A) Kale /Repu/tchainizi – Njira ya kompositi oika pamwamba
Mbeu imeneyi ya gulu la zamasamba ndi yodziwika bwino ku Afilika ndipo kusiyana kukupezeka kuchokera ku kale wochuluka wa makolo ndi wa Sukuma wiki ku Kenya. Zonse zachokera ku gulu la olerasiya Burasika ngakhale zimafanana ndi kabitchi, ndizosavuta kulima. Ndizofanana ndi Sipinachi pakuti zimapanga masamba omwe angakololedwe kwa nthawi yaitali. Mbeu ya Repu imapitilira kukula motalika. Masamba amakhala ndi zakudya zochuluka monga vitameni C chimodzimodzinso vitamin K ndi zochotsa zoipa zamthupi.
Kale ali ndi mulingo woyenera wa katenthedwe kobzalira kuchokera 7-24°C ndipo ayenera kubzalidwa mu nyengo ya kasupe komanso m’dzinja, pakuti sakwanitsa kuchita bwino mu nyengo yotentha kwambiri pamene adakali pa mulingo wobereka mbeu.
Kabzalidwe – 37.5cm Mizere Itatu
Mulingo wotsiriza wa mpata wa mbeu ndi 30cm pakati pa mbeu pa mizere itatu ya mpata wokwanira 37.5cm. Siyanitsani mzere wa mpata wa 75cm pakati ndi mizere itatu kuyambira pa 0; 37.5; 75cm kenako muyambenso pa chikhomo chamuyaya cha 75cm kuti mulole kufikira kukolola kosavuta kwa masamba. Ngati muli ndi munda waung’ono wa panyumba ndiye gwiritsani ntchito mpata wa 37.5cm m’munda wanu wonse kuti mulore kagwiritsidwe ntchito kabwino ka malo anu.
Zingwe Zoyala Pobzala Bande
Ikani chingwe kokwera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Chotsatira ikani zikhomo zoyembekezera 10cm munsi mwa zikhomo zamuyaya ndipo muike chigwe china kuti mukhazikitse bandi ya kompositi. Onetsetsani kuti chingwe chakungika ndipo chawongoka pochinyamutsa ndi kuchiponya pansi.
Kusuntha Bulangeti la Mulungu
Sunthani bulangeti la Mulungu pokankhira m’munsi pa mpata wa 10cm chabe, powonetsetsa kuti palibe bulangeti lomwe lakwiriridwa. Ngati mukwirira bulangeti lomwe silidaole, likhoza kupangitsa nthaka kukhala yopanda naitulojeni kwa kanthawi kena kupangitsa zokolola kuchepa.
Kumasula Nthaka
Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nkthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira.
Kukonza Michere ya munthaka
Kuti mukonze michere ya munthaka ndi kulora kupezeka bwino kwa chonde mu nthaka wazani supuni imodzi ya patebulo ya phulusa la mitengo kapena phulusa la mafupa kapenanso layimu pa 60cm iri yonse pa mzere wobzalira.
Kompositi oika Pamwamba
Ikani kompositi pamwamba muyeso wa 10cm kukula kwa m’mbali, 5cm kupita pansi mofanana kupingasa mzere. Ndizosafunikira kusakaniza kapena kukwilira kompositi mu nthaka. Bwerezani ndondomeko imeneyi kachiwiri pa mzere wa 37.5cm wina uliwonse womwe upangitse kuti Kale wanu apange nthunzi wabwino, koma kumbukirani kusiya njira yoyendamo pa mpata uli wonse wa mizere itatu ya mzere kuti mudzakolore masamba mosavuta.
Kale amadya chikatikati, koma amakhala mu nthaka mpaka miyezi isanu ndi umodzi (6) choncho ndi zofunikira kumudyetsa bwino kuchokera pachiyambi. Upangiri umenewu wa kompositi oika pamwamba ndi kutsatira bwino lomwe zimene Yehova wa chilengedwe chonse wationetsera ife kuyambira pachiyambi cha nthawi zonse, pamene adapanga kuti zomera zizidya kuchokera pamwamba.
Kupanga tingalande ndi Kubzala Mbeu
Pakati pa bandi wa kompositi dindani kupita pansi pang’ono ndi kumapeto kwa khasu kupanga ngalande yobzalira yoyenera ndi yofanana ya 2cm kupita pansi. Bzalani mbeu ya Kale 2cm kupitaa pansi ndi 15cm kutalikana. Kwirirani powalawaza kompositi ndi kukwirira mwapang’onopang’ono podzazikira kompositi. Patulirani mpaka pa muyeso wa 30cm kutalikana pamene zamera.
Musaike bulangeti pamwamba pa bandi kufikira pamene kumera kwachitika, kenako bulangeti lingathe kuikidwa patsinde la zomera. Onetsetsani kuti bulangete liri ndi kuphimbira kwa muyeso wa 100% ndi 2.5cm kukhuthala kuti liletse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.
Kubzala Mbande
Nthawi zonse ndi zabwino kuokera mbande za Kale m’munda kusiyana ndi kubzala mbeu. Ikani bulangeti pamwamba pa kompositi wa pamwamba musanaokere, kenako gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe, izikeni kupyola bulangeti ndi kuitsindikiza pakati pa bande wa kompositi wokula 10cm m’mbali, kufikira muyeso woyenera wa kupita pansi wa katalikidwe ka 30cm. Bzalani mzere wachiwiri kapena wa pakati wa mbande mukayalidwe ka dayamondi kuti mugwiritse ntchito bwino malo.
Mukuyenera kuonetsetsa kuti mitsitsi ya mbande zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbande, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo yobzalira ndiwokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Potsimikizira kuti izi palibe, gwirizitsani mbande pa malo ndi kutsindira ndi ndodo yabzalira kapena dzala zanu moimika, mukutsindira nthaka pang’onopan’gono mozungulira mitsitsi ya mbeu. Izi zimatsimikiza kuti mitsitsi ya mbeu siyidapindike ndi kutinso mulibe mipata ya mpweya kuzungulira pamalo a mitsitsi.
Kukolora
Pamene mukukolora, chotsani masamba awiri a munsi kwambiri, kupangitsa masamba a mkatikati kuchulukana bwino. Zomera zidzapitilira kupanga masamba kwa nthawi yaitali. Chotsaninso masamba ena aliwonse amatenda kuti mulimbikitse kukula kwa masamba ena atsopano ndi thanzi la chomera. Tidali ndi kholola maulendo okwanira 6-8 kuchokera ku mbeu zathu za Kale pa miyezi isanu ndi umodzi (6) ya kasinthasintha pa munda wachitsanzo wa Kulima mu Njira ya Mulungu
B) Kale/Repu/ tchainizi – Manyowa/Njira ya Kompositi Wochepa
Mbeu imeneyi ya m’gulu la zamasamba ndi yodziwika bwino ku Afilika ndipo kusiyana kukupezeka kuchokera ku kale wochuluka wa makolo ndi wa Sukuma wiki ku Kenya. Zonse zachokera ku gulu la Olerasiya Burasika ngakhale zimafanana ndi kabitchi, ndi zosavuta kulima. Ndizofanana ndi Sipinachi pakuti zimapanga masamba omwe angakololedwe kwa nthawi yaitali. Pamene Repu chomera chimapitilira kukula motalika. Masamba amakhala ndi zakudya zochuluka monga vitameni C komanso vitamin K ndi kuchotsa zosafunik mthupi.
Kale ali ndi mulingo woyenera wa katenthedwe kobzalira kuchokera 7-24°C ndipo ayenera kubzalidwa mu nyengo ya kasupe komanso m’dzinja, pakuti sakwanitsa kuchita bwino mu nyengo yotentha kwambiri pamene adakali pa mulingo wa mbande.
Kabzalidwe – 37.5cm Mizere Itatu
Mulingo wotsiriza wa mpata wa chomera ndi 30cm pakati pa zomera pa mizere itatu ya mpata wokwanira 37.5cm. Gawani mzere wa mpata wa 75cm pakati ndi mizere itatu kuyambira pa 0; 37.5; 75cm kenako muyambenso pa chikhomo chamuyaya cha 75cm kuti kukolola kwa masamba kukhale kosavuta. Ngati muli ndi munda waung’ono wa panyumba ndiye gwiritsani ntchito mpata wa 37.5cm m’munda wanu wonse kuti mulore kagwiritsidwe ntchito kabwino ka malo anu.
Kuika Chingwe
Ikani chingwe choyezera kumtunda kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Onetsetsani kuti chingwe chakungika ndipo chawongoka pochinyamutsa ndi kuchiponya pansi.
Kusuntha Bulangeti la Mulungu
Sunthani bulangeti la Mulungu pang’ono pa mpata wa 20cm kukokera m’munsi kuchokera pa chingwe chobzalira kuti nthaka ikhale poyera. Musasunthe kwambiri pakuti lingathe kukhudza mzere wotsatira wa 37.5cm.
Kumasula Nthaka
Zikani chotakasira nthaka 30cm kupita pansi ndi kuchikokera kumbuyo pang’ono kufikira mutaona kuti nthaka yamasuka kapena kulekana. Chotsani miyala imene mungaimve ndi chotakasira nthaka chanu koma musatengeke kuti mutembenuze nthaka, mukungoyenera kuimasula basi. Pitirizani kuchita zimenezi pa utali wokwanira 10cm mu nzere wobzalira.
Kukumba Tingalande
Kumbani kangalande ka 10cm kupita pansi, kusunthira nthaka kumunsi kwa chingwe chobzalira, ndi kusamala powunjika mulu wa nthaka yoti igwiritsidwe ntchito nthawi yina. Bwerezani ndondomeko imeneyi kachiwiri pa mzere wa 37.5cm wina uliwonse womwe upangitse kuti Kale wanu apange nthunzi wabwino, koma siyani njira yoyendamo pa mpata uli wonse wa mizere itatu ya mzere kuti mudzakolore mosavuta.
Kukonza Michere ya munthaka
Kuti mukonze michere ya munthaka ndi kulora kupezeka bwino kwa chonde mu nthaka wazani supuni imodzi ya patebulo ya phulusa la mitengo kapena phulusa la mafupa kapenanso layimu pa 60cm iri yonse pa mzere wobzalira.
Manyowa/Kompositi
Mogawa chimodzimodzi wazani 500ml ya manyowa kapena kompositi pa 60cm iri yonse ya katalikidwe kofanana ndi mapewa mu ngalande. Ngakhale Kale amadya chikatikati koma amakhala munthaka kwa pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi (6) choncho ndi kwabwino kudzidyetsa bwino kuyambira pachiyambi.
Muyezo wa kuzika kwa Mbeu ndi dothi lolekanitsira
Tengani nthaka ya pamwamba kuchokera pa mulu ndi kuphimba mbeu pofikira 3cm ya nthaka kukhazikitsa muyeso wotsiriza woyenera wa kabzalidwe wa 2cm kupita pansi ndi kuonetsetsanso kasiyanitsidwe kabwino ka kasanjidwe pakati pa mbeu ndi manyowa. Ngati simusiyanitsa mbeu kuchokera ku manyowa mudzapeza kumera kwa mbeu kosayenera chifukwa cha kupsa kwa mbeu. Izi siziri chomwechi ndi kompositi wa muyeso wapamwamba.
Kubzala Mbeu
Bzalani mbeu ya Kale pa muyeso wa 15cm kutalikana kapena mpata wotalikana m’mbali wa dzanja, 2cm kupita pansi ndipo kwirirani ndi nthaka yabwino yolekana, kuonetsetsa kumela kwabwino kofanana. Patulirani mpaka muyeso wa 30cm kutalikana pamene zamera.
Musaike bulangeti pamwamba pa bande kufikira pamene kumera kwachitika, kenako bulangeti lingathe kuikidwa patsinde la zomera. Onetsetsani kuti bulangeti liri ndi kuphimbira kwa muyeso wa 100% ndi 2.5cm kukhuthala kuti liletse kumera kwa udzu ndi kusunga chinyontho.
Kubzala Mbande
Nthawi zonse ndi zabwino kubzala mbande za Kale m’munda kusiyana ndi mbeu. Kwirirani mbande zanu zonse ndi nthaka kuchokera pa mulu wamunsi kufikira pamwamba pa nthaka patafanananso. Ikani bulangeti lokhuthala 2.5cm pamwamba pa ngalande yokonzedwa, kenako gwiritsani ntchito ndodo ya dibula yokhala ndi muyeso wa kazikidwe, izikeni kupyola bulangeti ndi kuitsindikiza pakati pa ngalande yokonzedwa ya muyeso wopita pansi woyenera, pa 30cm iriyonse. Bzalani mzere wachiwiri kapena wa pakati wa mbande mukayalidwe ka dayamondi kuti mugwiritse ntchito bwino malo.
Mukuyenera kuonetsetsa kuti mitsitsi ya mbande zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbande, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Potsimikizira kuti izi palibe, gwirizitsani mbande ya pa malo ndi kutsindira ndi ndodo yabzalira kapena dzala zanu moimika, mukutsindira nthaka pang’onopan’gono mozungulira mitsitsi ya mbande. Izi zimatsimikiza kuti mitsitsi ya mbande siyidapindike ndi kutinso mulibe mipata ya mpweya kuzungulira pa malo a mitsitsi.
Kukolora
Pamene mukukolora, chotsani masamba awiri a munsi kwambiri, kupangitsa masamba a mkatikati kuchulukana bwino. Zomera zidzapitilira kupanga masamba kwa nthawi yaitali. Chotsaninso masamba ena aliwonse amatenda kuti mulimbikitse kukula kwa masamba ena atsopano ndi thanzi la chomera. Tidali ndi kholola lokwanira maulendo 6-8 kuchokera ku mbeu zathu za Kale pa miyezi isanu ndi umodzi (6) ya kasinthasintha pa munda wachitsanzo wa Kulima mu Njira ya Mulungu.