A) Karoti – Njira ya Kompositi oika Pamwamba
Karoti amaonjezera kwambiri thanzi ku chakudya cha m`munda chilichonse chifukwa amakhala ndi beta kalotini ochuluka kwambiri (amakhala ndi vitamini A), mavitamini C, K ndi B6, amachotsa zinthu zoipa mthupi komanso ali ndi maminilozi. Karoti ndi osavuta kulima ndipo angathe kubzalidwa pafupipafupi kwa chaka chonse, amachita bwino pomubzala nyengo yozizira yapakati pa 15℃ mpaka 24℃. Nyengo yotentha kwambiri karoti samakula bwino. Konzani mabedi, makamaka potsatira mbeu yomwe mwabzala yomwe idathiliridwa manyowa a thanzi.
Kabzalidwe
Ngati mukulima munda waukulu, konzani mizere iwiri ya 20cm motalikirana kuti mudzifikika.
M`munda waung`ono wa pakhomo talikitsani bande ndi 45cm ndipo konzani mizere itatu yofanana yotalikirana ndi 20cm kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa.
Kumanga Zingwe M`malo Obzalira
Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zokhalitsa ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande wothira kompositi wa pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi.
Kusuntha Bulangete la Mulungu
Sunthani Bulangete la Mulungu m’munsi mwa bande wobzalira, onetsetsani kuti silidakwiriridwe mu nthaka. Ngati mungakwirire bulangete lomwe silidaole, lingathe kupangitsa kuti nthaka ikhale ndi nthawi yopanga naitulojeni osafunikira ndi kuchepetsa zokolora.
Kumasula Nthaka
Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere.
Kukonza Nthaka ya Mnchere
Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse.
Kompositi oika Pamwamba
Karoti amadya pang`ono ndipo akapasidwa chakudya chochuluka, mitsitsi imasintha maonekedwe ake achilengedwe ndi kugawanika. Kotero ndi kwabwino kwambiri kuti karoti abzalidwe motsatira mbeu zina mu kasinthasintha zomwe zathiridwa kompositi oika pamwamba popanda kufunikira kothiranso kompositi wina.
Komabe m`munda watsopano opanda chonde ingothirani 2cm ya kompositi oika pamwamba pa bande wokula pa muyezo wa 25cm m’mbali. Sikofunikira kusakaniza kompositi m`nthaka.
Kupanga tingalande ndi Kubzala Mbeu
Dindani 1cm ya kangalande kupita pansi pa bande wa 25cm m’makulidwe a m’mbali ndipo bwerezaninso pa mzere wina wa 20cm wa m’munsi mwake. Bzalani mbeu za kaloti pa muyezo wa 1cm kuzika pansi ndi motalikirana ndi 2.5cm kufikira pa mbeu ina, koma akamera patulirani mpaka pa muyezo wa 5cm pakati pa mbeu. Kubzala mbeu ya karoti mozika kwambiri zipangitsa kuti isamere bwino.
Ndizofunikira kwambiri kuti mupeze mbeu yabwino ya karoti ikhudzane ndi kompositi kotero phimbirani mbeu powaza kompositi pang`onopang`ono kenako tsindirani kompositi poyenda pamwamba pa mbali yotambalala ya thabwa.
Bulangete la Mulungu
Musaike bulangete pa mwamba pa bande wa kompositi wa pamwamba kufikira kaloti atamera, ndi pamene bulangete lingaikidwe. Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm m’mipata yoyendamo kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.
B) Karoti – Njira ya manyowa
Karoti amaonjezera kwambiri thanzi ku chakudya cha m`munda chiri chonse chifukwa amakhala ndi beta karotini ochuluka kwambiri (amakhala ndi vitamini A), mavitamini C, K ndi B6, amachotsa zinthu zoipa mthupi komanso ali ndi maminilozi. Karoti ndi osavuta kulima ndipo angathe kubzalidwa pafupipafupi kwa chaka chonse, amachita bwino pomubzala nyengo yozizira ya pakati pa 15℃ mpaka 24℃. Nyengo zotetha kwambiri karoti samakula bwino, konzani mabedi makamaka potsatira mbeu yomwe munabzala yomwe idathiridwa manyowa a thanzi.
Kabzalidwe
Ngati mukubzala pa munda waukulu, ndiye pangani mizere yokhala iwiri pa mpata wotalikana wa 20cm kuti mukhale ndi mpata wokwanira woyendamo.
Pa munda waung’ono wapakhomo, kulitsani beseni lanu kufikira muyeso wa 45cm ndi kubzala pa mizere itatu ya pa mzere umodzi yotalikana 20cm wina ndi unzake kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu ochepa.
Kuyala Zingwe M`mabeseni Osaya
Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo choyang’anizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 25cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kumanga chingwe china pamenepo. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi.
Kusuntha Bulangete la Mulungu
Sunthani bulangeti la Mulungu pa muyeso wa 10cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira, kuti nthaka ikhale poyera.
Kumasula Nthaka
Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere.
Kukonza Mabeseni Osaya
Chifukwa chakufupikana kwa muyeso wa 20cm pa mzere, ndikovuta kukumba tingalande ta mbeu za mizere zazing’ono zimenezi. M’malo mwake konzani beseni losaya kupita pansi pokumba nthaka pa muyeso wa 5cm kupita pansi pa muyeso wa 25cm wa pakati pa zingwe ndi kuchiika mbali ya kumunsi kwa malo otsetsereka.
Kukonza Nthaka ya Mchere
Kuti mukonze nthaka ya mnchere pa bande wokula 25cm muyeso wa m’mbali wazani bwino dzanja limodzi la phulusa pa mita iri yonse.
Manyowa
Karoti amadya pang`ono ndipo akapasidwa chakudya chochuluka, mitsitsi imasintha maonekedwe ake achilengedwe ndi kugawanika, kotero ndi kwabwino kwambiri kuti karoti abzalidwe motsatira mbeu zina mu kasinthasintha zomwe zathiridwa kompositi bwino popanda kufunikira kothiranso kompositi wina. Komabe, m`munda watsopano wopanda nthaka yabwino, wazani manyowa akale kwambiri pang`ono pa muyeso wokhuthala wa 1cm pansi pa mabeseni osaya ndipo salazani pang’ono basi.
Muyezo Wobzalira Mbeu ndi Kalekanitsidwe ka Nthaka
Kwirirani manyowa ndi nthaka kuti ikhalenso yofanana. Izi zipangitsa kusiyana bwino kwa mpata pakati pa manyowa ndi mbeu zomwe ndi zoyenera kupewa kupsa kwa mbeu.
Kukumba tingalande ndi Kubzala Mbeu
Dindani kangalande kokuya 1cm kupita pansi pa beseni ndipo bwerezaninso pa mzere wotsatira wa 20cm kutsika m’munsi. Bzalani mbeu ya kaloti pa muyeso wa 1cm kuya pansi ndi mpata wotalikana wa 2.5cm koma akangomera patulirani motalikirana pa muyeso wa 5cm pakati pa mbande. Kubzala mbeu ya kaloti mozika pansi kwambiri zimapangitsa kuti asamere bwino.
Ndizofunikira kwambiri kuti mbeu yabwino ya kaloti ikhudzane ndi dothi, kotero phimbirani mbeu powaza dothi pang`onopang`ono kenako tsindirani poyenda pamwamba pa mbali yotambalala ya thabwa.
Bulangete la Mulungu
Musaike bulangete pamwamba pa mbeu zobzalidwa m`mabeseni kufikira zitamera, ndi pamene mungaike bulangete. Onetsetsani kuti bulangete liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm m’mipata yoyendamo kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.