Masikwashi ndi monga maungu, maungu a mtedza, jemusikwashi, mavembe, zukini ndi patepani ndipo zimakhala ndi mavitamini A, C ndi E wambiri komanso amachotsa matenda mnthupi. Bzalani mbeu za masikwashi mu nyengo yozizira mpaka kumayambiliro a chirimwe ndi katenthedwe kapena kaziziridwe kabwino kuchokera 18 mpaka 28℃. Sizimachita bwino nthawi yozizira kwambiri ndipo zikuyenera kubzalidwa nyengo yozizira kwambiri ikadutsa. 

Kabzalidwe 

Masikwashi amabzalidwa mosiyanasiyana koma njira yophweka ndi kukumba mapando motalikirana ndi 120cm pakati pa mbeu ndi 150cm pakati pa mabande 

Kuika chingwe choyezera 

Mangani chingwe choyezera cha ma 60cm kuchokera ku chikhomo cha 75cm choyang`anizana nacho. Onetsetsani kuti chingwe chalimba komanso chawongoka pochinyamutsa ndi kuchiponyanso pansi. 

Kusuntha Bulangetet la Mulungu 

Sunthani Bulangete la Mulungu 30cm motsetseletsa pa chingwe choyezera chachiwiri chilichonse pomwe pali chizindikiro kapena motalikirana 120cm kuti dothi lionekere. 

Kukumba Mapando 

Konzani chokumbira mapando chabwino ndipo kumbani dzenje lokulirapo, 120cm iliyonse mu mzere, pochotsa dothi 20cm kulowa pansi ndi kukula kwake 20cm. Bwerezani izi bande lililonse lotsatira yotalikirana ndi 150cm ndikupanga ndondomeko ya dayamondi 

Kukonza Nthaka ya Mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kuti ikhale ya chonde chokwanira sakanizani masupuni awiri a phulusa/ ufa wa mafupa kapena masupuni atatu ang’ono a laimu ndi dothi la m`mapando. 

Kompositi / Manyowa 

Sakanizani kompositi kapena manyowa ochuluka khasu kudzadza ndi dothi lochokera m`mapando. Mukamagwiritsa ntchito manyowa, khuthulirani m`mapando ndikusiya dzenje la 6cm ndipo kenako ikani dothi lokhalokha lolekanitsa kuti mupewe kupselera kwa mbeu. Mukamagwiritsa ntchito kompositi, khuthulirani m`mapando zomwe mwasakaniza zija ndi kusiya dzenje la 3cm lobzalira chifukwa kompositi samapseleretsa mbeu 

Kubzala Mbeu 

Pa phando lirilonse bzalani mbeu zitatu, mu thilayango motalikirana 10cm ndipo kwilirani ndi dothi lokhalokha la pamulu wotsetseleka uja. Zikamera, siyani mbeu ziwiri zokha pa phando lirilonse. 

Bulangete la Mulungu 

Mbeu zikangokula moyandikira 10cm bwezeretsani bulangete kutsamira mitengo ya mbeu. Onetsetsani kuti bulangete la phimbira bwino ndi 100% ndipo ndi lalikulu mimba 2.5cm kuti liletse kukula kwa udzu wosafunikira ndi kusunga chinyotho. 

Kuteteza Tizilombo 

Chitetezo choyambilira chanu chothana ndi tizilombo komanso matenda ndi kusamalira mbeu kuti zisakhale ndi vuto lirilonse pokhala ndi nthaka yathanzi, chophimbira bwino ndi kuthira bwino kwa manyowa. Njira iliyonse ya chilengedwe yothana ndi tizilombo ikuyenera kukhala chidwi ndi kapewedwe kusiyana ndi kuchiza 

Nthenda yaikulu ya masikwashi ndi powdery mildew. Mvula kapena nyengo ya chinyontho ikatha, poperani kawiri pa mulungu lita imodzi ya mkaka yosakanizidwa ndi malita 9 amadzi omwe athilidwa pamodzi ndi supuni imodzi ya sopo kuti muthane ndi powdery mildew (onani chaputala 5). 

Yenderani mbeu zanu pafupipafupi ndipo ngati mwaona mbeu zogwidwa ndi matenda njira yabwino ndikuchotsa mbeu zimenezo ndikuzitaira kutali kwambiri ndi munda.