A) Sipinachi- Njira ya Kompositi oika pamwamba 

Sipinachi ali ndi muyeso waukulu wochotsa zosafunikira mthupi mwa masamba onse komanso ali ndi muyeso wochuluka wa mavitameni A, B, C ndi K, ndipo ali ndi Aironi wochuluka mwa michere ina yofunikira. Masamba amenewa a mgulu la masamba sali ofunukira kokha ku thanzi labwino, komanso mopatsa chidwi, ndi wosavuta kulima komanso kusamalira. 

Sipinachi angathe kubzalidwa nyengo ya kasupe kufikira ya dzinja, ndi nyengo yotentha ya kabzalidwe ya mlingo woyenera wa 13-20°C, dziwani kuti sachita bwino mu nyengo yotentha yopitirira 27 °C. 

Kabzalidwe – 37.5cm Mizere Itatu 

Muyeso wotsiriza wa katalikidwe ka zomera ndi 20cm pakati pa zomera pa mizere itatu ya 37.5cm pa mzere umodzi. Gawani mzere wa 75cm pakati, kubzala pa 0; 37.5 ndi 75cm, kenako bwerezani ndondomeko ya mizere itatu pa chikhomo china chokhalitsa chotsatira pa mzere wa 75cm. Mpata umenewu wa 75cm ndi njira yoyendamo kuti kukolola masamba kukhale kosavuta. Ngati muli ndi munda waung’ono wa panyumba, gwiritsani ntchito mpata wa 37.5cm munda onse kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu. 

Kayalidwe ka Zingwe Pobzala Bande 

Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kachiwiri zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 10cm kutsika kumunsi kuchokera pa zikhomo zokhalitsa ndi kumanga chingwe china pamenepo kuti mupange bande la manyowa oika pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu pokakhira munsi pa mpata wa 10cm wa bande lobzarira, kuti muonetsetse kuti palibe bulangeti lomwe laola. likhoza kupangitsa nthaka kukhala yopanda naitulojeni kupangitsa kukolola zochepa. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kukonza Michere ya Nthaka 

Kuti mukonze michere ya nthaka ndi kulora kuti zakudya zopezekeratu za zomera zigwire bwino ntchito wazani tebulo supuni imodzi ya phulusa la mtengo kapena la mafupa kapena la layimu, pa muyeso wa 60cm pa mzere wobzarira uliwonse. 

Kompsiti oika pamwamba 

Ikani kompositi pamwamba pa bande la muyeso wa 10cm kutalika kwa m’mbali, 5cm kupita pansi mogawa kupingasa mzere. Ndi zosayenera kukwilira kompositi mu nthaka. Sipinachi amadya chikatikati koma chifukwa cha mfundo yoti akhala ali m’munda kwa miyezi 6-8 ndikoyenera kumudyetsa bwino kuyambira pachiyambi. Upangiri umenewu wa kompsiti oika pamwamba ndi kutsatira bwino lomwe zimene Yehova wa chilengedwe chonse wationetsa ife kuyambira pachiyambi cha nthawi zonse, pamene adapanga kuti zomera zidzidya kuchokera pamwamba. Bwerezani ndondomeko imeneyi pa mzere uliwonse wa 37.5cm koma siyani mpata wa 75cm muyeso wa m’mbali, njira yoyendamo pa mizere iri yonse itatu ya mzere umodzi kuti kukolola kudzakhale kosavuta. 

Kupanga Tingalande ndi Kubzala Mbeu 

Pakati pa bande wa kompositi dindani kupita pansi pang’ono ndi kumapeto kwa khasu kupanga kangalande kobzalira koyenera ndi kofanana ka 2cm kupita pansi ndi pampata wa 10cm, umene ndi wofanana ndi mpata wa dzanja limodzi kupita m’mbali. Kwirirani mbeu powaza kompositi kuphimba ndi kutsendera kompositi. Patulirani mpaka pa muyeso wa mpata wa 20cm pamene zomera zamera, ndipo gwiritsani ntchito zomera zopatuliridwa kukhala ndiwo kapena saladi. Musaike bulangeti pamwamba pa bande kufikira zitamera, pamenepo ndi pamene bulangeti libweretsedwe pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wophimbira wa 100% ndi kukhuthala kwa 2.5cm kuti lilepheretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Kubzala Mbande 

Nthawi zonse ndi bwino kubzala mbande za sipinachi m’munda kusiyana ndi mbeu. Pamene mukubzala mbande, ikani bulangeti lokhuthala pa muyeso wa 2.5cm pamwamba pa kompositi oika pamwamba musanabzale. Gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi chizindikiro cha kazikidwe ka pansi, izikeni kupyola bulangeti ndi kuizika mu bande wa kompositi pa muyeso wa 10cm m’mbali pa muyeso woyenera ndi 20cm pakati pa mzere. Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo yobzalira ndiwokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. 

Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. Mizere itatu imapereka nthunzi wabwino wophimbira komanso kulolera kukolola kosavuta kuchokera ku mbali zonse. 

Kuthira fetereza obereketsa 

Ngati sipinachi waonetsa zizindikiro ziri zonse zachikasu kapena kuwawuka, thirani urea kapena madzi amanyowa osukunula. Pamene mukuthira madzi amanyowa osukunula, thirani muyeso wa 350ml pa tsinde la chomera chiri chonse. Pamene mukuthira urea, boolani una waung’ono wa 3cm kupita pansi, mpata wa m’mbali wa dzala zitatu mbali yakumtunda ya chomera china chirichonse. Thirani supuni imodzi ya ing’ono ya urea pa dzenje lina lirilonse ndipo kwirirani ndi nthaka. Bwerezani kuchita zimenezi nthawi iri yonse imene mungakolole masamba kachiwiri. 

Kukolora 

Pamene mukukolora, thyorani masamba awiri a akulu kwambiri a sipinachi, kulola masamba ena kuti achulukane bwino. Zomera zidzapitirira kupanga masamba ena kwa nthawi yaitali. Pitirizani kuchotsa masamba okhalitsa a mtundu wa chikasu kulimbikitsa kukula kwa masamba atsopano. Tidakhala ndi kukolola kokwanira kasanu ndi katatu m’munda wachitsanzo wa Kulima mu Njira ya Mulungu. 

B) Sipinachi – Njira ya Manyowa/ Kompositi Wochepa 

Sipinachi ali ndi muyeso waukulu wochotsa zosafunikira mthupi mwa masamba onse komanso ali ndi muyeso wochuluka wa mavitameni A, B, C ndi K, ndipo ali ndi Aironi wochuluka mwa michere ina yofunikira. Masamba amenewa a mgulu la masamba sali ofunikira kokha ku thanzi labwino, koma mopatsa chidwi, ndi wosavuta kulima komanso kusamalira. 

Sipinachi angathe kubzalidwa nyengo ya kasupe kufikira ya dzinja, ndi nyengo yotentha ya kabzalidwe ya mlingo woyenera wa 13-20°C, dziwani kuti sachita bwino mu nyengo yotentha yopitirira 27 °C. 

Kabzalidwe – 37.5cm Mizere Itatu 

Muyeso wotsiriza wa katalikidwe ka zomera ndi 20cm pakati pa zomera pa mizere itatu ya 37.5cm pa mzere umodzi. Gawani mzere wa 75cm pakati, kubzala pa 0; 37.5 ndi 75cm, kenako bwerezani ndondomeko ya mizere itatu pa chikhomo china chotsatira chokhalitsa pa mzere wa 75cm. Mpata umenewu wa 75cm ndi njira yoyendamo kuti kukolola masamba kukhale kosavuta. Ngati muli ndi munda waung’ono wa panyumba, gwiritsani ntchito mpata wa 37.5cm munda onse kuti mugwiritse ntchito bwino malo anu. 

Kuika Chingwe 

Ikani chingwe cha pamwamba kapena choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu pang’ono pa mpata wa 20cm kukokera m’munsi kuchokera pa chingwe chobzalira kuti nthaka ikhale poyera. Musasunthe kwambiri pakuti lingathe kukhudza mzere wotsatira wa 37.5cm. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kukumba Ngalande 

Kumbani ngalande ya 10cm kupita pansi, kusunthira nthaka kumunsi kwa chingwe chobzalira, ndi kusamala powunjika mulu wa nthaka yoti igwiritsidwe ntchito nthawi yina. Bwerezani ndondomeko imeneyi kachiwiri pa mzere wa 37.5cm wina uliwonse womwe upangitse kuti Sipinachi wanu apange nthunzi wabwino wophimbira, koma siyani njira yoyendamo pa mpata uli wonse wa mizere itatu ya mzere kuti mudzakolore mosavuta. 

Kukonza Nthaka ya Mnchere 

Kuti mukonze nthaka ya mnchere ndi kulora kuti zakudya zopezekeratu za zomera zigwire bwino ntchito wazani tebulo supuni imodzi ya phulusa la mtengo kapena mafupa kapena la layimu, pa muyeso wa 60cm pa mzere wobzarira uliwonse. 

Manyowa/Kompositi 

Wazani bwino muyeso wa 500ml wa manyowa/Kompositi pa mpata wina uliwonse wa 60cm, kapena wa kakulidwe ka msinkhu wa mapewa, m’ngalande. Ngakhale sipinachi amadya chikatikati amakhala mu nthaka mpaka miyezi yokwanira 6-8 choncho ndi bwino kumudyetsa bwino kuyambira pachiyambi. 

Kuzika kwa Mbeu ndi dothi lolekanitsira 

Tengani nthaka ya pamwamba kuchokera pa mulu ndi kuphimba mbeu pofikira 3cm ya nthaka kukhazikitsa muyeso wotsiriza woyenera wa kabzalidwe wa 2cm kupita pansi ndi kuonetsetsanso kasiyanitsidwe kabwino ka kasanjidwe pakati pa mbeu ndi manyowa. Ngati simusiyanitsa mbeu kuchokera ku manyowa mudzapeza kumera kwa mbeu kosayenera chifukwa cha kupsa kwa mbeu. Izi siziri chomwechi ndi kompositi yemwe waphikidwa bwino. 

Kubzala Mbeu 

Bzalani mbeu ya Sipinachi pa muyeso wa 10cm kutalikana kapena mpata wotalikana m’mbali wa dzanja limodzi, 2cm kupita pansi ndipo kwirirani ndi nthaka yabwino yofewa, kuonetsetsa kuti kangalande kali kogawidwa moyenera kokwera pang’ono mwamba kukhazikitsa kameredwe kabwino. 

Patulirani kufikira kutalikana kwa 20cm pamene zamera, gwiritsani zomera zopatulidwa monga ndiwo komanso saladi. Musaike bulangeti mungalande kufikira pamene mbeu zamera ndi pamene mungaike bulangeti pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangeti liri ndi kuphimbira kwa muyeso wa 100% ndi 2.5cm kukhuthala kuti liretse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Kubzala Mbande 

Kwarirani mbeu zanu zonse mngalande ndi nthaka yochokera pa mulu wam’munsi kufikira pamwamba pa nthaka patafanananso. Bwezeretsani bulangeti la muyeso wokhuthala wa 2.5cm pamwamba pa kangalande kokwiriridwa. Gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe, izikeni kupyola bulangeti ndi kuitsindikiza pakati pa kangalande kokonzedwa ya muyeso wopita pansi woyenera, pa 20cm iriyonse kudutsa mzere. Muyeso wa 10cm m’mbali pa muyeso woyenera ndi 20cm pakati pa mzere. 

Onetsetsani kuti mitsitsi ya mbeu zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbeu, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Pofuna kutsimikiza kuti zimenezi palibe, gwirizitsani mbande pa malo oyenera ndipo tsindirani ndi ndodo yanu ya dibula kapena dzala zanu moimika, tsindirani kompositi pang’onopang’ono kuzungulira mitsitsi ya mbande. Izi zipangitsa kuti mitsitsi isakhote ndi kuonetsetsa kuti palibe mipata ya mpweya pa malo opezeka mitsitsi. 

Mizere itatu imapereka nthunzi wabwino wophimbira komanso kulolera kukolola kosavuta kuchokera ku mbali zonse. 

Fatereza obereketsa 

Ngati sipinachi waonetsa zizindikiro ziri zonse zachikasu kapena kuwawuka, thiranii urea kapena madzi amanyowa osukunula. Pamene mukuthira madzi amanyowa osukunuka, thirani muyeso wa 350ml pa tsinde la chomera chiri chonse. Pamene mukuthira urea, boolani una waung’ono wa 3cm kupita pansi, mpata wa m’mbali wa dzala zitatu mbali yakumtunda ya chomera china chirichonse. Thirani supuni imodzi ya ing’ono ya urea pa dzenje lina lirilonse ndipo kwirirani ndi nthaka. Bwerezani kuchita zimenezi nthawi iri yonse imene mungakolole masamba kachiwiri. 

Kukolora 

Pamene mukukolora, thyorani masamba awiri a akulu kwambiri a sipinachi, kulola masamba ena kuti achulukane bwino. Zomera zidzapitirira kupanga masamba ena kwa nthawi yaitali. Pitirizani kuchotsa masamba okhalitsa a mtundu wa chikasu kulimbikitsa kukula kwa masamba atsopano. Tidakhala ndi kukolola kokwanira maulendo asanu ndi katatu m’munda wachitsanzo wa kulima mu njira ya Mulungu.