6.2.2 Kabitchi, Kolifulawa ndi Bulokoli – Njira ya Kompositi/Manyowa 

Gulu la Burasika ndi lodziwika bwino kwambiri la masamba a mgulu la masamba ndipo onse ali ndi mavitameni C ndi K ochuluka. Kabitchi ali wopita patali mu gulu la masamba odziwika bwino pa dziko lonse lapansi ndi phindu lazakudya lakawiri kusiyana ndi Bulokoli ndi Kolifulawa. Komabe ma Burasika onse amafuna upangiri wabwino, nthaka ya chonde, zothira mmapando zochuluka ndi kutetezedwa kwabwino kwa tizirombo ndipo mbeu izi ziyenera kupewedwa kufikira luso labwino litapezeka ku mbeu zina. 

Zimachita bwino ndi nyengo yozizira komanso yachinyezi ndi mulingo woyenera wa katenthedwe kobzalira wa 15-24 °C, koma ndi malire a 0-30°C kuonetsa kukonda kwawo nyengo yozizira kusiyana ndi nyengo yotentha yobzalira. Mitundu ina ya mbeuzi zingathe kupilira ku chisanu. 

Kabzalidwe 

Ndizoyenera kukhala ndi kakulidwe kachikatikati, kusiyana ndi mitu ya kabitchi yaikulu yokhala ndi muyeso wa 45cm pakati pa mbeu ndi 75cm pakati pa mizere. Ngati mukonda mitu ikuluikulu ya kabitchi ikani mpata wa mbeu zanu wa 60cm ndi 75cm m’malo mwake. 

Kuika Chingwe Choyezera 

Ikani chingwe cha ma 45cm choyezera kuchokera ku chikhomo chamuyaya chimodzi cha 75cm kufikira ku chikhomo cholumikizana nacho cha mbali yina. Onetsetsani kuti chingwe chakungika ndipo chawongoka pochinyamutsa ndi kuchiponya pansi. 

Kusuntha Bulangeti la Mulungu 

Sunthani Bulangeti la Mulungu pa mpata wa 30cm motsikira kumunsi kuchokera pa phando lina lirilonse, kuti nthaka iwonekere. 

Kumasula Nthaka 

Perekani mwayi wabwino ku kabitchi wanu kuti achite bwino pomasula mzere uliwonse wa 75cm kufikira 30cm kupita pansi. 

Kukumba Mapando 

Mipata yaitali ndi yabwino chifukwa zoika mmapando zimaikidwa mwachindunji m’mapando kusiyana ndi zoikidwa pamwamba. Kumbani phando 15cm kupita pansi pa mpata uliwonse wa 45cm wa katalikidwe, kukokera nthaka kumunsi kwa chingwe chanu choyezera, kusamalira kuwunjika bwino kwa nthaka kuti igwiritsidwe ntchito nthawi ina. Phando likhale 12cm m’mbali, 15cm mulitali ndi 15cm kupita pansi. Bwerezani mapandowa pa mzere uliwonse wa 75cm. 

Kukonza Michere ya munthaka 

Kuti mukonze nthaka ya mnchere ndi kulora kupezeka kwa chonde bwino lomwe nthaka wazani supuni imodzi ya patebulo ya phulusa kapena layimu pa phando lina lirilonse. 

Manyowa/Kompositi 

Ndi zabwino kwambiri kuika 500ml ya Kompositi komabe mungathenso kuika manyowa pa phando lina lirilonse. Tengani nthaka kuchokera m’munsi pa mulu wanu wa nthaka ndi kuphimba mbeu zonse kufikira nthaka ya pamwamba italingananso. Bwezeretsani bulangeti lokhuthala 2.5cm pamwamba pa phando lobzalira. 

Kubzala Mbande 

Pamene mbande zafika pa mlingo wa 10-12cm kutalika zikhala kuti ndi zokonzeka kuti zingathe kuwokeredwa. Zikani ndodo ya dibula kupyola bulangeti kupita pakatikati pa phando lina lirilonse kufikira mlingo wozika woyenera. Mukuyenera kuonetsetsa kuti mitsitsi ya mbande zanu siyikukhota monga mwa maonekedwe a chilembo cha J zomwe zingakhudze kakulidwe ka mbande, choncho tsimikizani kuti mlingo wozika wa una wa dzenje la ndodo ya dibula ndi wokwanira, komanso osati wokuya kwambirinso. Ngati dzenje liri lakuya kwambiri lipangitsa kuti pakhale mpata wa mpweya pansi pa mitsitsi zomwe sizirinso zofunika. Potsimikizira kuti izi palibe, gwirizitsani mbande ya tomato pa malo ndi kutsindira ndi ndodo ya dibula kapena dzala zanu moimika, mukutsindira nthaka pang’onopan’gono mozungulira mitsitsi ya mbande. Izi zimatsimikiza kuti mitsitsi ya mbeu siyidapindike ndi kutinso mulibe mipata ya mpweya kuzungulira pamalo a mitsitsi. 

Fetereza obereketsa 

Izi ndi zakudya zofunikira kwambiri za zomera choncho ngati zomera zionetsa zizindikiro zina zirizonse za chikasu, thirani urea kapena manyowa osukunula amadzi. Pamene mukuthira manyowa osukunula amadzi, thirani 350ml pa tsinde liri lonse la zomera. Ikani urea, bayani kadzenje kakang’ono ka 3cm kupita pansi, kukula kwa m’mbali 3cm, mbali yokwera ya mbeu iri yonse. Ikani tiyi sipuni ya Urea mu dzenje liri lonse ndipo kwilirani ndi dothi. Bwerezani kuthira sabata ya chiwiri iri yonse ngati kuli koyenera mpaka kufikira patatha masabata okwanira asanu ndi limodzi. 

Kuteteza Tizilombo 

Kabitchi, Kolifulawa ndi Bulokoli amatengeka ndi tizilombo tochuluka komanso matenda komano chitetezo chanu choyambirira ndiye kupanga kuti mbeu zanu zikhale zopanda nkhawa iri yonse pokhala ndi nthaka yabwino, bulangete lokhuthala bwino ndi kaperekedwe kabwino ka zakudya za nthaka. Upangiri wina uliwonse wa chilengedwe wa tizilombo umakhazikika pa kupewa osati kuchiza. Ndizofunika kukhala ndi miyezi khumi ndi iwiri (12) yopuma mu dongosolo la kasinthasintha wanu ndi mbeu zimenezi. Yang’anirani mbeu zanu pafupipafupi ndipo ngati mwazindikira mbeu zogwidwa ndi matenda, nthawi zambiri njira yabwino ndi yongochotsa zomera zimenezi ndi kuzitaya kutali kwambiri ndi munda wanu. 

Kukolora 

Khalani oyang’anitsitsa mukayandikira kukolora pofuna kuwonetsetsa kuti mbeu zisaumirire, pakuti zikatero kabitchi amasweka pamene Kolifulawa ndi Bulokoli amasanduka maluwa.