Njira yosavuta yosiyanitsira magulu osiyanasiyana a masamba ndi kuzigawa mu zipatso, zamasamba ndi zamizu, zomwe zidzakhale zikusinthidwasinthidwa miyezi isanu ndi umodzi iliyonse mu nthawi yolima ya nyengo yozizira ndi chilimwe. Ndondomeko ndi Upangiri ulionse wa ulimi wa masamba ufotokozedwa paokhapaokha kutengera ngati mukugwiritsa ntchito njira yoika kompositi pamwamba kapena manyowa/ kompositi ochepa. 

6.1. Masamba a zipatso 

6.1.1. Nyemba za zitheba ndi Mnsawawa 

A) Nyemba za zitheba ndi Mnsawawa – Kompositi oika pamwamba 

Kupatula kukhalamo zolimbitsa thupi zambiri, zimene ziri zofunikira kwambiri makamaka madera osauka komwe kumapezeka kabohaidiraiti (zongokhutitsa) wambiri mu chakudya, nyemba za zitheba ndi Mnsawawa zimapereka vitamini A, B, C ndi K, kuteteza ku matenda ndi zina zofunikira mochepa ku moyo wa thanzi. Nyemba za zitheba zimakula bwino mu nyengo ya kumapeto kwa chilimwe ndi katenthedwe kapena kazizilidwe ka 16 mpaka 25℃. Mbali inayi Mnsawawa zimachita bwino mu nyengo yozizira ndi ya mvula ndi katenthedwe kapena kazizilidwe ka 12 mpaka 23℃ 

Kabzalidwe 

Bzalani nyemba za zitheba kapena mnsawawa 10cm kuchokera pa mbeu iliyonse ndi 75cm kuchokera pa mnzera kufika pa wina. 

Kuika chingwe kuti muike kompositi wanu pamwamba 

Ikani chingwe kapena choyezera pamwamba kuchokera pa chikhomo chamuya cha 75cm mpaka ku chikhomo cha 75cm choyang’anizana nacho mbali inayo. Kenako ikani mtengo wongogwirizira pansi kuchokera 10cm ndipo ikani chingwe china kuti muike kompositi wanu pamwamba. Onetsetsani kuti zingwe zonse zalimba ndi kuongoka pozikunga bwino. 

Kusuntha Bulangete 

Sunthani Bulangete la Mulungu 10cm motsika kuchokera chingwe chodzalira, muonetsetse kuti bulangete sinakwilirike mu nthaka. Ngati mungakwilire bulangete yomwe sidaole, ingathe kuyambitsa nthawi yosafunikira ya naitulogeni mu nthaka ndi kuchepetsa zokolora. 

Kutekesa Nthaka 

Lowetsani foloko pansi 30cm ndipo kokani chambuyo pang`ono, kufikira mutaona kuti nthaka yatekeseka kapena kulekana. Chotsani miyala yomwe mungaikhudze ndi foloko, koma musayese kunyamula kapena kutembenuza nthaka, mukuyenera kumangoikanula pang`onopang`ono basi. Bwerezani zimenezi 10cm iliyonse mumzere. 

Kukonza mchere osafunikira wa munthaka 

Kuti mukonze mchere osafunikira wa munthaka ndi kuipangitsa kupezeka ndi zofunikira zabwino za zomera thirani sipuni imodzi ya phulusa kapena ufa wa zinyenyeswa za mafupa kapena sipuni yaing’ono ya laimu, pa 60cm iliyonse mu tingalande. 

Kompositi oika pamwamba 

Ikani kompositi ochuluka 3cm kukwera ndi 10cm mbali pa mzera ulionse wa 75 cm. sizofunika kumusakaniza kompositi mu nthaka. Njira iyi yoika kompositi pa mwamba timatsatira mmene Ambuye a Chilengedwe chonse anationetsa kuchokera pa chiyambi, mmene anapangira kuti mbeu zizidya kuchokera pa mwamba. 

Kangalande ndi kubzyala 

Pakati pa mulu wa kompositi, kankhirani pansi pang’ono ndi khasu lanu kuti mupange malo odikha abwino oti mubzyalepo kuya kwake 3cm kapena mbali mwa chibiliti cha macheso. Kenako ikani nyemba kapena mnsawawa pa kutalikirana kwa 10 cm imene mwachidule ndi kutalikirana kwa dzanja lanu. Kwilirani mbeu ndi kompositi pakhale fulati 

Bulangete la Mulungu 

Musaike bulangete pa mwamba pa mbeu zanu kufikira zitamera kenako mukhoza kukokera bulangete lanu kufikira tsinde la mbeu zanu. Onetsetsani kuti bulangete lakwanira paliponse ndipo lakhuthala 2.5cm lomwe lidzaletsa kumera kwa tchire komanso kusunga chinyontho. 

Kukolora 

Kolorani nyemba zanu za zitheba ndi mnsawawa pafupi pafupi cholinga choti zizipangabe maluwa ndi kuyamba zitheba zatsopano. 

B) Nyemba za zitheba ndi mnsawawa – upangiri wa Manyowa/ kompositi ochepa 

Kupatula kukhala ndi pulotini (zomanga thupi) wambiri, amene ali ofunika kwambiri m`Madera a osauka omwe mu zokudya zao mumapezeka kabohaidiraiti (zongokhutitsa) wochuluka, zitheba ndi mnsawawa mumapezekanso mavitamini A, B, C ndi K, ndi zina zofunikira mochepa m`moyo wa thanzi. Zitheba zimachita bwino nyengo yozizira mpaka kumapeto a chilimwe ndi katenthedwe kapena kaziziridwe kabwino ka 16℃ mpaka 25℃. Mnsawawa zimachita bwino mu nyengo yozizira ndi katenthedwe kapena kaziziridwe kabwino ka 12℃ mpaka 23℃. 

Bzalani zitheba kapena mnsawawa motalikilana 10cm ndi 75cm mizere. 

Kumanga chingwe 

Mangani chingwe kapena chingwe choyezera kuchokera pachikhomo cha 75cm ndi kuchilumikizitsa ku 75cm ya chikhomo cha mbali yoyang`anizana nayo. Onetsetsani kuti chingwe chalimba ndipo chawongoka pochinyamula ndi kuchigwetsanso pansi. 

Chosani Bulangete la Mulungu 

Sunthani Bulangete la Mulungu 20cm kupita munsi kuchokera ku chingwe chobzala, kuti musaikwilire. 

Kumasula nthaka 

Lowetsani foloko 30cm pansi ndipo ichotseni pang`onopang`ono, pokhapokha muone kuti nthaka yalekana komanso yakanuka. Chotsani miyala ndi zigulumwa zilizonse mungazikhudze ndi foloko, koma musayesere kunyamula kapena kutembenuza nthaka, mukuyenera kungoikanula mwapang`onopang`ono. Bwerezani zimenezi 10cm iliyonso ya mzere. 

Kukumba Tingalande 

Kumbani tingalande tozika 10 cm, dothi likhale kumunsi kwa chingwe chodzalira, samalani dothi lomwe mwakumba kuti muligwilitsenso ntchito. Kumbaninso ka ngalande kena pa mpata wa 75cm. 

Kukonza nthaka ya mchere 

Kuti mukonze nthaka ya mchere ndi kukhala ndi chonde chokwanira thirani supuni imodzi yaikulu ya phulusa kapena ufa wa mafupa kapena supuni imodzi yaing’ono ya laimu mongowaza pa 60cm mukangalande. 

Manyowa kapena kompositi 

Wazani 500ml (kapu ya abambo) ya manyowa kapena kompositi pa mita iliyonse mukangalande. Nyemba sizimadya kwambiri ndipo izi zikuyenera kukwanira ngakhale nthaka ilibe chonde chokwanira. 

Dothi lolekanitsa ndi mulingo oti mubzale mbeu 

Tengani dothi lofewa bwino la pamene mwakumba kangalande kanu ndi kukwilira pang’ono manyowa kapena kompositi 3cm, musiye mpata wina wa 3cm kuti mubzaleko mbeu yanu. 

Ngati simulekanitsa manyowa ndi mbeu yanu, kumera kwa mbeu kumakhala kovuta chifukwa mbeu zina zimapsya. Izi sizimachitika ndi kompositi wopangidwa bwino. 

Kubzala 

Bzalani mbeu 3cm kulowa pansi ndi 10cm kutalikirana ndipo kwilirani bwino ndi dothi lofewa lopanda zigulumwa, timayamikira kuti pakwere pang’ono kuti mbeu yanu imere bwino. 

Bulangete la Mulungu 

Mbeu zikamera kokerani bulangete mpaka pa tsinde la mbeu. Onetsetsani kuti bulangete laphimbira bwino paliponse ndi 100% ndi 2.5cm kunenepa kwake kuti udzu osafunikira usamere komanso kusunga chinyezi. 

Kukolora 

Kolorani zitheba ndi mnsawawa zanu pafupipafupi cholinga choti maluwa amerenso ndi kupanga mbeu zina