6.1.2. Mabiringano – Njira ya manyowa kapena ndowe 

Mabiringano ali ndi mavitamini ndi maminilozi ochepa, 

koma ali ndi anti – oxidanti (zosukunura zosafunikira mnthupi). Ndi amodzinso mwa zipatso zamasamba zazikulu zosavuta kulima ndizosagwidwa kwambiri ndi tizilombo kapena matenda kusiyana ndi tomato. Akuyenera kulimidwa mu dothi lozika, losunga bwino madzi ndi lachonde. 

Mabiringano amakula bwino mu nthawi yozizira kapena chilimwe ndi katenthedwe kapena kazizidwe kabwino ka pakati pa 20 mpaka 27℃ 

Kabzalidwe 

Kuti muzitha kuyenda mosavuta m`munda, alimi a minda ing`onoing`ono akuyenera kubzala mabiringano m`mizere iwiri yotalikirana 75cm ndi 60cm pakati pa 

mbeu, kenako dumphani bande ndi kusiya njira yotalika 

150cm mpaka kufikira bande linalo. 

Alimi aminda ing`onoing`ono angathe kuwabzala potalikirana 60 ndi 75cm kuti agwiritse ntchito bwino malo awo ochepa. 

Bilingano imalemera kwambiri ndipo pachifukwa cha ichi mukulangizidwa kuti mumange timatabwa kapena timitengo tolimbitsira mbeuzo m`malire mwa mabande. 

Kuika chingwe chokumbira mapando cha ma 60cm 

Ikani chingwe chokumbira cha ma 60cm kuchokera ku chikhomo cha 75cm mpaka kulumikiza ndi chikhomo china cha 75cm choyang`aniza nacho. Onetsetsani kuti chingwe chalimba komanso chawongoka pochinyamutsa ndi kuchigwetsanso pansi. 

Kusuntha Bulangete la Mulungu 

Sunthani Bulangete la Mulungu 30cm motsetseretsa munsi pa phando iliyonse, kuti nthaka ionekere. 

Kukamula Nthaka 

Perekani mwayi onse ochita bwino ku ma mabiringano anu pokamulira 75cm iliyonse ya mzere wa m`mabande ndi 30cm kulowa pansi 

Kukumba Mapando 

Mapando otalikirana kumapangitsa kuti manyowa kapena kompositi aikidwe pa phando penipeni kusiyana ndi kompositi oika pamwamba. Kumbani phando 15cm kulowa pansi otalikirana 60cm, unjikani dothi kumunsi kwa chingwe chokumbira mapando, samalani pounjika dothi mwadongosolo kuti mugwiritsenso ntchito, Mapando akuyenera kuti akule mbali 12cm, atalike 15cm ndi 15cm kulowa pansi. Bwerezani izi pa 75cm iliyonse kapena pa munda wa ukulu mizera iwiri ya ma 75cm ndi ma 150cm moyendamo. 

Kukonza Nthaka ya Mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kuti chonde chokwanira chifikire kumbeu thilani supuni imodzi yaikulu phulusa kapena ufa wa mafupa kapena supuni imodzi ya ing’ono ya laimu monngowaza paphando liri lonse pa 60cm. 

Kompositi kapena manyowa 

Ndikoyenera kuthira 500ml ya kompositi pa phando iliyonse, Ngati mulibe kompositi mukuyenera kugwiritsa nchito ndowe zakale, zambiri zokhwima chifukwa ndowe zakumene zimapangitsa kuti masamba kumangokula osabereka zipatso zochuluka.  

Muyezo wobzalira ndi kalekanitsidwe ka nthaka 

Kwilirani manyowa kapena kompositi ndi dothi ya pamulu ili munsi ija kufikila lidzadze phando. Bwezeletsani bulangete lonenepa 2.5cm pamwamba pa mapando. 

Kubzala [Mbande] Mbeu yomera kale 

Dutsitsani ndodo ya dibula kupyola bulangete ndipo lowetsani pakati pa phando iriyonse, mpaka pa muyeso wolowa pansi bwino. Mukuyenela kuonetsetsa kuti mizu ya mbewu isapindike ngati J zomwe zingazapangitse kuti mbewu zisadzamele bwino, onetsetsani kuti dzenje la ndodo ya dibula, ndilokwanila koma osati lilowenso pansi kwambiri, lipangitsa kuti mukhale mipata yodutsira mpweya pansi pa mizu zomwe ziri zosayenera. Kuti musakumane ndi mavuto amenewa, gwirani mbeu ya Bilingano moyenera ndipo lowetsani ndodo ya dibula kapena chala chanu moongoka, kuika dothi pang`onopang`ono mozungulira mizu ya mbeu. Izi zimathandiza kuti mizu ya mbeu isapindike ndipo sipamakhala mipata ya mpweya kuzungulira chigawo cha mizu. 

Kuteteza Tizilombo 

Chitetezo choyambirila chanu pothana ndi tizilombo ndi matenda ndi kusamalira mbeu zanu zisanyetchere komanso nthaka yathanzi, kuphimbira ndi udzu okwanira bwino, komanso chonde chabwino. Njira yachilengedwe yothana ndi tizirombo iliyonse ikuyenera kukhala chidwi popewa osati kuchiza (onani chaputala 5) 

Mbeu zonse za m’banja lofanana, mabiringano, tomato, tsabola ndi mbatata zimagwidwa ndi tizilombo komanso matenda ofanana, ndikoyenera kukhala ndi zaka ziwiri musadabzale mbeu zimenezi mukasinthasintha wanu. 

Yenderani mbeu zanu pafupipafupi ndipo mukaona mbeu zomwe zagwidwa ndi matenda mwachidziwikire njira yabwino ndi kuchotsa mbeu zimenezo ndi kuzitaya kutali ndi munda.