A) Letesi- Njira ya Kompositi oika pamwamba 

Letesi ndi mbeu ya saladi wamasamba wodziwika bwino amene ali ndi vitamini A wochuluka. Letesi ali mmitundu yosiyanasiyana ndi maonekedwe osiyanasiyananso ochuluka. 

Letesi ali ndi katenthedwe kabwino kakakulidwe ka pakati pa 5-15 oC. Ngakhale amachita bwino mu katenthedwe kozizirira, amatha kulolera nyengo yotentha kwambiri mpaka pa 30 oC. Bzalani letesi kuchokera nthawi ya kasupe kufikira miyezi ya dzinja. 

Kabzalidwe 

Ngati mukubzala m’munda waukulu, kotero pangani mizere iwiri-iwiri pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mufikire kukhala ndi mpata waukulu oyendamo. Pa munda waung’ono, fumulani kompositi wa pamwamba kukhala 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya kutalikana kwa 20cm pa mzere umodzi kuti mugwiritse bwino ntchito malo anu ochepa 

Kayalidwe ka zingwe pofuna kubzala. 

Ikani chingwe choyezera pamwamba kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri ikani zikhomo zosakhalitsa pa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande la kompositi wa pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu pokankhira m’munsi pa mpata wa 25cm wa bande wobzalira, onetsetsani kuti palibe bulangeti lomwe laola, zikhoza kupangitsa nthaka kukhala wopanda naitulojeni kupangitsa kukolola zochepa. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nkthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kukonza Michere ya Munthaka 

Kuti mukonze michere ya mu nthaka pa bande wa 25cm kukula kwa m’mbali, wazani mogawa dzanja limodzi lodzaza la phulusa la mitengo kapena la mafupa pa mita iriyonse. 

Kompositi oika pamwamba 

Letesi amadya pang’ono choncho ikani mphasa ya 2cm ya kompositi wa pamwamba pa bande wa muyeso wa 25cm kukula m’mbali. Siziri Zoyenera kukwilira kompositi mu nthaka. Upangiri umenewu wa manyowa oika pamwamba ndi kutsatira bwino lomwe zimene Yehova wa chilengedwe chonse wationetsa ife kuyambira pachiyambi cha nthawi zonse, pamene adapanga kuti zomera zidzidya kuchokera pamwamba. 

Bulangeti la Mulungu 

Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm kuti udzu usamere ndi kusunga chinyontho. 

Mbande 

Letesi amabzalidwa bwino kuchokera ku mbande, kupereka changu komanso kuphweka kwa kakulidwe kofanana. Gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi chizindikiro cha kazikidwe ka pansi, izikeni kupyola bulangeti ndi kuizika mu bande wa kompositi pa muyeso wopita pansi woyenera. Kakhirani mkati maenje amenewa pa muyeso wa 20cm pakati pa zomera ndi 20cm pakati pa mizere imene iri mu kayalidwe ka dayamondi. 

Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbande zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbande, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. 

Kukolora 

Letesi ali ndi mitundu ya mbeu yochuluka komanso ndi makulidwe osiyana. Wina amokololedwa monga masamba ang’onoang’ono, ena monga masamba akuluakulu munyengo yonse yolima ndi ena monga mitu kuzulapo yense. 

B) Letesi- Njira ya Manyowa 

Letesi ndi mbeu ya saladi yamasamba yodziwika bwino imene iri ndi vitamini A wochuluka. Letesi amachokera ku zolimidwa zochuluka zokhala ndi mitundu ya mbeu yabwino yochuluka. 

Letesi amakula bwino ndi katenthedwe kabwino ka pakati pa 5-15 oC. Ngakhale amachita bwino mu katenthedwe kozizirira, amatha kulolera nyengo yotentha kwambiri mpaka pa 30 oC. bzalani letesi kuchokera nthawi ya kasupe kufikira miyezi ya dzinja. 

Kabzalidwe 

Ngati mukubzala m’munda waukulu, kotero pangani mizere iwiri-iwiri pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mufikire kukhala ndi mpata waukulu oyendamo. Pa munda waung’ono, kulitsani kompositi oika pamwamba kukhala pa muyeso wa 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya kutalikana kwa 20cm pa mzere umodzi kuti mugwiritse bwino ntchito malo anu ochepa. 

Kuyala Zingwe Pobzala mmabeseni osaya 

Ikani chingwe cha m’mwamba choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zokhalitsa ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange beseni lobzalira la pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu 10cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira kuti nthaka iwonekere. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kupanga Mabeseni Osaya 

Chifukwa chakufupikana kwa mizere ya kayalidwe ka 20cm, ndizovuta kwambiri kukumba ngalande za mbeu zimenezi za mizere yaing’ono. M’malo mwake konzani beseni losaya pokumba 5cm pakati pa zingwe za 25cm ndi kuliika dothi cha kumunsi. 

Kukonza Michere ya Nthaka 

Kuti mukonze michere ya nthaka pa bande wa 25cm kukula kwa m’mbali, wazani mogawa dzanja limodzi lodzaza la phulusa la mitengo kapena la mafupa pa mita iriyonse. 

Kuika Manyowa 

Wazani 1cm ya manyowa pansi penipeni pa beseni losaya ndi kusalaza bwino. Phimbani manyowa ndi nthaka kuti pakhalenso monga m’mene padaliri poyamba pasanakumbidwe beseni. 

Bulangeti la Mulungu 

Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm kuti udzu usamere ndi kusunga chinyontho. 

Mbande 

Letesi amabzalidwa bwino kuchokera ku mbande, kupereka changu komanso kuphweka kwa kakulidwe kofanana. Gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi chizindikiro cha kazikidwe ka pansi, izikeni kupyola bulangeti pa muyeso wa kupita pansi koyenera. Kakhirani mkati maenje amenewa pa muyeso wa 20cm pakati pa zomera ndi 20cm pakati pa mizere imene iri mu kayalidwe ka dayamondi. Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbande zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbande, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo yobzalira ndiwokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani dothi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. 

Kukolora 

Letesi ali ndi mitundu ya mbeu yochuluka komanso ndi makulidwe osiyana. Wina amokololedwa monga masamba ang’onoang’ono, ena monga masamba akuluakulu munyengo yonse yolima ndi ena monga mitu pozulapo yense.