A) Anyenzi – Njira ya Kompositi oika Pamwamba
Anyenzi ndi odziwika bwino pa nkhani yowonjezeredwa mu ndiwo ku Afirika. Ali ndi vitamini C ochuluka komanso foleti ndipo alinso ndi peputayidi wambiri yemwe amathandiza pogonjetsa matenda akusalimba kwa mafupa.
Anyenzi amakonda kubzalidwa m`munyengo zozizira za pakati pa 12℃ – 25℃ ndipo amachita bwino kwambiri kozizira kusiyana ndi kotentha. Anyenzi kuti akhwime amatenga nthawi yaitali (kuchokera miyezi 4 mpaka 7) kotero “m’munda waung`ono wa pakhomo” ndi mbeu zabwino kuzibzala miyezi imeneyo, kuphatikizanso anyenzi wotsekemera. Bzalani anyenzi kuchokera ku mapeto a chilimwe mpaka dzinja ndipo kumbukirani kuti amafuna madzi ambiri akayamba kubereka masamba, ndiye “m’madera ogwa mvula nthawi ya chilimwe ngati mvula sikugwa”, onetsetsani kuti muli ndi njira yabwino yakanthiriridwe ka madzi.
Kabzalidwe
Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani mizere yokhala iwiri pa mpata wotalikana wa 20cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo. Munda waung’ono wapakhomo, kulitsani bande lanu kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa.
Kuyala Zingwe Zobzalira
Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo choyang’’anizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande wothira kompositi wa pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi.
Kusuntha Bulangete la Mulungu
Sunthani Bulangete la Mulungu m’munsi mwa bande wobzalira, muonetsetse kuti silidakwiriridwe ndi pang’ono pomwe. Ngati mungakwirire bulangete lomwe silidaole, lingathe kupangitsa kuti nthaka ikhale ndi nthawi yopanga naitulojeni osafunikira ndi kuchepetsa zokolora.
Kumasula Nthaka
Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere.
Kukonza Nthaka ya Mchere
Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse.
Kompositi oika Pamwamba
Anyezi amadya pang`ono ndiye ikani muyeso wochepa wa 2cm wa kompositi oika pamwamba pa bande wotalika 25cm m’mbali. Sibwino kukwilira kompositi mu nthaka. Njira imeneyi ya kathiridwe ka kompositi wa pamwamba ndi kutsatira zomwe Ambuye wa chilengedwe chonse adaonetsa kwa ife kuchokera kumayambiriro a nthawi zonse, pamene iye adapanga kuti zomera zizidya kuchokera pamwamba.
Kukumba tingalande ndi Kubzala Mbeu
Dindani kangalande ka 2cm kuya pansi pa bande lopangidwa la muyeso wa 25cm kakulidwe ka m’mbari ndipo bwerezaninso zimenezi mu mzere wina wotsatira wa 20cm wa m’munsi. Bzalani mbeu za anyenzi pa muyeso wa 2cm kupita pansi ndi muyeso wotalikirana ndi 5cm. Ndizofunikira kwambiri kuti mbeu yabwino ya anyezi ikhudzane ndi kompositi. Kotero phimbirani mbeu powaza kompositi pang`onopang`ono kufikira pamwamba kenako tsindirani kompositi poyenda pamwamba pa mbali yotambalala ya thabwa. Pamene wamera, patulirani anyezi pa muyeso wa 10cm wa pakati pa zomera ndipo gwiritsani ntchito anyezi opatulidwa mmalo ena. Musaike bulangete pamwamba pa mabande obzalidwa kufikira mbeu zitamera, ndi pamene mungathe kuika bulangete pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangete liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm m’mipata yoyendamo kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.
Mbande za Anyezi
Anyezi amachita bwino kwambiri akabzalidwa mochita kuokeredwa. Pakatha masabata 7 mpaka 8, mbeu zofesedwa zidzakhala zitafika kakulidwe ka muyeso wonenepa wa cholembera cha mkala mu nazale ndipo zikuyenera kukawokeledwa. Ikani bulangete lalikulu lokhuthala kufikira 2.5cm pamwamba pa kompositi oika pamwamba kenako gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe ka pansi, izikeni ndodoyi kupyola bulangeti ndi kuizika pa bande wa kompositi wa pamwamba, pa mulingo woyenera ndi muyeso wa 10cm kutalikana kwa zomera ndi 20cm kutalikana kwa mizere. Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi.
Kukolora Anyezi
Anyenzi amatenga nthawi yaitali kuti akhwime (miyezi 4 mpaka 7) ndipo akuyenera ku umitsidwa bwino musadamusunge. Choyamba pamene tsamba layamba chikasu pindani masamba, musawakhodzore zomwe zingapangitse kuti aume mwachangu. Mukamudzula, musungeni mu mnthunzi, pouma, malo opita mphepo bwino. Gwiritsani ntchito koyambirira anyezi yense amene waonongeka ndipo mudziyang’ana pafupipafupi mbeu zoumazo ku matenda a mosungira mbeu.
B) Anyezi – Njira ya Manyowa
Anyenzi ndi odziwika bwino pa nkhani yowonjezeredwa mu ndiwo ku Afirika. Ali ndi mavitamini ochuluka komanso foleti ndipo alinso ndi peputayidi wambiri yemwe amathandiza pogonjetsa matenda akusalimba kwa mafupa.
Anyezi amakonda kubzalidwa mnyengo zozizira za pakati pa 12℃ mpaka 25℃ ndipo amachita bwino kwambiri kozizira kusiyana ndi kotentha. Anyezi kuti akhwime amatenga nthawi yaitali (kuchokera miyezi 4 mpaka 7), kotero “m’munda waung`ono wapakhomo “ndi mbeu zabwino kuzibzala m`miyezi imeneyi, kuphatikizanso anyezi wotsekemera. Bzalani anyezi kuchokera kumapeto a chilimwe mpaka dzinja ndipo kumbukirani kuti amafuna madzi ambiri akayamba kubereka masamba, ndiye “m’madera ogwa mvula nthawi ya chilimwe ngati mvula sikugwa, Onetsetsani kuti muli ndi njira yabwino yakathiriridwe ka madzi.
Kabzalidwe
Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani mizere yokhala iwiri pa mpata wotalikana wa 20cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo. M’munda waung’ono, kulitsani bande lanu kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa.
Kuyala Zingwe m`mabeseni Osaya obzalira
Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo choyang’anizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange beseni losaya. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi.
Kusuntha Bulangete la Mulungu
Sunthani bulangete la Mulungu pa muyeso wa 10cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira, kuti nthaka ikhale poyera.
Kumasula Nthaka
Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene ungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere.
Kukonza Mabeseni Osaya
Chifukwa cha kufupikirana kwa mizere pa mpata wa 20cm, ndi kovuta kukumba kangalande ka mbeu za m`mizere yofupikiranayi. M`malo mwake, konzani mabeseni osaya pokumba nthaka ndikuitulutsa pa muyeso wa 5cm pakati pa zingwe zotalikana 25cm ndipo liikeni kotsika kumunsi.
Kukonza Nthaka ya Mchere
Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse.
Manyowa
Wazani manyowa wokwanira muyeso wa 1cm pansi pa beseni losaya limeneri ndipo apalapaseni moyenera.
Muyezo Wobzalira Mbeu ndi Kalekanitsidwe ka Nthaka
Phimbirani manyowa ndi dothi mpaka pa mlingo wofanana ndi kayalidwe ka nthaka. Izi zidzaonetsetsa kalekanitsidwe kabwino pakati pa mbeu ndi manyowa zomwe ziri zofunikira kwambiri popewa kupselera kwa mbeu.
Kukumba kangalande ndi Kubzala Mbeu
Dindani kangalande 2cm kuya pansi pa beseni lopangidwa ndipo bwerezaninso zimenezi mu mzere wina wotsatira wa 20cm wa m’munsi. Bzalani mbeu za anyenzi pa muyeso wa 2cm kupita pansi ndi muyeso wotalikirana ndi 5cm. mbeu ya anyezi ndi yaing’ono kwambiri, kotero ndizofunikira kwambiri kuti mbeu yabwino ikhudzane ndi nthaka. Phimbirani mbeu powaza dothi pang`onopang`ono kenako tsindirani poyenda pamwamba pa mbali yotambalala ya thabwa. Pamene wamera, patulirani anyezi pa muyeso wa 10cm wa pakati pa zomera ndipo gwiritsani ntchito anyezi opatulidwa mmalo ena.
Musaike bulangete pamwamba pa mabande obzalidwa kufikira mbeu zitamera, ndi pamene mungathe kuika bulangete pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangete liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm m’mipata yoyendamo kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.
Mbande
Ndi bwino kuokera anyenzi ochita kufesedwa kusiyana ndi mbeu. Kwirirani beseni ndipo bwezeretsani bulangete lokhuthala pa muyeso wa 2.5cm pamwamba pake. Gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe ka pansi, izikeni ndodoyi kupyola bulangeti ndi kuizika pa beseni lokonzedwa, pa mulingo woyenera ndi muyeso wa 10cm kutalikana kwa zomera ndi 20cm kutalikana kwa mizere.
Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani dothi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi.
Kukolora
Anyenzi amatenga nthawi yaitali kuti akhwime (miyezi 4 mpaka 7) ndipo akuyenera ku umitsidwa bwino musadamusunge. Choyamba pamene tsamba layamba chikasu pindani masamba, musawakhodzore zomwe zingapangitse kuti aume mwachangu. Mukamudzula, musungeni mu mnthunzi, pouma, malo opita mphepo bwino. Gwiritsani ntchito koyambirira anyezi yense amene waonongeka ndipo mudziyang’ana pafupipafupi mbeu zoumazo ku matenda a mosungira mbeu.