zimadyeka mwa pang`onopang`ono ndipo izi zimathandizira kuti m`manyowa muzipita mpweya. Tengani zinthu zolimba mosapitilira 2m³ kuti mupange 10% ya manyowa kugwiritsa ntchito zikonyo za chimanga, mapesi, nthambi za mitengo, zipalo zamatabwa. 

d) Zouma 

Zinthu zouma zimachulukitsa mulu ndi Kaboni pa kompositi wathu ndipo zikuyenera kupanga 35% ya mulu wa komositi. Tolerani zithu zouma mosapitilira 8m³, zopangidwa ndi udzu ofolera nyumba, masamba kapena tchile lokhalitsa. 

Mwachidule, zinthu zopangira Kompositi:15×50kg ya matumba a ndowe; 8 kubiki mita zobiriwira (45%), 2 kubiki mita zatinkhuni (10%) ndi 8 kubiki mita zouma (35%). 

Kuonjezera thumba la kompositi omwe anapangidwa kale kapena manyowa ochokera ku zinthu za mnkhalango zingathe kukhala zopindula popanga kompositi wanu ndi tizilombo tachilengedwe. 

Zipangizo zikuyenera kuikidwa mosiyana mpaka nthawi imene china chilichonse chakwanira. Kuonkhanitsa zinthu zokwanira kuti mupangire kompositi zimatenga nthawi, nde zimafunika dongosolo lokwanira. Alimi olima mu Njira ya Mulungu akuyenera kukhala mu magulu a anthu asanu kuti azipemphera, kuphunzitsana ndi kuthandizana wina ndi nzake. Ngati magulu amenewa angakumane pa modzi mu nthawi yomwe kuli zinthu zobiriwira zochuluka, angathe kuchitira limodzi milu ya kompositi mu dera mwawo machiyanjano ndi mgwirizano. 

Kumanga mulu wa kompositi 

Konzani chinthu cha mbali zinayi chokhala ndi mbali ziwiri zofanana ndi mamita awiri mulitali pogwiritsa ntchito mitengo isanu ndi umodzi yotalika mamita okwana awiri. Muyenera kukhala ndi mitengo yotalika 2.6m yomwe mungathe kuizika pansi 60cm. Mukamamanga kompositi onetsetsa kuti mukupanga ndi manambala azipangizo olondola. Njira yake yophweka ndi kumanga kugwiritsa ntchito magawo anayi a zopangira kompositi. Pamene mukumanga gawo iliyonse nyowetsani zopangira komposit m`madzi musanaziike pa mulu, cholinga choti munyowetse zigawo zonse mwadongosolo. Kunyowetsa kwabwino koyambirira kukutanthauza kuti muzizangoonjezera madzi mwina kamodzi kapena kawiri munthawi yotembenuza manyowa athu. 

Yambani ndi 5cm zatinkhuni, kenako 15cm zouma, kenako 20cm zobiriwira, kenako matumba awiri wonyowa bwino, ndowe zatsopano (zosakhalitsa) pamwamba pake. Chithunzi chiri munsichi ndi chionetsero chabe mukhoza kukhala ndi magao ambiri kuposera apa, pitilizani kuika zipangizo kufikira mulu ukwane 2 mita kuchokera pansi kupita mmwamba. 

Kutembenuza mulu 

Mumasiku atatu, mulu wa kompositi udzakhala kuti watentha ndipo udzafunika kutembenuzidwa, kusakaniza kompositi pamalo omwe pakumana 2m ndi 2m ina ndi njira yabwino yochitira izi, gwiritsani ntchito foloko kapena nkhasu. Kutembenuza kumabweretsa kutentha kapena kuzizira kwabwino, kumasakaniza zinthu zonse, kumabweretsa zinthu zamkati kunja ndi za kunja mkati, kumapereka mpweya wabwino ndi kuona komanso kuonjezera chinyontho. Ngati mulu sukutembenuzidwa tizirombo tofunika timafamo, umanunkha komanso kompositi yake simakhala yabwino. 

Kutenthedwe kapena kazizilidwe 

Mulu wa Kompositi umatetha kwambiri mofulumira chifukwa cha mabakiteliya omwe amakhala akuvunditsa zinthu pa mulu paja. Katenthedwe kapena kazizilidwe kabwino kakuyenera kukhala pakati pa 55 mpaka 68 cholinga choti tiphe mbeu komanso tizilombo tosafunikira tomwe timayambitsa matenda. Ngati simutembenuza manyowa anu, katenthedwe kapena kazizilidwe katha kupitilira 70 mosavuta, komwe ndi kutentha kwambiri, kumapha tizilombo tofunikira, komanso kuotcha ndi kuononga kaboni. 

Njira yabwino yoyezera kutenthedwa kapena kuzizilidwa ndi kugwiritsa ntchito chida choyezera katenthedwe kapena kazizilidwe. Tembenuzani manyowa katenthedwe kapena kazizilidwe kasanafike 68. Njira yophweka ndi kugwiritsa ntchito chithu chachitsulo chokwana 8mm. Mukachizika kwa maminitsi ochepa, yesani ngati mungathe kuchigwira kwa masekanzi okwana asanu. Ngati simungathe ndiye kuti mutha kutembenuzanso. 

Njira yabwino yosavuta yamatembenuzidwe ndi iyi; tembenuzani pakatha masiku atatu alionse koyambilira, izi muchite kokwanira katatu, kenako pakatha masiku khumi alionse, apa mutembeza kawiri kapena katatu. 

Mulu wa Kompositi umazizira mukangotembenuza kumene kenako umatenthanso kufikira kutembenuza kachikena. Izi zimachitika kufikira naitulogeni yense atagwiritsidwa ntchito. Ngati mungatsatire ndondomeko ya mulingo wa zipangizo wa matumba 15 andowe, zikatero kompositi adzatenthedwa mokwanira bwino komanso adzavundirana mokwaniranso ndipo adzakhala atatheka ndi kuzizira patatha masabata 6 mpaka 8. 

Kusakaniza 

Pamene mukutembenuza, sakanizani zipangizo zonse mwadongosolo kubweretsa za kunja mkati cholinga choti zilandire kutentha kochuluka ndi zinthu zamkati zipite kunja cholinga choti zinthu zonse zithe kufunditsidwa ndi mabaketiliya 

Mulingo wachinyontho 

Ndikwabwino kuyesera kuona ngati kompositi ali ndi chinyontho chokwanira, ngati chinyontho chambiri chikuthawa ngati nthunzi ndikofunikira kubwezeretsa. Yeserani kusunga 50% ya mulingo wa chinyontho cha kompositi wanu. 

Mutha kuyesa izi pamene mukutembenuza kompositi, powafinya m`manja mwanu. Ngati madzi angatuluke, ndiye kuti yanyowa kwambiri, ngati madzi satuluka koma potambasula dzanja sakuumbana pamodzi, ndiye kuti auma kwambiri, onjezerani madzi, ngati pofinya madzi alionse sadatuluke ndipo potambasula dzanja ndiyoumbanabe ndiye kuti ikuyandikira ku mulingo wa chinyontho woyenera wa 50% 

Pamwamba pa Kompositi pakhale potsetseleka ndipo ikani udzu kapena matumba oikira chimanga pamwamba pake cholinga choti madzi a mvula asaonjezere kunyowetsa kompositi, zimene zingapangitse kuti mulu wa kompositi uzizire kwambiri.  

Kumalizika 

Pakatha miyezi iwiri mukutembenuza mulu wanu Kompositi amakhla kuti watheka komabe mumusiye musanamugwiritse ntchito kwa miyezi ina inai kuti amalizike. Sukufunikira kuti mutembenuzenso koma sungani panthunzi kapena muvundikire ndi chinthu chopita mphepo kapena udzu cholinga choti asaume 

Tisavindikire kompositi ndi chinthu chosapita mpweya monga pepala ya pulasitiki chifukwa tizilombo tamoyo timabanika. 

Mukamaliza, kompositi wanu akuyenera kukhala wa mtundu wa kuda mwakhakhi, kununkhira bwino, wosachedwa kunyenyeka kapena kumbwera ndipo muzitha kuona tizingwe tamafangasi. 

Akamalizika, kompositi atha kusungidwa mpaka kwa nthawi yaitali asadachoke chonde. Pa nthawi imene kompositi adzakhala mu chonde chokhazikika. 

Kagwiritsidwe ntchito ka kompositi 

Kompositi ndi zomwe timathira m`munda, tikuyenera kumaona munda ulionse alimi omwe tawaphunzitsa akugwiritsa ntchito kompositi ndi kukhulupirika ndi zomwe Mulungu mukukwanira kwake mu zonse waika mmanja mwathu. 

Kompositi angagwiritsidwe ntchito ngati othira pamwamba, mmapando kapena mtingalande. Kompositi wabwino amapangitsa kuti zokolora zikhale zochuluka ndipo amapangidwa pa mtengo otchipa ndi masiku ochepa kusonkhanitsa zipangizo ndi kutembenuza mulu ka sanu ndi kamodzi basi. Mwayi opindula ngati mlimi wa masamba pochepetsa mtengo wa zomwe tingalowetse ndi kulima mbeu zopatsa nthanzi zimatengera ndi zomwe tathira mmapando athu.