6.1.3 Tsabola onunkhira – Kompositi kapena Manyowa 

Zipatso za tsabola onunkhira ziri m`maonekedwe ndi m`mitundu yosiyanasiyana (obiliwira, orenji, wachikasu ndi ofira) ndipo ali ndi vitamin C wochuluka komanso amachotsa zinthu zosafunika m`nthupi (anti – oxidants). Ndimasamba azipatso zazikulu zosavutirako kulima, zamasamba koma sizichedwa kugwidwa ndi tizilombo komanso matenda ndipo zimafuna nthaka yozika, losunga bwino madzi ndi yachonde.Tsabola amachita bwino munyengo yozizira kapena kumayanbiliro achirimwe ndi katenthedwe kapena kaziziridwe kabwino ka pakati pa 20 mpaka 27℃ . 

Kabzalidwe 

Tsabola amabzalidwa mochulukana mmunda kusiyana ndi mabiringano, Bzalani tsabola motalikirana 45cm pakati pa mbeu ndi 75cm kutalikirana kwa mizere, chimodzimodzi ndi kabitchi. Mbeu ya tsabola ili ndi vuto lokugwaigwa kumapeto a nthawi yokolora, pachifukwa chimenechi mukulangizidwa kumanga timatabwa kapena timitengo toimitsira m`mizere ya m`mabande kuti mbeu zilimbe. 

Kuika chingwe choyezera cha ma 45cm 

Mangani chingwe choyezera cha 45cm kuchokera ku chikhomo cha 75cm mpaka ku chikhomo china cha 75cm chomwe chalumikizana nacho moyang`anizana. 

Sunthani Bulangete la Mulungu 

Sunthani Bulangete la Mulungu motsetseleka 30cm kuchokera pa phando, kuti nthaka ionekere 

Kumasula Nthaka 

Perekani mwayi wochita bwino kwa tsabola wanu pomasulira ndi foloko molowa pansi 30cm ku 75cm iliyonse ya m`mabande. 

Kukumba Mapando 

Kubzala motalikirana kumapangitsa kuti mbeu ziponyedwe molondola m`mapando kusiyana ndi kompositi oika pamwamba. Kumbani phando la 15cm kulowa pansi motalikirana 45cm iliyonse, unjikana dothi kumunsi kwa chingwe, unjikana dothi lanu mosamalitsa kuti mudzaligwiritsenso ntchito. Mapando akuyenera kukhala 12cm m`mbali, 15cm mulitali ndi kuya pansi 15cm. Bwerezani izi ndi 75cm iliyonse yotalikirana kwa mzere. 

Kukonza Nthaka ya Mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kuti ikhale ndi chonde chokwanira thilani supuni imodzi ya phulusa kapena ufa wa mafupa kapena supuni imodzi ya laimu, mu 45cm iliyonse ya mapando. 

Kompositi/Manyowa 

Ndikoyenera kuthira 500ml ya kompositi pa phando iliyonse. Ngati mulibe kompositi, mukuyenera kugwiritsa ntchito ndowe zokhalitsa, zakale chifukwa ndowe zakumene zimapangitsa kuti masamba amere ambiri ndi kuchepetsa kubereka kwa zipatso. 

Muyezo Wobzalira Mbeu ndi kalekanitsidwe ka nthaka 

Kwilirani kompositi kapena manyowa ndi dothi la pamulu lakumunsi lija kufikira phando lonse litavindikilidwa ndi dothi. Ikaninso bulangete lonenepa 2.5cm pa mwamba pa mapando. 

Kubzala Mbeu 

Dutsitsani ndodo ya dibula kudutsa pa bulangete ndipo lowetsani pakati pa phando iliyonse mpaka pa muyezo woyenera wolowa pansi. Onetsetsani kuti mizu ya mbeu isapindike mu maonekedwe a J zomwe zingazabweretse vuto losamera bwino kwa mbeu, ndiye onetsetsani kuti dzenje Lomwe mwaboola ndi ndodo ya dibula yalowa pansi bwino osatinso kwambiri. Ngati dzenje lalowa pansi kwambiri, lidzayambitsa kuti mukhale mipata ya mpweya pansi pa mizu zomwe zili zosafunikira. Kuti musakumane ndi vuto limemeli, gwirani mbeu ya tsabola m`malo mwake, lowetsani ndodo ya dibula kapena dzala zanu mowongoka, ikani dothi pang`onopang`ono mozungulira mizu ya mbeu. Izi zimapangitsa kuti mizu ya mbeu isapindike ndipo pasakhale mipata ya mpweya mozungulira mizu. 

Kuteteza Tizilombo 

Chitetezo chanu choyambirira pofuna kuthana ndi tizilombo komanso matenda ndi kusamalira mbeu pokhala ndi nthaka ya thanzi, kuphimbira ndi udzu okwanira ndi kuthila kompositi kapena manyowa okwanira. Njira iliyonse yothana ndi tizilombo yachilengedwe ikuyenera kukhala chidwi pa nkhani yakapewedwe osati kuchiza (onani chaputala 5) 

Mbeu zonse za m’banja lofanana, Mabiringano, Tomato, Tsabola ndi Mbatata zimagwiridwa ndi tizilombo komanso matenda ofanana ndiye tikuyenera kukhala ndi zaka ziwiri musadabzale pomwepo mbeu zimenezi mundondomeko ya kasinthasintha wanu. 

Yenderani mbeu zanu pafupipafupi ndipo ngati mwaona mbeu zomwe zagwidwa ndi matenda njira yabwino ndikuchotsa mbeu zimenezo ndi kuzitaira kutali ndi munda.