Chimanga chotsekemera / chobiriwira chimakhala ndi mavitamini komanso maminilozi ochepa, komabe ndi chodziwika kwambiri chipatso chachikulu cha masamba chophweka kulima komanso cholimba kwambiri
Chimanga chotsekemera chimakula bwino mu katenthedwe kapena kazizilidwe ka 15 mpaka 25℃ koma kwambiri chimachita bwino kotentha kusiyana ndi kozizira ndi nthawi yabwino yobzalira kuchokera ku zinja mpaka chilimwe.
Kabzalidwe
Bzalani chimanga pa 60cm kutalikirana kwa mapando ndi 75cm kutalikirana kwa mabande. Chimanga chotsekemera ndi mtundu waufupi wa chimanga ndiye chikuyenera kubzalidwa mochuluka kusiyana ndi chimanga chabwinobwino, ndiye timakwanitsa izi posapatulira.
Kumanga chingwe choyezera cha ma 60cm
Mangani chingwe choyezera cha 60cm kuchokera ku chikhomo cha 75cm kukalumikiza pa chikhomo china cha 75cm choyang`anizana nacho. Onetsetsani kuti chingwe chalimba komanso chawongoka pochinyamutsa ndikuchigwetsanso.
Kusuntha Bulangete la Mulungu
Sunthani Bulangete la Mulungu 30cm motsitsa pa phando lirilonse cholinga choti nthaka ionekere
Kumasula Nthaka
Ngati nthaka yanu yagwirana, perekani mwayi wabwino ku chimanga chanu kuti chichite bwino poimasula ndi foloko pa mzere 75cm uliwonse molowa pansi 30cm koma chifukwa cha mapando ozika 15cm aja sikoyenera kutero.
Kukumba Mapando
Kutalikirana bwino kwa mbeu zimapangitsa kuti manyowa ndi kompositi ziponyedwe molondora mu mapando koma osati kompositi oika pamwamba. Kumbani phando mozika 15cm motalikirana 60cm, kankhirani dothi kotsika kumunsi kwa chingwe choyezera chija, samalitsani pounjika dothi kuti mudzaligwiritsenso ntchito. Mapando akuyenera akule 12cm, atalike 15cm ndipo azike 15cm. Bwerezani upangiri umenewu motalikirana kwa bande iliyonse ndi 75cm.
Kukonza Nthaka ya Mchere
Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kuti chonde chidzifikira mbeu mokwanira thilani supuni imodzi ya phulusa/ ufa wa mafupa kapena supuni imodzi ya laimu, pa phando lirilonse.
Kompositi/Manyowa
Ndikoyenera kuthira 500ml ya kompositi, pa phando lirilonse. Ndi bwinonso kugwiritsa ntchito ndowe zatsopano zomwe zimakhala ndi naitulojeni wambiri, ndipo ndiwofunikira kwambiri tikamalima chimanga chotsekemera.
Muyezo Wobzalira Mbeu ndi Kalekanitsidwe ka Nthaka
Tengani dothi pang`ono pa mulu wotsetsereka uja ndipo phimbirani kompositi kapena manyowa zonse ndi dothi lolekanitsa la 3cm. Siyani muyezo womaliza wobzalira wotalika monga chibiliti cha machesi kapena kuzika 5cm.
Kubzala Mbeu
Bzalani mbeu zitatu pa phando lirilonse kumanzere, pakati ndi kumanja kwilirani ndi dothi la pamulu ndipo bwezereretsani bulangete pamwamba pa mapando. Ndikosafunikira kupatulira chimanga choteskemera chifukwa choti ndi mtundu waung`ono wa chimanga ndipo chimachita bwino chikakhala chochuluka kusiyana ndi mbeu zina.
Bulangete la Mulungu
Chimanga chotsekemera chitha kumera bulangete lili pomwepo, kusiyana ndi mbeu zina za masamba zomwe zimafunika mpata wabwino wa 5cm kuti zimere. Onetsetsani kuti bulangete laphimbidwa bwino ndi 100% ndipo lokula mimba 2.5cm kuti liletse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.
Fetereza obereketsa
Ngati chimanga chanu chikuonetsa zizindikiro zili zonse zobwera chikasu kapena kupselera, bailani fetereza wa urea kapena manyowa amadzi.
Boolani dzenje laling`ono lozika 3cm, motalikira muyezo wa dzanja pa phando lirilonse. Kenako thilani supuni imodzi yaing’ono ya urea mu dzenje ndi kukwilira ndi dothi. Mukamathira manyowa osukunula amadzi, thilani pansi pa mbeu 350ml. Bwezerani kathilidweka chimanga chikafika m`maondo ndi chikamapanga ngayaye.
Kukolora
Kolorani chimanga nyenje zomaliza zikatuluka mu makoko zikayamba kuuma cholinga choti chikhale chotsekemera komanso chamadzi