Zimakhala zopweteka kwa mlimi kudzala mbeu yabwino kuisamalira mpaka kuyandikira nthawi yokolora ndi kumayiona ikuonongedwa ndi tizilombo kapena matenda. Tikuyenera kudziwa kuti tikugwira ntchito mu dziko lachionongeko ndipo tikufunika choyambirira kwenikweni kuti tizipempherera mbeu zathu kuti chitetezo cha Mulungu pa tizilombo ndi matenda chikhalepo, komanso kuchita zinthu m`malamulo ake a Mulungu amene angakhale ndikuthekera kwa chitetezo chake chonse (onani Mifungulo ya m’Baibulo, mu buku la Mphunzitsi).
Nthaka Yamoyo ndi Yathanzi
Kunja kwa pemphero la uzimu komanso ndi mphamvu zomwe Mulungu anatidalitsa nazo, chomwe timayang`ana kwambiri poteteza tizilombo ndi umoyo ndi nthanzi la nthaka. Nthaka ya nthanzi ndi mmene timapezeramo zonse zachilengedwe zofunikira zolengedwa ndi Mulungu zabwino, kukulitsa bwino mbeu ndi tizilombo tamoyo tofunikira. Mbeu zanthanzi zili ndi chitetezo chachilengedwe ku tizilombo ndi matenda, koma zimachitika izi ngati zikudya bwino ndi kuzilima mu nthaka ya thanzi, yamoyo. Kusamvetsetseka kwa moyo wa munthaka ndi kusapumira kugwira ntchito ndipo zomwe taphunzira kuyambirira kunja kwa bukuli la kalimidwe ka masamba zikuyenera kuti tikambirane. Komabe ndikofunika kuti tikhale ndi mitundu ya chilengwe zamoyo zochuluka cholinga choti pakhale ubale okhazikika pakati pa tizilombo tomwe timadya zomera zakufa ndi zamoyo komanso zilombo zomwe zimadya zinzake. Minda ndi nthaka yopanda chonde ili ndi chiopsezo chachikulu polimbkitsa kuchuluka kwa tizilombo ndi matenda omwe amafalikira malo onse chifukwa simukumakhala zilombo zodya zinzake zachilengedwe zomwe zingamateteze kuchuluka kwa chiwerengero. Kupha chilombo chimodzi zingathenso kupha zilombo zofunika zonse, zimene zingayambitse tizilombo ndi matenda ena, ndikofunika kuonetsetsa kuti chiwerengero cha zamoyo chili chimodzimodzi kapena chikatikati. Njira zabwino zosamalira chonde mu nthaka ndi kuithira kompositi wabwino kwambiri ndi bulangete la Mulungu, koma chiwerengero cha zamoyo chapakatikati chomwe chimafunika chimatenga nyengo zochepa kuti muone zotsatira zabwino.
Tikulimbikitsa alimi kuti adziwe mmene chilengedwe chawo chalumikizirana – achule amadya nyongolosi, zouluka, zouluka usiku zangati gulugufe, ndi nkhono; nyongolosi zimakonza kaonekedwe ka nthaka komanso mabowo odutsa mpweya, njuchi ndi agulugufe amathandizira kuti zomera zichulukane, mbalame zimadya ma afidi, ziyangoyango za zouluka zina zimatetezanso tizilombo kwambiri ndi zina zotero. Maganizo oti munda ukuyenera kukhala “opanda kanthu komanso musapezeke tizilombo” ndiofunika asinthidwe kuti tipindule.
Kasinthasintha wa mbeu
Zilombo ndi matenda zimachulukana kwambiri mu nthaka mukamalima mbeu imodzimodzi chaka ndi chaka. Ndi lamulo kuti pa miyezi 6 ina iliyonse kusinthasintha kwa masamba a zipatso, masamba ndi mizu kuchitike, cholinga choti muthane ndi mnzungulire wa matenda amenewa. Kasinthasintha ameneyu adzapindula poteteza kuchulukana kwa zilombo ndi matenda, kwa chaka chonse. Kasinthasintha mkati mwa kasintha kumachepetsanso chiopsezo cha kuchulukana kwa matenda ngakhale mu miyezi 6. Ndizomvetsa chisoni kuti alimi ambiri akulimabe mbeu imodzimodzi ndipo samamvetsetsa chifukwa chimene mbeu zao zikumagwidwa ndi matenda pafupipafupi.
Kuyenderera pafupipafupi
Alimi akuyenera kuyenderera mbeu tsiku ndi tsiku kuti aone zomwe zikuchitika ndi kuononga kwa zilombo ndi matenda, ndi kupeza njira yoyenera yothana nazo.
Kugwira ndi kupha
Njira yodalilika yothana ndi zilombo zikuluzikulu monga mntchembere zandonda, mfinye, bololo, nkhono ndi silagi ndi kuzigwira mkuzipha, ngati uli munda waung`ono. Ndikosavuta kupeza nkhono ndi silangisi usiku. Muthanso kuyika nkhuku m`munda omwe mukufuna kulima kwa masiku ochepa kuti zikadye anamkapande ndi zilombo zina zodula mbeu musanabzale.
Chotsani masamba kapena zomera zogwidwa ndi matenda mwachangu
Ndikoyenera kusenga masamba ena alionse omwe agwidwa ndi matenda kapena kudzula mbeu ya matendayo ndi kuitaya kutali ndi munda, musasiye m`munda momwemo kapena m`malile a munda kapena ndi zopangira kompositi. Izi zimachepetsa kufalikira kwa matenda kapena zilombo kuchulukana ku mbeu yoyandikira ndipo ingateteze mbeu ngati yagwidwa mofulumira.
Misampha ndi zoopysezera
Misampha ya zilombo zowononga imathamangitsira kutali zilombo ku mbeu ndipo itha kukhala kuwala, fungo kapena misampha yeniyeni. Chitsanzo chabwino cha misampha ya zilombo zowononga ndi kuika zikho{makapu} zing`onozing`ono, monga zikho zakale za yogati, mu nthaka ndi kuikamo 2cm ya mowa kuti zithamangitse nkhono ndi masilangi kutali. Mowa umanunkha kwambiri ndipo nkhono imalowa mu chigoba chake italedzera. Zikho ziyenera kutsukidwa tsiku ndi tsiku ndipo mowa ukuyenera kuikidwamo wina pakatha masiku ochepa
Ikani chinthu chonyowa bwino, monga thabwa mozungulira mbeu, zingathandize kuthana ndi nkhono komanso masilagi mosavuta zikamafuna kupeza nthunzi masana.
Zidole zonga munthu ndi mbale za nyimbo zakale kuzimanga pamwamba pa masamba ndi chingwe cha mbedza zingathe kuthandiza pothamangitsa kutali mbalame zoononga
Fungo lothamangitsira zilombo
Njira yabwino yothana ndi zilombo zoononga ndi matenda ndi kupewa, chifukwa zimaletsa kufalikira zisanayambe. Ngati muli ndi mbiri ina ya chilombo chowononga m`munda mwanu mbuyomu, ndiye kuti mukuyenera kupopera mankhwara othamangitsira kutali pa masiku 7 –mpaka14 ali onse kuti zisabweretse vuto mu nyengo imeneyo.
Mbeu monga marigodi, petoniya, udzu onunkhira mandimu, phundabwi, rozimere ndi zina zambiri zoturutsa fungo, zimathandiza pothamangitsa zirombo zoononga m`munda. Zingathe kuonjezeredwa m`munda, m`mipata kapena m`mabande, munda onse
Anyenzi, tsabola ndi adyo akapoperedwa amathandiza kwambiri pothamangitsa tizilombo towononga, palinso mbeu zina zofunikira za mafuta zomwe zimathamangitsa tizirombo monga mkina, malalanje, ikalapitasi, udzu onunkhira mandimu, lavenda, jatulofa, rozimere, thaime ndi kulova. Zafungo zambiri zimenezi zikasakanizidwa bwino zimakhala ndi mphamvu kwambiri.
Kupopera malo okhudzika ndi matenda
Anthu ambiri akaona kuti zilombo zoononga zayamba m`munda, amapopera munda onse, zomwe sinjira yabwino yothanira nazo. Ndikoyenera kupopera malo omwe akhudzidwa ndikuteteza mwachangu, kuti zisafalikire munda onse. Kumbukirani kuti mankhwara amenewa angaphe ndi kuthamangitsa zilombo zonse zothandiza ndi zowononga, ndiye chepetsani kuononga chilengedwe komwe mungathe kuyambitsa pothilira malo okhao omwe akhudzidwa ndi tiziromboto. Poperani ndi nozolo yaing`ono bwino malo okhudzikao chakumadzulo kuti musaononge mbeu zanu. Onetsetsani kuti mankhwara asakanizidwa bwino ndipo sangaononge mwachisawawa powapopera kale malo oyesera. Tili ndi zitsanzo zamankhwara zocheperako mwa zambiri zomwe zilipo.
Kupopera sopo: Kumathandiza kuthana ndi nyenje, ma afidi, chikanga, thilipisi ndi kangaude. Poperani malo omwe zilipo zochuluka kuti methane nazo zonse. Masipuni awiri amadzi asopo pa lita ya madzi imodzi.
Kupopera sopo ndi mafuta: Ndikothandiza kwambiri chifukwa zimaphatikiza pamodzi mphamvu ya sopo, ndi kuvindikira kwa mafuta, komanso kuthamangitsira kutali zilombo zowononga kwa nthawi yaitali. Ma afidi, thilipisi, kangaude, zikanga ndi zouluka zoyera, zimapuma kudzera pakhungu pao, ndiye zikavindikiridwa ndi mafuta zimabanika. Fungo la zomera zoteteza yochokera ku tsabola, anyenzi ndi adyo komanso mafuta ena ofunikira amagwira ntchito modabwitsa pothana mwachangu ndi zilombo m`munda.
Njira yoyamba – Madzi a sopo supuni imodzi, viniga supuni imodzi, mafuta akanola kapena soya 10ml ndi madzi lita imodzi
Njira yachiwiri - Perani tsabola owawa kwambiri okwana 6 (kapena masupuni awiri a ufa wa tsabola), adyo muwiri ndi anyezi mmodzi, onjezerani supuni imodzi ya sopo wa madzi, masupuni awiri a mafuta amasamba ndi kapu imodzi ya madzi otentha vindikirani kwa usiku onse, sefani ndipo onjezerani madzi mpaka akwane lita imodzi.
Njira yachitatu – Mafuta a mkina (ochokera ku nthanga za mtengo wa mkina) ndi mafuta omwe akumagwiritsidwa ntchito kwambiri pothana ndi mfunye, mnchembere zandonda, nyenje, kangaude, milibagi ndi zilombo zouluka zoyera. Kupopera masamba a mbeu kumasokoneza kadyedwe ndi umoyo, ndi kupha tizilombo ngakhale zimachitika mochedwa. Kupopera mafuta a mkina kumathandizanso kuti zitete zisadye komanso kuthandiza pothana ndi matenda ofutwa. Mafuta a mkina saononga tizilombo tofunikira. Supuni yaikulu imodzi ya sopo wamadzi, masupuni awiri akulu a mafuta a mkina ndi lita imodzi ya madzi.
Kupopera mkaka – Kugwiritsa ntchito mkaka osungunula ndi madzi kwapezeka kukhala kothandiza pothana ndi matenda ofutwa chimodzimodzi ngati mankhwala amafagasi ogula. Mkaka umathandizanso pothana ndi kachilombo ka mozaiki, bokisi ndi matenda ena a fangasi ku ma sikwashi, tomato, nkhaka ndi mbeu zina. Sakanizani mkaka okwana 100ml ndi madzi okwana 900ml.
Sopo ndi soda
Soda ndi owawa kwambiri (muli PH okwera) ndipo ndi m`dani wa matenda a fangasi monga kufutwa ndi kuwauka kwa tomato, mbatata ndi sikwashi. Supuni imodzi ya sopo wamadzi, supuni imodzi ya soda ndi madzi lita imodzi. Yesani kaye padera musadathire mbeu zonse.
Bakiteriya wa Thuringenisisi – Njira yopindula ina ndi kugwiritsa ntchito kwa Bakiteliya wa thuringenisisi kapena Bt. Bt ndi bakiteriya wachilengedwe opezeka munthaka amene amatulutsa mankhwara okupha omwe ali oopsa ku zilombo zazing`ono. Bt amapoperedwa ngati mankhwara ophera tizilombo achilengedwe pamasamba ambeu ndipo ndi njira yothandiza kwambiri ya chilengedwe pothana ndi tizilombo toononga tomwe tili tating`ono popanda chiopsezo ku zamoyo zina. Bt kuti agwire mtchito bwino akuyenera kuti zilombo zidye ndipo akangomumeza amaononga khomo la njira lodutsira chakudya ya chilombo ndi kumwalira.
Kuthira mankhwala a ufa
Phulusa limathandiza kwambiri popewa kapuchi ndi mntchembere zandonda zachilendo mu chimanga ndi mu chimanga chotsekemera. Ikani phulusa ku msonga kwa mbeu ina iliyonse chimanga chikafika m’maondo pofuna kuthana ndi mntchembere zandonda. Kugwetsa mapesi mukamaliza kukolora kumathandizanso kwambiri kuti mntchembere zandonda zisaswe mazira. Kugwetsa mapesi mukakolora kumapangitsa kapuchi kuti afe ndi mphavu yakuwala kwa dzuwa ndi kudzionetsara ndi kudyedwa ndi nkhawena komanso nkhuku.
Pofuna kuthana ndi mntchembere zandonda zachilendo m`munda wa chimanga, thilani phulusa milungu iwiri iliyonse kufikira nthawi yopota. Izi zadziwika zitayesedwa kukhala zaphindu ngakhale alimi oyandikana nao adalepheleratu pogwiritsa ntchito njira ya mankhwara
Diatomaceous ndi phulusa la choko lopangidwa kuchokera ku ma atomu awiri amafuta. Akapoperedwa ku zilombo amakakamira pa nkhungu pao ndikuchotsa madzi, kuyambitsa kusowa kwa madzi nthupi ndi kufa kumene. Angatheso kuthilidwa mozungulira pansi pa mtengo wa mbeu ndi kuziteteza ku mntchembere zandonda, nkhono ndi masilagi.
Anthu athanzi amadya zomera zathanzi zochokera ku nthaka ya thanzi lomwe lili nthaka ya moyo!!!! Tikuyenera kuchita chilichonse chomwe tingathe kuchita kuti tilimbikitse umoyo wa nthaka, monga Atate wathu wa kumwamba anationetsera mu chilengedwe chake kuyambira kumayambiliro.
Munda wolimidwa mwa chilengedwe, kusachita bwino mumasamba kukuyenera kuonedwa kuti mupindule zochuluka, koma mwachidziwikire osati zilepheretse kuchita bwino. Yesetsani kupewa kugwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo omwe ali oopsa kwa anthu ndi chilengedwe. Kumbukirani kuti kupha tizilombo tonse, fagai ndi bakiteliya sindiko kuthetsa vuto. M`malo mwake tikuyesera kulimbikitsa malo abwino a zachilengedwe kuti zofunika zonse zipezeke. Onetsetsani kuti mukutsatira ulimi wa bwino munjira ya Mulungu, kusamaalira nthaka ndi za moyo zake, kupereka chilengedwe chabwino ku mbeu za nthanzi, kutsatira njira yochepetsera tizilombo ndi kupewa kugwiritsa ntchito mankhwara ngati kotheka.