A) Anyezi Otsekemera – Njira ya Kompositi oika pamwamba 

Anyenzi Otsekemera ndi m`modzi mwa mbeu zomwe zikumaonjezeredwa m`minda ya masamba. Ali ndi vitamini C ndi foleti wambiri komannso ali ndi peputayidi wochuluka. 

Anyenzi Otsekemera amabzalidwa nyengo yozizira ya pakati pa 12℃ mpaka 25℃ ndipo athanso kubzalidwa kwa chaka chonse m`madera ozizira kwambiri. Ali ndi ubwino kuposa Anyenzi wina uja chifukwa amakhwima pa milungu 6 mpaka 10, komanso amabzalidwa wochuluka zomwe zimampangitsa kukhala wabwino ku “minda ing`onoing`ono ya zakudya yapakhomo”. 

Kabzalidwe 

Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani tingalande titatu totalikirana 10cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo. M’munda waung’ono, kulitsani bande lanu kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa Tingalande tisanu totalikirana 10cm wina ndi unzake kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa. 

Kuyala Zingwe Zobzalira pa Bande 

Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo choyang’anizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande wothira kompositi wa pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangete la Mulungu 

Sunthani Bulangete la Mulungu m’munsi mwa bande wobzalira pa mpata wa 25cm, onetsetsani kuti silidakwiriridwe munthaka ndi pang’ono pomwe. Ngati mungakwirire bulangete lomwe silidaole, lingathe kupangitsa kuti nthaka ikhale ndi nthawi yopanga naitulojeni osafunikira ndi kuchepetsa zokolora. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere. 

Kukonza Nthaka ya Mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse. 

Kompositi oika Pamwamba 

Anyenzi Otsekemera amadya pang`ono ndiye thirani muyeso wochepa wa 2cm wa kompositi oika pamwamba pa bande wotalika 25cm m’mbali. Sibwino kusakaniza kompositi mu nthaka. Njira imeneyi ya kompositi wa pamwamba ndikutsatira zomwe Ambuye wa chilengedwe chonse adaonetsa kwa ife kuchokera kumayambiliro a nthawi zonse, pamene iye adapanga kuti zomera zizidya kuchokera pamwamba. 

Kupanga Tingalande ndi Kubzala mbande 

Dindani kangalande ka 2cm kuya pansi pa bande lopangidwa pa muyeso wa 25cm kakulidwe ka m’mbari ndipo bwerezaninso zimenezi mu mzere wina wotsatira wa 10cm wa m’munsi kupanga tingalande titatu mmunda waukulu kapena tingalande tisanu pa munda waung’ono wapakhomo. 

Bzalani mbeu za anyenzi wotsekemera pa muyeso wa 2cm kupita pansi ndi muyeso wotalikirana ndi 5cm. Ndizofunikira kwambiri kuti mbeu yabwino ikhudzane ndi kompositi. Kotero phimbirani mbeu powaza kompositi pang`onopang`ono kenako tsindirani kompositi poyenda pamwamba pa mbali yotambalala ya thabwa. 

Musaike bulangete pamwamba pa mabande obzalidwa kufikira mbeu zitamera, ndi pamene mungathe kuika bulangete pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangete liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm m’mipata yoyendamo kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Mbande za Anyenzi Otsekemera 

Anyenzi Otsekemera amachita bwino kwambiri akafesedwa. Bzalani mbeu zitatu pa mbeu zofesedwa ziri zonse ndipo okerani zikafika nsinkhu wotalika wa 10cm. Ndi bulangete liri pamwamba pa kompositi wa pamwamba pomwepo gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe ka pansi, izikeni ndodoyi kupyola bulangeti ndi kuizika pa bande wa kompositi, pa mulingo woyenera wokhala ndi muyeso wa 10cm kutalikana kwa zomera ndi 10cm kutalikana kwa mizere. 

Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala dzanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. 

Kukolora Anyenzi Otsekemera 

Anyenzi Otsekemera amangotenga masabata 6 mpaka 10 kuti akoloredwe mukatha kumupatulira. Pamene masinde ake akula mokwanira chotsani zomera ndipo dulani mizu ndi nsonga pokonzekera kukagulitsa. Anyenzi Otsekemera amakoloredwa pamene mwamufuna, ndipo athanso kuonjezeredwa mu basiketi ya masamba mwa nthawi zoikika zokhazikika. 

B) Anyezi Otsekemera – Njira ya Manyowa 

Anyezi Otsekemera ndi modzi mwa mbeu zomwe zikumaonjezeredwa m`minda ya masamba. Ali ndi vitamini C ndi foleti komanso ali ndi peputayidi wochuluka. 

Anyenzi Otsekemera amabzalidwa nyengo yozizira ya pakati pa 12mpaka 25℃ ndipo anthanso kubzalidwa kwa chaka chonse M`madera ozizira. Ali ndi ubwino kuposa Anyenzi wina uja chifukwa amakhwima, masabata 6 mpaka 10, amabzalidwanso wochuluka zomwe zimampangitsa kukhala wabwino ku “minda ing`onoing`ono ya zakudya zapakhomo” 

Kabzalidwe 

Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani tingalande titatu totalikana 10cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo. M’munda waung’ono, kulitsani beseni lanu losaya kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa tingalande tisanu totalikana 10cm kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa. 

Kuyala Zingwe Zobzalira pa Bande 

Ikani chingwe cha m’mwamba choyezera kuchokera ku chikhomo chamyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande yobzalira. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangete la Mulungu 

Sunthani bulangete la Mulungu pa muyeso wa 10cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira, kuti nthaka ikhale poyera. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere. 

Kukonza Mabeseni Osaya 

Chifukwa cha kufupikirana kwa mizere yotalikirana pa mpata ndi 10cm, ndi kovuta kukumba mapando kwa mbeu za m`mizere yofupikiranayi. M`malo mwake, konzani mabeseni osaya kupita pansi pokumba nthaka pa muyeso wa 5cm pakati pa zingwe zotalikana 25cm ndipo dothi likhale kumunsi. 

Kukonza Nthaka ya Mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse. 

Manyowa 

Wazani manyowa wokwanira muyeso wa 1cm pansi pa beseni losaya limeneri ndipo apalapaseni moyenera. 

Muyezo Wobzalira Mbeu ndi Kalekanitsidwe ka Nthaka 

Phimbirani manyowa ndi dothi mpaka pa mlingo wofanana ndi kayalidwe ka nthaka. Izi zidzaonetsetsa kalekanitsidwe kabwino pakati pa mbeu ndi manyowa zomwe ziri zofunikira kwambiri popewa kupselera kwa mbeu. 

Kukumba Tingalande ndi Kubzala Mbeu 

Dindani ka ngalande 2cm kuya pa beseni lopangidwa ndipo bwerezaninso zimenezi mu mzere wina wotsatira wa 10cm wa m’munsi. Ngati mukubzala pa mmunda waukulu, kotero konzani tingalande tokhala titatu pa mzere umodzi totalikana 10cm. Koma ngati uli munda waung’ono wa pakhomo, kulitsani bande lanu kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa tingalande tisanu totalikana 10cm wina ndi unzake kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa. 

Bzalani mbeu ya anyenzi Otsekemera pa muyeso wa 2cm kupita pansi ndi muyeso wotalikirana ndi 5cm. Mbeu ya anyenzi Otsekemera ndi yaing’ono kwambiri, kotero ndi zofunikira kwambiri kuti mbeu yabwino ikhudzane ndi nthaka. Phimbirani mbeu powaza dothi pang`onopang`ono kufikira pamwamba kenako tsindirani dothi poyenda pamwamba pa mbali yotambalala ya thabwa. 

Musaike bulangete pamwamba pa mabeseni obzalidwa kufikira mbeu zitamera, ndi pamene mungathe kuika bulangete pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangete liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm m’mipata yoyendamo kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Mbande 

Anyezi Otsekemera amachita bwino kwambiri akafesedwa. Bzalani mbeu zitatu pa mbeu zofesedwa ziri zonse ndipo bzalani zikafika nsinkhu wotalika wa 10cm. Phimbirani mbeu ndi beseni pothira dothi lochokera mbari ya kumunsi kwa mulu wa dothi lounjikidwa. Gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe ka pansi, izikeni ndodoyi kupyola bulangeti ndi kuizika pa nthaka pa mulingo woyenera wokhala ndi muyeso wa 10cm kutalikana kwa zomera ndi 10cm kutalikana kwa mizere. 

Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. 

Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. 

Kukolora Anyenzi Otsekemera 

Anyenzi Otsekemera amangotenga masabata 6 mpaka 10 kuti akoloredwe mukatha kumupatulira. Pamene masinde ake akula mokwanira chotsani zomera ndipo dulani mizu ndi nsonga pokonzekera kukagulitsa. Anyenzi Otsekemera amakoloredwa pamene mwamufuna, ndipo athanso kuonjezeredwa mu basiketi ya masamba mwa nthawi zoikika zokhazikika.