6.2.1 Bonongwe 

A) Bonongwe - Njira ya Kompositi oika pamwamba 

Bonongwe angathe kubzalidwa pa phindu la masamba komanso mbeu, komano mitundu yochuluka imachita bwino ndi kuigwiritsa ntchito kwina. Masamba ali opatsa thanzi ndipo ali ndi mavitameni ochuluka awa, A, B ndi C, ndi mulingo waukulu wa Kasiyamu ndi Aironi kuposa masamba a sipinachi. Bonongwe ndi chomera chopilira ndi choyanjana ndi nthaka ya chonde chochepa, malo otentha ndi nyengo zosowa madzi. Bonongwe amachita bwino mu nyengo ya kasupe mpaka mu nyengo yobzalira ya dzinja pokhala kuti bononongwe amafuna nyengo ya katenthedwe ka 15℃ kuti amere. Bonongwe ali ndi mulingo woyenera wakatenthedwe komerela ka 23-35°C ndipo ndi masamba obiliwira ochita bwino nyengo ya dzinja kusiyana ndi Sipinachi kapena Kale. 

Kabzalidwe – 37.5cm Mizere Itatu 

Zamasamba: Mulingo wotsiriza wa mpata wa bonongwe ndi 30cm pakati pa zomera pa mizere itatu ya mpata wokwanira 37.5cm. Siyanitsani mizere ya mpata wa 75cm pakati ndi mizere itatu kuyambira pa 0; 37.5; 75cm kenako muyambenso pa chikhomo chamuyaya cha muyeso wa 75cm kuti mulole kufikira kukolola kosavuta kwa masamba. Bonongwe wa mbeu amabzalidwa motalikana kwambiri pakuti amafika pa mulingo wa 2m kutalika, komanso 30cm kuchokera pakatikati pa zomera ndi mizere ya 75cm. 

Kuyala zingwe kuti mupange bande lobzalira 

Ikani chingwe chamwamba choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Kenako zikani zikhomo zosakhalitsa pa muyeso wa 10cm kutsika m’munsi kuchokera pa zikhomo zamuyaya ndi kuika chingwe china pamenepo kupanga bande la kompositi la pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zakungika ndipo zawongoka pozinyamutsa ndi kuzigwetsanso pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani bulangeti la Mulungu pokankhira munsi pa muyeso wa mpata wa 10cm chabe pa bande loti mubzalepo, powonetsetsa kuti palibe bulangeti lomwe lakwiriridwa. Ngati mukwirira bulangeti lomwe silidaole, likhoza kupangitsa nthaka kukhala yopanda naitulojeni kupangitsa kukolola zochepa. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kukonza Michere ya Nthaka 

Kuti mukonze michere ya nthaka ndi kulora kupezeka bwino kwa chonde mu nthaka wazani supuni imodzi ya patebulo ya phulusa kapena layimu pa 60cm iri yonse pa nzere wobzalira. 

Kompositi oika Pamwamba 

Bonongwe wamasamba amadya chikatikati choncho ikani 3cm ya kompositi oika pamwamba, pamwamba pa bande lokula 10cm m’mbali. Ndizosayenera kumusakaniza kompositi mu nthaka. Upangiri umenewu wa kompositi oika pamwamba ndiye kutsatira molingana ndi zimene Yehova wa chilengedwe chonse wationetsa kuyambira pa chiyambi cha nthawi, pamene adapanga zomera kuti zidye kuchokera pamwamba. Bwerezani ndondomeko imeneyi kenanso pa 37.5cm iri yonse ya mzere, yomwe ipangitse kuti bonongwe wanu wamasamba aphimbire nthunzi wabwino, koma siyani mpata wa 75cm motalikana wa kupezeka kwa malo woyendamo pa mizere itatu iri yonse kuti kukolora kukhale kosavuta. 

B) Bonongwe – Manyowa/Njira ya Kompositi Wochepa 

Bonongwe angathe kubzalidwa pa phindu la masamba komanso mbeu, komano mitundu yochuluka imachita bwino ndi kuigwiritsa ntchito kwina. Masamba ali opatsa thanzi ndipo ali ndi mavitameni ochuluka awa, A, B ndi C, ndi mulingo waukulu wa Kasiyamu ndi Aironi kuposa masamba a sipinachi. Bonongwe ndi chomera chopilira ndi choyanjana ndi nthaka ya chonde chochepa, malo otentha ndi nyengo zosowa madzi. Bonongwe amachita bwino mu nyengo ya kasupe kupyolera mu nyengo yobzalira ya dzinja molingana ndi kuti bononongwe amafuna nyengo yakatenthedwe ka muyeso wa 15℃ kuti amere. Bonongwe ali ndi mulingo woyenera wakatenthedwe komerela ka 23-35°C ndipo ndi masamba obiliwira ochita bwino nyengo ya dzinja kusiyana ndi Sipinachi kapena Kale. 

Kabzalidwe – 37.5cm Mizere Itatu 

Zamasamba: Mulingo wotsiriza wa mpata wa chomera cha bonongwe ndi 30cm pakati pa zomera pa mizere itatu ya mpata wokwanira 37.5cm. Siyanitsani mizere ya mpata wa 75cm pakati ndi mizere itatu kuyambira pa 0; 37.5; 75cm kenako muyambenso pa chikhomo chamuyaya cha 75cm kuti mulole kufikira kukolola kosavuta kwa masamba. Bonongwe wa mbeu amabzalidwa motalikana kwambiri pakuti amafika pa mulingo wa 2m kutalika, komanso 30cm kuchokera pakatikati pa zomera ndi mizere ya muyeso wa 75cm. 

Kuika chingwe 

Ikani chingwe chakumtunda choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Onetsetsani kuti chingwe chakungika ndipo chawongoka pochinyamutsa ndi kuchiponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani Bulangeti la Mulungu 20cm motsika kumunsi kuchokera pa chingwe chobzalira, kuti nthaka iwonekere. Ndipo musalisunthire kutali pakuti lingakhudze mzere wotsatira woyandikana nawo wa 37.5cm. 

Kumasula Nthaka 

Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndikuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira. 

Kukumba Tingalande 

Kumbani kangalande ka 10cm kuzika pansi, sunthani nthaka chotsika pa chingwe chobzalira, kusamalira kuti muunjike nthaka kuti mudzagwiritse ntchito nthawi yina. Pa bonongwe wa masamba, bwerezani ndondomeko imeneyi pa mpata wa 37.5cm uliwonse zimene zipangitse kuti bonongwe wanu apange thunzi wabwino wophimbira, koma siyani njira yoyendamo kuchoka pa mzere uliwonse wa mizere itatu kuti kukolola kukhale kosavuta. 

Kukonza Michere ya Nthaka 

Kuti mukonze michere ya nthaka ndi kulora kupezeka bwino kwa chonde nthaka, wazani sipuni imodzi ya patebulo ya phulusa kapena layimu pa 60cm iri yonse pa nzere wobzalira. 

Manyowa/Kompositi 

Mogawa chimodzimodzi wazani 500ml za manyowa kapena kompositi pa mita ina iriyonse mu kangalande. 

Muyezo wa kuzika kwa Mbeu ndi dothi lolekanitsira 

Tengani nthaka yofewa bwino ya pamwamba kuchokera pa mulu ndi kukwilira pang’ono manyowa kapena kompositi ndi 3cm ya dothi kukhazikitsa muyezo wotsiriza woyenera wa kabzalidwe wa 1cm kupita pansi ndi kuonetsetsanso kasiyanitsidwe kabwino pakati pa mbeu ndi manyowa. Ngati simusiyanitsa mbeu ndi manyowa mudzapeza kumera kwa mbeu kosayenera chifukwa cha kupsa kwa mbeu. Izi siziri chomwechi ndi kompositi wopangidwa bwino. 

Kubzala 

Bzalani mbeu za bonongwe wamasamba 1cm kupita pansi, pa 15cm motalikana ndi kuphimba ndi nthaka yomasuka komanso yabwino, kuonetsetsa kuti kangalande kakwezedwa pang’ono mmwamba kuti pakhale kameledwe kabwino ka mbeu. Patulirani mpaka pa muyeso wa 30cm pamene kumera kwachitika. 

Bulangeti la Mulungu 

Musaike bulangeti pamwamba pa kangalande kufikira pokhapokha zitamera, ndipamene bulangeti lidzabweretsedwa pansi pa masinde a zomera. Onetsetsani kuti bulangeti liri pa muyeso wa 100% wophimba ndi kukhuthala kwa 2.5cm kuti liletse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho. 

Kukolora 

Pamene mukukolora bonongwe wamasamba obiliwira, chotsani masamba a munsi kwambiri, kupangitsa masamba a mwamba kuchulukana bwino. Ndipo bonongwe apitirira kupanga masamba obiriwira kwa miyezi inanso yochepa.