Mbatata yotsekemera ndi imodzi mwa mbeu za mizu zopatsa thanzi kwambiri, yokhala ndi chakudya chokhutitsa (kabohayidiletsi) chosakanizidwa bwino komanso vitamini A ochuluka, mwa zina zonse. Mbatata yotsekemera ikuyenera kukhala mbeu yaikulu yodyedwa m` mabanja ku Afirika chifukwa chokhala ndi thanzi lambiri kusiyana ndi mbeu zina za ufa. Ndi yosavuta kubzala, imatolerana ndi kutentha komanso kopanda madzi, imatsekemera kwambiri ndipo imatulusa matani 10 mpaka 40 pa hekitala iri yonse.
Mbatata yotsekemera imabzalidwa m`madera otentha a muyeso wa 15℃ mpaka 33℃ komanso ndi katenthedwe koyenera ka pakati pa 20℃ mpaka 25℃. M`madera ogwa mvula nthawi ya chilimwe a kum`mwera kwa Afirika, bzalani mu sepitembala mpaka mu Novembala, koma chifukwa choti iri ndi nthawi yake yobzalira ya miyezi 4 mpaka 7 ndi bwino kumubzala mofulumira kusiyana ndi mochedwa. M’madera otsika, anyengo yotentherako ndi madera otentha kwambiri Mbatata Yotsekemera itha kubzalidwa pafupipafupi kwa chaka chonse.
Kabzalidwe
Chifukwa cha chilengedwe chake choyangayanga cha Mbatata Yotsekemera, patulani malo okwanira bwino kuti mupewe ziyangoyango kusokoneza mbeu zina zamasamba. Mbatata Yotsekemera siimachita bwino m`malo odzaza madzi kwambiri, ndiye pamene pali vuto limeneli gwiritsani ntchito mabedi okwera okhazikika ngati m’mene zafotokozeredwa mu chaputala 2.4. Peweni kumubzala mu nthaka yokhala ndi dongo lambiri, chifukwa imasunga madzi kwambiri. Ku Uganda, gulu la ku “Double Portion Farm” amabzala Mbatata Yotsekemera m`maekala m’malo osakwera mu nthaka yotaya madzi pa muyeso wabwino kwambiri. Mbeu imabzalidwa kuchokera ku zodulidwa zake motalikirana pa mpata wa 30cm pa mbeu komanso 75cm pa mpata wa pakati pa mizere.
Kuyala Zingwe Za Tingalande
Ikani chingwe cha m’mwamba choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo choyang’anizana nacho cha mbali yina. Onetsetsani kuti zingwe zonse zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuziponya pansi.
Kusuntha Bulangete la Mulungu
Sunthani bulangete la Mulungu pa muyeso wa 30cm kutsika m’munsi mwa beseni lobzalira, kuti nthaka ikhale poyera.
Kumasula Nthaka
Ngati nthaka yanu iri yogwirana perekani mwayi wochita bwino ku Mbatata Yotsekemera pomasula mzere uli wonse wa 75cm pa muyeso wopita pansi wa 30cm koma chifukwa cha mizere yakuya kupita pansi ndi 15cm izi sizingakhale zoyenera.
Tingalande
Kumbani mizere yakuya kupita pansi ndi 15cm mu mzere uli wonse wa 75cm, mosamala posataya dothi kutali kwambiri ndi mbali ya kumunsi.
Kukonza Nthaka ya Mchere
Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kuti ikhale ya chonde chopezeka, thirani supuni imodzi ya phulusa, ufa wa mafupa kapena supuni imodzi ya laimu, pa muyeso wa 60cm iri yonse pa mizere yobzalira.
Manyowa/Kompositi Wochepa
Wazani kompositi kapena manyowa wokwanira muyeso wa 500ml pa mita iri yonse kenako kwirirani ndi 3cm ya dothi kuti mukhale ndi muyezo wobzalira wa 10cm.
Mbeu ya Mbatata Yoduliza-duliza
Mbatata Yotsekemera amabzalidwa kuchokera ku mitengo yake yoduliza-duliza yopanda matenda (vailasi) yomwe yakhala m`munda kwa miyezi itatu. Sungani mitengo yoduliza-duliza yotalika 30cm malo apa nthunzi kufikira masiku atatu kuti mizu iyambe kuphuka musanakabzale.
Kubzala Mbeu ya Mbatata Yoduliza-duliza
Onetsetsani kuti mtengo wa mbeu uli wonse uli ndi malo amene mitsitsi ingathe kuphukapo. Zikani mbeu yoduliza-duliza yotalika 30cm pogwira mbali yakumwamba ku mchira kulowe mu ngalande. Pindani mbali ya m`mwamba ya mtengo m`maonekedwe a chilembo cha L ndipo kwilirani ndi dothi, siyani mbali ya m`mwamba yapanthaka yokwana 10cm. Mukuyenera kuti 10cm ikhale mogonera nthaka, komanso 10cm yokhala moima koma mu nthaka momwemo, ndi 10cm pamwamba pa nthaka. Kwirirani mtengo wina wotsatira ngati momwe mwachitira kumalizira ndi 10cm ya mtengo wa 30cm uli wonse molondora mzere.
Bulangete la Mulungu
Kukwezera dothi sikofunikira kuti mbatata afufume bwino koma bulangete labwino ndilo lofunika. Phimbirani bulangete lokhuthala bwino pakati pa 5cm mpaka 10cm, poika mozungulira mitengo yoduliza-duliza ya mbatata, kuti mulimbikitse kufufuma kapena kukula kwa mbatata yeniyeni kuchitika moyandikana ndi dothi lapansi pa bulangete. Bulangete likakula bwino mumakolora mosavuta mbatata yotsekemera yanu posasokoneza nthaka kwenikweni.
Kukolora
Tsatani mitawi ya mbatata kuti mupeze mbatata yeniyeni pansi ndipo kenako gwiritsani ntchito foloko kuti muchotse pang`onopang`ono mbatata yotsekemera yomwe nthawi zambiri imapezeka pafupi, pansi pa bulangete. Masamba a thanzi amenewa angathe kukoloredwa nthawi iliyonse pamene mwawafuna, akuyenera kuwonjezeredwa pa munda wa pakhomo.